Numeri
3 Iyi ndi mbiri ya mbadwa za* Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose mʼphiri la Sinai.+ 2 Mayina a ana a Aroni anali awa: woyamba Nadabu kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+ 3 Ana a Aroni mayina awo anali amenewa. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anaikidwa* kuti akhale ansembe.+ 4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova atapereka moto wosaloledwa kwa Yehova+ mʼchipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Pomwe Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo.
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 6 “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+ 7 Iwo azikwaniritsa udindo wawo pomuthandiza komanso potumikira gulu lonse pa ntchito zapachihema chokumanako. 8 Azisamalira ziwiya zonse+ zapachihema chokumanako, komanso kukwaniritsa udindo wawo wotumikira Aisiraeli pogwira ntchito zapachihema.+ 9 Upereke Alevi kwa Aroni ndi ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera kwa Aisiraeli.+ 10 Uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, ndipo azigwira ntchito zawo zaunsembe.+ Munthu wamba* aliyense amene wayandikira malowo, aziphedwa.”+
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12 “Ine ndasankha Alevi pakati pa Aisiraeli mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa* a Aisiraeli+ ndipo Aleviwo adzakhala anga. 13 Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo,+ ndinapatula mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli kuti akhale wanga, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
14 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai+ kuti: 15 “Uwerenge ana a Levi potengera nyumba ya makolo awo komanso mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kupita mʼtsogolo.”+ 16 Choncho Mose anawerenga Aleviwo pomvera zimene Yehova anamulamula. 17 Mayina a ana a Levi anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+
18 Mayina a ana a Gerisoni, potengera mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simeyi.+
19 Ana a Kohati, potengera mabanja awo, anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+
20 Ana a Merari, potengera mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+
Mabanja a Alevi anali amenewa potengera nyumba za makolo awo.
21 Mabanja a Alibini+ ndi Asimeyi anachokera mwa Gerisoni. Amenewa ndi amene anali mabanja a Agerisoni. 22 Amuna onse amene anawerengedwa kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo anakwana 7,500.+ 23 Mabanja a Agerisoni ankamanga misasa yawo kumbuyo kwa chihema,+ mbali yakumadzulo. 24 Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25 Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema+ ndi nsalu yoyala pachihemacho, nsalu yake yophimba,+ nsalu yotchinga pakhomo,+ 26 nsalu+ za mpanda wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe za chinsalu chake, komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.
27 Mabanja a Aamuramu, Aizara, Aheburoni ndi Auziyeli anachokera mwa Kohati.+ Amenewa ndi amene anali mabanja a Akohati. 28 Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, analipo 8,600. Amenewa ntchito yawo inali kutumikira pamalo oyera.+ 29 Mabanja a ana a Kohati ankamanga msasa wawo kumʼmwera kwa chihema.+ 30 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31 Ntchito yawo inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ziwiya+ zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼmalo oyerawo, nsalu yotchinga+ komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+
32 Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndi amene ankayangʼanira anthu onse amene ankatumikira pamalo oyera.
33 Mabanja a Amali ndi Amusi anachokera mwa Merari. Amenewa ndi amene anali mabanja a Amerari.+ 34 Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo analipo 6,200.+ 35 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga msasa wawo kumpoto kwa chihema.+ 36 Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake, zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi zipilala, ziwiya zake zonse+ ndi ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 37 Ankasamaliranso zipilala za mpanda wozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo+ komanso zikhomo ndi zingwe zake.
38 Amene ankamanga msasa wawo kumʼmawa kwa chihema, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira mʼmalo opatulika, mʼmalo mwa Aisiraeli. Munthu wamba aliyense* amene wayandikira malowo, ankayenera kuphedwa.+
39 Amuna onse afuko la Levi amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova analipo 22,000. Anawerenga amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo potengera mabanja awo.
40 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uwerenge ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo+ ndipo ulembe mayina awo. 41 Unditengere Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42 Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 43 Ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, anakwana 22,273.
44 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 45 “Utenge Alevi mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli. Utengenso ziweto za Alevi mʼmalo mwa ziweto za Aisiraeli. Aleviwo akuyenera kukhala anga. Ine ndine Yehova. 46 Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47 utenge masekeli* 5 pa munthu aliyense,+ mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera.* Sekeli imodzi ndi yokwana magera* 20.+ 48 Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera Aisiraeli amene apitirira chiwerengero cha Alevi.” 49 Choncho Mose analandira ndalama zowombolera Aisiraeli amene chiwerengero chawo chinaposa cha Alevi. 50 Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, analandira ndalama zokwana masekeli 1,365, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera. 51 Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.