Yehova Ndiye Wolamulira Wathu!
“Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.”—MACHITIDWE 5:29, “NW.”
1, 2. Kodi ndi kaimidwe kotani ka atumwi kamene Mboni za Yehova zimatenga pamene malamulo a anthu aombana ndi chifuniro cha Mulungu?
YEHOVA MULUNGU analola amuna 12 kutengeredwa ku bwalo lamilandu lalikulu. Umu munali m’chaka cha 33 C.E., ndipo bwalolo linali Bwalo Lalikulu Lamilandu Lachiyuda. Ozengedwa milanduwo anali atumwi a Yesu Kristu. Tamvetserani! ‘Tinakulamulirani kusaphunzitsa pamaziko a dzina iri,’ atero mkulu wa ansembe, ‘koma mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu.’ Atamva zimenezo, Petro ndi atumwi ena akulengeza kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.” (Machitidwe 5:27-29, NW) Kwenikweni, iwo anati: “Yehova ndiye Wolamulira wathu!”
2 Inde, Yehova ndiye Wolamulira wa atsatiri owona a Yesu. Ichi chamveketsedwa bwino m’bukhu Labaibulo la Machitidwe a Atumwi, lolembedwera mu Roma pafupifupi 61 C.E. ndi “Luka sing’anga wokondedwa.” (Akolose 4:14) Mofanana ndi atumwiwo, anthu a Yehova lerolino amamvera Wolamulira wawo wakumwamba pamene malamulo a anthu aombana ndi chifuniro chake. Koma kodi tingaphunzirenso chiyani m’bukhu la Machitidwe? (Paphunziro laumwini, tikuvomereza kuti muŵerenge mbali za bukhulo zomwe zasonyezedwa m’zilembo zakuda.)
Yesu Atuma Mboni
3. Pamene atsatiri a Yesu ‘abatizidwa ndi mzimu woyera,’ kodi chodera nkhaŵa chawo chachikulu chinali chiyani?
3 Atumwiwo akanatha kutenga kaimidwe kolimba kaamba ka Mulungu chifukwa chakuti adali atalimbikitsidwa mwauzimu. Kristu anafera pamtengo wozunzirapo, koma iwo anadziŵa kuti anali ataukitsidwa. (1:1-5) Yesu “anadziwonetsera yekha wamoyo” ndipo anaphunzitsa chowonadi Chaufumu atavala matupi aumunthu m’masiku 40 onse. Iye anauzanso ophunzira ake kuyembekezera m’Yerusalemu kaamba ka kubatizidwa ndi ‘mzimu woyera.’ Pamenepo kulalikira kukakhala nkhaŵa yawo yaikulu, monga momwe kuliri kwa Mboni za Yehova lerolino.—Luka 24:27, 49; Yohane 20:19–21:24.
4. Kodi chikachitika nchiyani pamene mzimu woyera ukafika pa atsatiri a Yesu?
4 Asanabatizidwebe ndi mzimu woyera, atumwiwo analingalira molakwa kuti ulamuliro wapadziko lapansi ndiwo ukathetsa ufumu wa Roma pamene anafunsa kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” (1:6-8) Ndithudi, Yesu anayankha kuti ayi, pakuti ‘sikunali kwa iwo kudziŵa nthawi kapena nyengo.’ ‘Pamene mzimu woyera ukadza pa iwo,’ uwo ukawapatsa mphamvu ya kuchitira umboni Ufumu wakumwamba wa Mulungu, osati wapadziko iri lapansi. Iwo akalalikira mu Yerusalemu, Yudeya, ndi Samariya, “ndi kufikira malekezero ake a dziko.” Mothandizidwa ndi mzimuwo, Mboni za Yehova zikuchita ntchito yoteroyo pamlingo wa chiunda chonse m’masiku ano otsiriza.
