Machitidwe a Atumwi
2 Tsopano onse anali atasonkhana pamodzi pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite.+ 2 Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo phokoso lake linadzaza mʼnyumba yonse imene iwo anali.+ 3 Kenako anaona malilime ooneka ngati malawi amoto, ndipo anagawanika nʼkukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi. 4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana,* mogwirizana ndi mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.+
5 Pa nthawi imeneyo, Ayuda oopa Mulungu ochokera mʼmitundu yonse yapadziko lapansi ankakhala ku Yerusalemu.+ 6 Choncho mkokomowu utamveka, panasonkhana gulu lalikulu la anthu. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense anawamva akulankhula mʼchilankhulo chake. 7 Zimenezi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Anthuni, kodi onse akulankhulawa si anthu a ku Galileya?+ 8 Ndiye zikutheka bwanji kuti aliyense pagulu lathuli akumva chilankhulo chake? 9 Pano pali Apati, Amedi+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto ndi kuchigawo cha Asia.+ 10 Pali anthu ochokera ku Fulugiya, ku Pamfuliya, ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali pafupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, omwe ndi Ayuda ndiponso anthu amene analowa Chiyuda.+ 11 Komanso pali Akerete ndi Aluya. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu mʼzilankhulo zathu.” 12 Onse anadabwa kwambiri ndipo anathedwa nzeru moti ankafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” 13 Koma ena ankawaseka nʼkumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.”
14 Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Inu anthu a ku Yudeya ndi inu nonse a mu Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetserani mosamala zimene ndikufuna kukuuzani. 15 Sikuti anthuwa aledzera ngati mmene inu mukuganizira, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko mʼmawa.* 16 Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17 ‘“Ndipo mʼmasiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzapereka* mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi aakazi adzalosera. Anyamata adzaona masomphenya ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo ndipo iwo adzanenera.+ 19 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndiponso zizindikiro padziko lapansi. Padzakhala magazi, moto ndi utsi wokwera mʼmwamba. 20 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndiponso laulemerero la Yehova* lisanafike. 21 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”’+
22 Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu wa ku Nazareti ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyera. Anatero kudzera muntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ ngati mmene inunso mukudziwira. 23 Munthu ameneyu, amene anaperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu+ ndi kudziwiratu kwake zamʼtsogolo, munachititsa kuti aphedwe pokhomeredwa pamtengo ndi anthu osamvera malamulo.+ 24 Koma Mulungu anamuukitsa+ pomumasula ku zopweteka* za imfa, chifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwire mwamphamvu.+ 25 Paja Davide ananena za iyeyu kuti, ‘Ndimaika Yehova* patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 26 Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unasangalala ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, 27 chifukwa simudzandisiya* mʼManda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.*+ 28 Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.’*+
29 Abale anga, ndilankhula ndithu momasuka za kholo lathu Davide. Iye anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda,+ ndipo manda ake tili nawo mpaka lero. 30 Iye anali mneneri ndipo ankadziwa kuti Mulungu anamulonjeza polumbira, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi wa mbadwa zake.+ 31 Iye anadziwiratu zamʼtsogolo ndipo ananeneratu za kuuka kwa Khristu kuti sanasiyidwe mʼManda,* komanso thupi lake silinavunde.+ 32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 33 Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu. 34 Ndipotu Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 36 Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphera pamtengo,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.”
37 Iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Abale athu, tichite chiyani pamenepa?” 38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense abatizidwe+ mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera. 39 Chifukwa lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndiponso kwa anthu onse akutali, onse amene Yehova* Mulungu wathu angawasankhe.”+ 40 Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku mʼbadwo wa maganizo olakwikawu.”+ 41 Choncho amene analandira mawu akewo mosangalala anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezereka ndi anthu pafupifupi 3,000.+ 42 Choncho iwo anapitiriza kutsatira zimene atumwiwo ankaphunzitsa, kucheza,* kudyera limodzi+ komanso kupemphera.+
43 Anthu onse anayamba kuchita mantha kwambiri ndipo atumwiwo anayamba kuchita zinthu zodabwitsa ndiponso zizindikiro zambiri.+ 44 Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo. 45 Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo+ nʼkugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.+ 46 Tsiku lililonse ankasonkhana mʼkachisi mogwirizana. Ankaitanirana chakudya mʼnyumba zawo ndiponso ankagawana zakudya mosangalala komanso ndi mtima wonse. 47 Ankatamanda Mulungu ndiponso ankakondedwa ndi anthu onse. Komanso tsiku lililonse, Yehova* anapitiriza kuwonjezera anthu amene ankawapulumutsa.+