Ekisodo
21 “Izi ndi zigamulo zoti uwauze:+
2 Mukagula kapolo wa Chiheberi,+ adzakhala kapolo wanu kwa zaka 6, koma mʼchaka cha 7 muzimumasula ndipo azichoka osapereka chilichonse.+ 3 Ngati anabwera ali yekha, adzachokanso ali yekha. Ngati anabwera ndi mkazi, mkazi wakeyo adzapita naye. 4 Ngati mbuye wake wamupatsa mkazi nʼkumuberekera ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo ndi ana ake adzakhala a mbuye wake, ndipo mwamunayo adzachoka yekha.+ 5 Koma kapoloyo akanena motsimikiza kuti, ‘Ndimakonda kwambiri mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana anga, ndipo sindikufuna kumasulidwa kuti ndichoke,’+ 6 mbuye wakeyo azibwera naye pamaso pa Mulungu woona. Kenako azipita naye pachitseko kapena pafelemu, akatero mbuye wakeyo azimuboola khutu ndi choboolera, ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.
7 Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi kukhala kapolo, sadzachoka ngati mmene akapolo aamuna amachokera. 8 Ngati mbuye wake sakusangalala naye ndipo sakufuna kuti akhale mkazi wake wamngʼono koma akufuna kumugulitsa kwa munthu wina,* mbuyeyo alibe ufulu womugulitsa kwa anthu a mtundu wina chifukwa wamʼchitira zachinyengo. 9 Koma akamupereka kwa mwana wake wamwamuna, azimupatsa ufulu wonse umene umaperekedwa kwa ana aakazi. 10 Mwana wamwamunayo akakwatira mkazi wina, woyambayo asaleke kumʼpatsa chakudya, zovala komanso kugona naye monga mkazi wake.*+ 11 Koma ngati sakumuchitira zinthu zitatu zimenezi, mkaziyo achoke osapereka ndalama iliyonse.
12 Aliyense amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa.+ 13 Koma ngati sanamuphe mwadala ndipo Mulungu woona walola kuti zichitike, ndidzakukonzerani malo amene angathawireko.+ 14 Munthu akamupsera mtima mnzake mpaka kumupha mwadala,+ munthuyo aziphedwa. Ngakhale atathawira kuguwa langa lansembe, muzimuchotsa nʼkukamupha.+ 15 Munthu amene wamenya bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.+
16 Wina akaba munthu+ nʼkumugulitsa kapena akapezeka ndi munthu wobedwayo,+ aziphedwa.+
17 Aliyense wotemberera bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.+
18 Anthu akamakangana, ndiye wina nʼkumenya mnzake ndi mwala kapena chibakera,* mnzakeyo osafa koma wavulala ndipo ali chigonere, muzichita izi: 19 Ngati akutha kudzuka nʼkuyamba kuyendayenda kunja pogwiritsa ntchito ndodo, amene anamʼmenya uja asamalandire chilango. Koma azingopereka malipiro a nthawi imene womenyedwayo wakhala asakugwira ntchito, mpaka mnzakeyo atachiriratu.
20 Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, kapoloyo nʼkumufera, munthuyo azilangidwa ndithu.+ 21 Koma ngati kapoloyo wakhalabe ndi moyo tsiku limodzi kapena masiku awiri, mbuye wakeyo sakuyenera kulangidwa chifukwa kapoloyo anamugula ndi ndalama zake.
22 Ngati amuna akumenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi woyembekezera, moti mkaziyo nʼkubereka mwana nthawi yake isanakwane+ koma palibe amene wamwalira,* wovulaza mkaziyo azimulipiritsa mogwirizana ndi zimene mwamuna wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera kwa oweruza.+ 23 Koma ngati wina wamwalira, pamenepo muzipereka moyo kulipira moyo.+ 24 Wina akavulaza mnzake koopsa, pazikhala diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi,+ 25 kutentha ndi moto kulipira kutentha ndi moto, chilonda kulipira chilonda, kumenya kulipira kumenya.
26 Ngati munthu wamenya kapolo wake wamwamuna kapena kapolo wake wamkazi padiso nʼkumuvulaza kwambiri, azimasula kapoloyo ndipo azimulola kuchoka ngati malipiro a diso lake.+ 27 Ndipo akagulula dzino la kapolo wake wamwamuna kapena la kapolo wake wamkazi, azimasula kapoloyo ndipo azimulola kuchoka ngati malipiro a dzino lake.
28 Ngati ngʼombe yagunda mwamuna kapena mkazi, munthuyo nʼkumwalira, ngʼombeyo iziponyedwa miyala nʼkuphedwa+ ndipo nyama yake sikuyenera kudyedwa. Zikatero mwiniwake wa ngʼombeyo sakuyenera kulangidwa. 29 Koma ngati ngʼombe inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwiniwake anachenjezedwapo koma sankaiyangʼanira, ndiyeno yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iziponyedwa miyala ndipo mwiniwakeyo aziphedwanso. 30 Ngati waweruzidwa kuti apereke dipo,* ayenera kulipira mtengo wonse wowombolera moyo wake umene amugamula. 31 Kaya ngʼombeyo inagunda mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi, mwiniwake wa ngʼombeyo aziweruzidwa mogwirizana ndi chigamulo chimenechi. 32 Ngati yagunda kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwiniwake azilipira ndalama zokwana masekeli* 30 kwa mbuye wa kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iziphedwa mwa kuiponya miyala.
33 Ngati munthu wasiya dzenje losavundikira kapena wakumba dzenje koma osatsekapo ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo, 34 mwiniwake wa dzenjelo azilipira.+ Malipirowo azipereka kwa mwiniwake wa chiwetocho, koma iye azitenga nyama yakufayo. 35 Ngati ngʼombe ya munthu yavulaza nʼkupha ngʼombe ya mnzake, azigulitsa ngʼombe yamoyoyo nʼkugawana ndalamazo komanso azigawana nyama yakufayo. 36 Koma ngati ngʼombeyo inkadziwika kuti ili ndi chizolowezi chogunda zinzake, koma mwiniwake sankaiyangʼanira, azipereka ngʼombe kulipira ngʼombe, ndipo azitenga yakufayo.”