5. Kodi Yesu akadza motani m’njira imene anapitira?
5 Yesu anali atangopereka kumene ntchito ya kulalikira kwa padziko lonse imeneyo pamene anayamba kukwera kumka kumwamba. Kukwera kumeneko kunayamba ndi kunyamuka komka m’mwamba kuchoka kwa ophunzira ake, ndipo pambuyo pake Yesu analowa pamaso pa Wolamulira wake wakumwamba ndi pantchito muufumu wauzimu. (1:9-11) Pamene mtambo unatsekereza atumwi kusawatheketsa kuwona Yesu, iye anavula thupi lake laumunthu. Angelo aŵiri anawonekera ndipo anati iye ‘akadza m’njira yofananayo.’ Ndipo zakhalatu tero. Ophunzira a Yesu okha ndiwo amene anamuwona pochoka, monga momwedi Mboni za Yehova zokha ndizo zazindikira kudza kwake kosawonekako.
Yehova Apanga Chosankha
6. Kodi woloŵa m’malo Yudase Isikariote anasankhidwa motani?
6 Mwamsanga atumwiwo anabwerera ku Yerusalemu. (1:12-26) M’chipinda chapamwamba (mwinamwake m’nyumba ya mayi wa Marko, Mariya), atumwi okhulupirika 11 limodzi ndi abale a Yesu a bambo wina, ophunzira ake ena, ndi amake, Mariya, analimbikira m’pemphero. (Marko 6:3; Yakobo 1:1) Koma kodi ndani yemwe akalandira “udindo” wa Yudase? (Salmo 109:8) Ophunzira pafupifupi 120 analipo pamene Mulungu anasankha mwamuna wodzaloŵa m’malo wopereka Yesu, Yudase, ndi kubwezeretsa chiŵerengero cha atumwi kukhala 12. Wosankhidwayo anafunikira kukhala yemwe adali wophunzira m’nthaŵi ya uminisitala wa Yesu ndi mboni ya kuuka kwake. Ndithudi, mwamunayo anafunikiranso kuvomereza Yehova kukhala Wolamulira wake. Pambuyo papemphero, mayere anaponyedwa pa Matiya ndi Yosefe Barsaba. Mulungu anapangitsa mayerewo kugwera Matiya.—Miyambo 16:33.
7. (a) Kodi zinali bwanji kuti Yudase ‘anagula munda ndi mphotho za chosalungama’? (b) Kodi Yudase anafa motani?
7 Ndithudi Yudase Isikariote sanavomereze Yehova kukhala Wolamulira wake. Eya, iye anapereka Mwana wa Mulungu ndi tindalama tasiliva 30! Yudase anabweza ndalamazo kwa akulu a ansembe, koma Petro anati woperekayo ‘anagula munda ndi mphotho ya chosalungama.’ Motani? Eya, iye anapereka ndalamazo ndi chifukwa chogulira “Munda wa Mwazi,” monga momwe unkatchedwera. Iwo wazindikiridwa kukhala munda wathyathyathya cha kum’mwera kwa Chigwa cha Hinomu. Unansi wake ndi Wolamulira wakumwamba utawonongedweratu, Yudase ‘anadzipachika yekha pakhosi.’ (Mateyu 27:3-10) Mwinamwake chingwecho chinaduka kapena nthambi ya mtengo inakhadzuka, kotero kuti “anagwa chamutu, naphulika pakati” pamene anagwera pa matanthwe osongoka. Aliyense wa ife asakhaletu mbale wonyenga!
Adzazidwa Ndi Mzimu Woyera!
8. Kodi ndiliti pamene ophunzira a Yesu anabatizidwa ndi mzimu woyera, ndipo ndi chiyambukiro chotani?
8 Kodi bwanji ponena za kubatizidwa ndi mzimu woyera kolonjezedwako? Iko kunachitika pa Pentekoste wa 33 C.E., masiku khumi pambuyo pa kukwera kwa Yesu. (2:1-4) Ubatizo umenewo unali wochititsa chidwi chotani nanga! Tangolingalirani chochitikacho. Ophunzira pafupifupi 120 anali m’chipinda chapamwamba pamene ‘mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse.’ Imeneyo sinalitu mphepo, koma inamveka ngati iyo. Malilime “onga amoto” anatera pa wophunzira ndi mtumwi aliyense. “Anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena.” Pamene ubatizo umenewo unachitika, iwo anabadwanso mwa mzimu woyera, anadzozedwa, ndi kuikidwa chizindikiro monga chisonyezero cha choloŵa chauzimu.—Yohane 3:3, 5; 2 Akorinto 1:21, 22; 1 Yohane 2:20.
