Ekisodo
20 Kenako Mulungu analankhula mawu awa:+
2 “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+ 3 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+
4 Musadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi.+ 5 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine. 6 Koma ndimasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu mibadwo masauzande amene amandikonda komanso kusunga malamulo anga.+
7 Musagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wanu molakwika,+ chifukwa Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina Lake molakwika osamulanga.+
8 Muzikumbukira tsiku la Sabata ndipo muziliona kuti ndi lopatulika.+ 9 Muzigwira ntchito zanu zonse kwa masiku 6.+ 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu. Musamagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu.*+ 11 Chifukwa kwa masiku 6 Yehova anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndipo anayamba kupuma pa tsiku la 7.+ Nʼchifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata ndipo analipanga kukhala lopatulika.
12 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+
16 Musapereke umboni wonamizira mnzanu.+
17 Musalakelake nyumba ya mnzanu. Musalakelake mkazi wa mnzanu,+ kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ngʼombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzanu.”+
18 Ndiyeno anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, ankaona kungʼanima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva komanso kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaima patali.+ 19 Choncho anthuwo anauza Mose kuti: “Iweyo uzilankhula ndi ife, ndipo ife tizimvetsera, koma Mulungu asalankhule ndi ife kuopera kuti tingafe.”+ 20 Ndiyeno Mose anauza anthuwo kuti: “Musaope, chifukwa Mulungu woona wabwera kuti akuyeseni+ nʼcholinga choti mupitirizebe kumuopa kuti musachimwe.”+ 21 Choncho anthuwo anaimabe patali pomwepo, koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu woona.+
22 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Aisiraeli uwauze kuti, ‘Mwaona nokha kuti ine ndalankhula nanu kuchokera kumwamba.+ 23 Musadzipangire milungu yasiliva komanso milungu yagolide kuti muziilambira pamodzi ndi ine.+ 24 Mundipangire guwa lansembe ladothi, ndipo muziperekapo nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zamgwirizano,* nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu. Dziwani kuti mʼmalo onse amene ndachititsa dzina langa kukumbukiridwa,+ ndidzabwera kwa inu kumeneko ndipo ndidzakudalitsani. 25 Mukamandipangira guwa lansembe lamiyala, musamamangire miyala yosemedwa ndi zida.+ Chifukwa mukagwiritsa ntchito miyala yosema, ndiye kuti mwadetsa guwalo. 26 Ndipo guwa langa lansembe lisakhale lamasitepe, kuopera kuti pokwera pamenepo maliseche anu angaonekere.’”