116 Ndimakonda Yehova
Chifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+
2 Amatchera khutu lake nʼkundimvetsera,+
Ndipo ndidzaitanira pa iye moyo wanga wonse.
3 Zingwe za imfa zinandikulunga.
Ndinkangomva ngati ndatsala pangʼono kufa.+
Ndinavutika chifukwa cha nkhawa komanso chisoni.+
4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+
“Inu Yehova, ndipulumutseni!”
5 Yehova ndi wokoma mtima komanso wolungama.+
Mulungu wathu ndi wachifundo.+
6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+
Ndinafooka chifukwa cha nkhawa koma iye anandipulumutsa.
7 Moyo wanga upumulenso,
Chifukwa Yehova wandichitira zinthu mokoma mtima.
8 Inu mwandipulumutsa ku imfa,
Mwapukuta misozi yanga ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe.+
9 Ndidzayenda pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ndinali ndi chikhulupiriro, nʼchifukwa chake ndinalankhula.+
Ndinavutika kwambiri.
11 Nditapanikizika ndinati:
“Munthu aliyense ndi wabodza.”+
12 Yehova ndidzamubwezera chiyani
Pa zabwino zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso,
Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,
Pamaso pa anthu ake onse.+
15 Mʼmaso mwa Yehova
Imfa ya anthu ake okhulupirika ndi yopweteka kwambiri.+
16 Ndikukupemphani, inu Yehova,
Chifukwa ine ndi mtumiki wanu.
Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.
Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+
17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+
Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+
Pamaso pa anthu ake onse,+
19 Mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,+
Pakati pa iwe Yerusalemu.
Tamandani Ya!+