9. Kodi ophunzira odzazidwa ndi mzimu analankhula ponena za chiyani?
9 Chochitikachi chinayambukira Ayuda ndi otembenuka mu Yerusalemu kuchokera mu ‘mtundu uli wonse pansi pa thambo.’ (2:5-13) Atazizwitsidwa, iwo anafunsa kuti: “Nanga ife timva bwanji yense m’chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?” Chingakhale chinali chinenero cha malo onga ngati Mediya (kummawa kwa Yudeya), Frugiya (mu Asia Minor), ndi Roma (ku Ulaya). Pamene ophunzirawo analankhula “zazikulu za Mulungu” m’zinenero zosiyanasiyana, omvetsera ambiri anadabwa, koma oseka analingalira kuti iwo analedzera.
Petro Apereka Umboni Wochititsa Chidwi
10. Kodi chochitika pa Pentekoste wa 33 C.E. chinakwaniritsa ulosi uti, ndipo kodi ichi chiri ndi kukwaniritsidwa kwake kwamakono?
10 Petro anayamba kuchitira umboni mwakusonyeza kuti 9 koloko inali mmawa kwenikweni kuti munthu nkuledzera. (2:14-21) Mmalo mwake, chochitikachi chinali kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu la kutsanulira mzimu woyera pa anthu ake. Mulungu anauzira Petro kulozera ku nthaŵi yathu mwakuwonjezera mawu akuti “m’masiku otsiriza” ndi akuti “adzanenera.” (Yoweli 2:28-32) Yehova akapereka zozizwa mmwamba ndi zizindikiro padziko lapansi tsiku lake lalikulu lisanadze, ndipo oitanira padzina lake m’chikhulupiriro okha ndiwo akapulumutsidwa. Kutsanulira mzimu kofananako pa odzozedwa kwaŵatheketsa “kunenera” mwamphamvu kwambiri ndipo mogwira mtima lerolino.
11. Ponena za Yesu, kodi nchiyani chimene chinachitidwa ndi Ayuda ndi Mulungu?
11 Kenako Petro anazindikiritsa Mesiya. (2:22-28) Mulungu anachitira umboni Umesiya wa Yesu mwa kumtheketsa kuchita ntchito zazikulu, zizindikiro, ndi zozizwa. (Ahebri 2:3, 4) Koma Ayuda anampachika iye pamtengo “ndi manja a anthu osayeruzika,” Aroma osalabadira chilamulo cha Mulungu. Yesu ‘anaperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu’ m’lingaliro lakuti ichi chinali chifuniro chaumulungu. Komabe, Mulungu anaukitsa Yesu, ndipo anataya thupi lake laumunthulo kotero kuti silinavunde.—Salmo 16:8-11.
12. Kodi Davide anawoneratu chiyani, ndipo kodi chipulumutso chimadalira pachiyani?
12 Ulosi Waumesiya unagogomezeredwa mowonjezereka pamene umboni wa Petro unapitirizabe. (2:29-36) Iye ananena kuti Davide anawoneratu kuukitsidwa kwa mwana wake wamkulu koposa, Yesu Mesiyayo. Kuchokera pamalo okwezeka kudzanja lamanja la Mulungu m’mwamba, Yesu anali atatsanulira mzimu woyera womwe anaulandira kwa Atate wake. (Salmo 110:1) Amvetseri a Petro ‘anawona ndi kumva’ kugwira ntchito kwake pamene anawona malilime onga amoto pa mitu ya atumwiwo ndi kuwamva akulankhula zinenero zachilendo. Iye anasonyezanso kuti chipulumutso chimadalira pa kuzindikira Yesu monga Ambuye ndi Mesiya.—Aroma 10:9; Afilipi 2:9-11.
Yehova Apereka Chiwonjezeko
13. (a) Kuti abatizidwe moyenerera, kodi nchiyani chimene Ayuda ndi otembenuka anafunikira kuvomereza? (b) Kodi ndi angati amene anabatizidwa, ndipo kodi ichi chinali ndi chiyambukiro chotani mu Yerusalemu?
13 Mawu a Petro anali okhutiritsa chotani nanga! (2:37-42) Amvetseri ake analaswa mtima pokhala atavomereza kuphedwa kwa Mesiya. Chotero iye anawafulumiza kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya [mzimu woyera].” Ayuda ndi otembenuka anali atavomereza kale Yehova kukhala Mulungu ndi kufunikira kwawo mzimu wake. Tsopano iwo anangofunikira kulapa ndi kuvomereza Yesu kukhala Mesiya kuti abatizidwe m’dzina (kuzindikira malo antchito kapena ntchito) la Atate, Mwana, ndi mzimu woyera. (Mateyu 28:19, 20) Mwa kuchitira umboni kwa Ayuda ndi otembenuka amenewo, Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yoyamba yauzimu imene Yesu anampatsa kutsegula khomo la chidziŵitso ndi mwaŵi wakuti Ayuda okhulupirira aloŵe mu Ufumu wa kumwamba. (Mateyu 16:19) Patsiku limodzi limenelo, 3,000 anabatizidwa! Tangolingalirani unyinji umenewo wa mboni za Yehova ukumalalikira m’gawo laling’ono la Yerusalemu!
14. Kodi nchifukwa ninji ndipo kodi ndi m’njira yotani mmene akhulupiriri ‘anakhalira nazo zonse zodyerana’?
14 Ambiri ochokera ku zigawo zakutali analibe makonzedwe a kukhala kwa nthaŵi yaitali komatu anafuna kuphunzira zambiri zonena za chikhulupiriro chawo chatsopanocho ndi kulalikira kwa ena. Motero atsatiri oyambirira a Yesu anathandizana mwachikondi, mongatu mmene Mboni za Yehova zimachitira lerolino. (2:43-47) Kwa kanthaŵi kochepa okhulupirira “anakhala nazo zonse zodyerana.” Ena anagulitsa chuma chawo, ndipo ndalamazo zinagaŵiridwa kwa osoŵa. Ichi chinachititsa mpingo kuyamba bwino pamene ‘Yehova anawaonjezera tsiku ndi tsiku opulumutsidwa.’
Kuchiritsa ndi Zotulukapo Zake
15. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Petro ndi Yohane analoŵa m’kachisi, ndipo kodi anthu anachita motani?
15 Yehova anachilikiza atsatiri a Yesu kudzera mwa “zizindikiro.” (3:1-10) Motero, pamene Petro ndi Yohane analoŵa m’kachisi pa 3:00 madzulo kaamba ka ola lakupembedza lochitidwira pamodzi ndi nsembe yamadzulo, munthu wopunduka miyendo chibadwire anali pafupi ndi Khomo Lokongola akumapempha “zaulere.” Petro anati ‘Siliva ndi golidi ndiribe, koma chimene ndiri nacho, ichi ndikupatsa: M’dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda.’ Pomwepo mwamunayo anachiritsidwa! Pamene analoŵa m’kachisi “nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu,” anthu “anadzazidwa ndi kudabwa.” Mwinamwake ena anakumbukira mawu awa: “Wopunduka adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:6.
16. Kodi atumwi anatha motani kuchiritsa munthu wopunduka?
16 Anthu odabwitsidwawo anasonkhana pa khumbi la Solomo, khonde lotsekedwa chakummawa kwa kachisi. Pompo Petro anapereka umboni. (3:11-18) Iye anasonyeza kuti Mulungu anawapatsa atumwi mphamvu ya kuchiritsa munthu wopundukayo kudzera mwa Mtumiki Wake wolemekezedwa, Yesu. (Yesaya 52:13–53:12) Ayuda anamkana ‘woyera ndi wolungamayo’; mosasamala kanthu za izo, Yehova anamuukitsa iye. Ngakhale kuti anthuwo ndi olamulira awo sanadziŵe kuti ankapha Mesiya, m’kuteroko Mulungu anakwaniritsa mawu aulosi akuti “adzamva kuwawa Kristu.”—Danieli 9:26.
17. (a) Kodi Ayuda anafunikira kutenga kachitidwe kotani? (b) Kodi chachitika nchiyani chiyambire ‘kutumizidwa kwa Kristu’ m’tsiku lathu?
17 Chifukwa cha kuchitira Mesiya zimenezo, Petro anasonyeza chimene Ayuda akayenera kuchita. (3:19-26) Iwo anafunikira ‘kulapa,’ kapena kunyansidwa ndi machimo awo, ndi ‘kutembenuka,’ kapena kusandulika, kutenga njira yosiyana. Atakhulupirira mwa Yesu monga Mesiya, kuvomereza dipo, kutsitsimulidwa kukadza kwa iwo kuchokera kwa Yehova monga okhululukidwa machimo. (Aroma 5:6-11) Ayuda anakumbutsidwa kuti iwo anali ana a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo awo, pamene anauza Abrahamu kuti: “Mu mbewu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.” Motero Mulungu anatumiza choyamba Mtumiki wake Waumesiya kudzapulumutsa Ayuda olapa. Mokondweretsa, chiyambire ‘kutumizidwa kwa Kristu’ m’ulamuliro wa Ufumu wakumwamba mu 1914, pakhala kubwezeretsedwa kotsitsimula kwa chowonadi ndi gulu lateokratiki pakati pa Mboni za Yehova.—Genesis 12:3; 18:18; 22:18.
Iwo Sanaleke!
18. Kodi ndi “mwala” wotani umene unayesedwa wopanda pake ndi “omanga nyumba” Achiyuda, ndipo kodi chipulumutso chiri kokha kupyolera mwa yani?
18 Atakwiyitsidwa kuti Petro ndi Yohane analengeza kuuka kwa Yesu, akulu ansembe, mdindo wapakachisi, ndi Asaduki anawaika m’ndende. (4:1-12) Asaduki sanakhulupirire m’chiukiriro, koma ena ambiri anakhulupirira, amuna okha akumafika pachiŵerengero cha 5,000. Atafunsidwa ndi bwalo lalikulu lamilandu la ku Yerusalemu, Petro anati mwamuna wopundukayo anachiritsidwa “m’dzina la Yesu Kristu Mnazarayo,” amene anapachikidwa ndi iwo koma anaukitsidwa ndi Mulungu. “Mwala” woyesedwa wopanda pake ndi “omanga nyumba” Achiyuda umenewu unakhala “mutu wa pangondya.” (Salmo 118:22) “Ndipo,” akutero Petro, “palibe chipulumutso mwa wina yense.”
19. Pamene analamulidwa kuleka kulalikira, kodi atumwi anayankha motani?
19 Kuyesayesa kunapangidwa kwa kuletsa kulankhula koteroko. (4:13-22) Pokhala ndi munthu wochiritsidwayo limodzi nawo, chinali chosatheka kukana “chizindikiro chozindikirika” chimenechi, komabe Petro ndi Yohane anawopsyedwa ‘kusalankhula kapena kuphunzitsa dzina la Yesu kwa munthu aliyense.’ Kodi yankho lawo linali lotani? “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziwona ndi kuzimva.” Iwo anamvera Yehova monga Wolamulira wawo!
Mapemphero Ayankhidwa!
20. Kodi ophunzira anapempherera chiyani, ndipo ndi chotulukapo chotani?
20 Monga mmene Mboni za Yehova zimapempherera pamisonkhano, moteronso ophunzirawo anapemphera pamene atumwi omasulidwawo anasimba zimene zinawachitikira. (4:23-31) Zinadziŵika kuti olamulira Herode Antipa ndi Pontiyo Pilato, limodzi ndi Aroma Akunja ndi anthu a m’Israyeli, anali anasonkhana kutsutsa Mesiya. (Salmo 2:1, 2; Luka 23:1-12) Poyankha pemphero lawo, Yehova anadzaza ophunzirawo ndi mzimu woyera, kotero kuti analankhula mawu a Mulungu molimba mtima. Wolamulira wawo sanapemphedwe kuti athetse chizunzo koma kuti awatheketse kulalikira molimba mtima mosasamala kanthu za icho.
21. Kodi Barnaba anali yani, ndipo kodi iye anali ndi mikhalidwe yotani?
21 Okhulupirira anapitirizabe kukhala nazo zonse zodyerana, ndipo palibe amene anasoŵa kanthu. (4:32-37) Wothandizira wina anali Mlevi Yosefe wa ku Kupro. Atumwi anamutcha Barnaba, lotanthauza ‘Mwana Wachitonthozo,’ mwachidziwikire chifukwa chakuti anali wothandiza ndi wamtima wabwino. Ndithudi, tonsefe tiyenera kufuna kukhala anthu onga iye.—Machitidwe 11:22-24.
Abodza Avumbulidwa
22, 23. Kodi chimo la Hananiya ndi Safira linali chiyani, ndipo kodi tingapindule motani ndi chokumana nacho chawo?
22 Komabe, Hananiya ndi mkazi wake, Safira, analeka kuvomereza Yehova kukhala Wolamulira wawo. (5:1-11) Iwo anagulitsa munda ndi kusunga ndalama zina pamene kwa atumwi anapereka chisonyezero chakuti anawapatsa zonse. Chidziŵitso choperekedwa ndi mzimu wa Mulungu chinatheketsa Petro kuzindikira chinyengo chawo, chikumawatsogolera ku imfa. Ha ndi chenjezo lotani nanga kwa amene Satana akuwayesa kukhala achinyengo!—Miyambo 3:32; 6:16-19.
23 Pambuyo pa chochitikachi, palibe aliyense amene anali ndi cholinga choipa yemwe anakhala wolimbika mtima kuphatikana ndi ophunzirawo. Ena anakhala akhulupiriri. (5:12-16) Ndiponso, pamene odwala ndi ovutitsidwa ndi mizimu yoipa anakhulupirira m’mphamvu ya Mulungu, ‘anachiritsidwa onsewa.’
Mverani Mulungu Koposa Anthu
24, 25. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri Achiyuda anazunza atumwi, koma kodi ndi muyezo wotani umene okhulupirika ameneŵa anakhazikitsa kwa atumiki onse a Yehova?
24 Mkulu wa ansembe ndi Asaduki anayesa tsopano kudodometsa kufutukuka kodabwitsako mwa kuika m’ndende atumwi onse. (5:17-25) Koma usiku umenewo mngelo wa Mulungu anawamasula. Ndipo pofika mbanda kucha iwo ankaphunzitsa m’kachisi! Chizunzo sichingaletse atumiki a Yehova.
25 Komabe, chitsenderezo chinagwiritsiridwa ntchito pamene atumwi anaperekedwa ku Bwalo Lalikulu Lamilandu Lachiyuda. (5:26-42) Komabe, atalamulidwa kuleka kuphunzitsa, iwo anati: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.” (NW) Ichi chinakhazikitsa muyezo kwa ophunzira a Yesu, umene ukutsatiridwa ndi Mboni za Yehova lerolino. Atachenjezedwa ndi m’phunzitsi wa Chilamulo Gamaliyeli, atsogoleriwo anakwapula atumwiwo, ndikuwalamulira kuleka kulalikira, ndipo anawamasula.
26. Kodi ndimotani mmene utumiki wa atumwi umalinganirana ndi wa Mboni za Yehova lerolino?
26 Atumwiwo anasangalala kuti anaŵerengedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu. “Ndipo masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira [mbiri yabwino, NW].” Inde, iwo anali atumiki a kunyumba ndi nyumba. Mboni zamakono za Mulungu zirinso tero, zimene zalandiranso mzimu wake chifukwa chakuti zimamumvera ndikunena kuti, “Yehova ndiye Wolamulira wathu!”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi ntchito yotani imene iyenera kukwaniritsidwa ndi atsatiri a Yesu, kale ndi tsopano lino?
◻ Kodi chinachitika nchiyani pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E.?
◻ Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yoyamba yauzimu imene Yesu anampatsa?
◻ Kodi tingaphunzirenji kuchokera m’cho- kumana nacho cha Hananiya ndi Safira?
◻ Atalamulidwa kuti aleke kulalikira, kodi ndi muyezo wotani umene atumwi anakhazikitsira Mboni za Yehova zonse?