Deuteronomo
22 “Mukaona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wanu ikusochera, musamangoisiya osaibweza.+ Muziikusa nʼkuipititsa kwa mʼbale wanuyo. 2 Koma ngati mwiniwake sakhala pafupi ndi inu kapena simukumudziwa, muzitenga chiwetocho nʼkupita nacho kunyumba kwanu. Muzisunga chiwetocho mpaka mwiniwakeyo atafika kudzachifufuza ndipo muzimubwezera.+ 3 Muzichita zimenezi ndi bulu wa mʼbale wanu, nsalu yake, kapena chilichonse chimene mʼbale wanu wataya inu nʼkuchipeza. Simukuyenera kungochisiya osachitola.
4 Mukaona bulu wa mʼbale wanu kapena ngʼombe yake itagwa pamsewu musamangoisiya. Muzimuthandiza mʼbale wanuyo poidzutsa.+
5 Mkazi asamavale chovala cha mwamuna ndipo mwamuna asamavale chovala cha mkazi. Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.
6 Ngati mwapeza chisa cha mbalame mʼmbali mwa msewu kaya chili mumtengo kapena pansi, muli ana kapena mazira, mayi atafungatira ana kapena mazirawo, musamatenge mayi ndi ana omwe.+ 7 Muzionetsetsa kuti mwathamangitsa mayiyo, koma anawo mungathe kuwatenga. Muzichita zimenezi kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali.
8 Mukamanga nyumba yatsopano muzimanganso kampanda padenga la nyumbayo+ kuopera kuti nyumba yanu ingakhale ndi mlandu wa magazi ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.
9 Mʼmunda wanu wa mpesa musamadzalemo mbewu zamitundu ina,+ chifukwa mukachita zimenezo zokolola zanu zonse komanso mphesa zanu zidzaperekedwa kumalo opatulika.
10 Musamamange ngʼombe ndi bulu kuti muzilimitse pamodzi.+
11 Musamavale chovala chimene anachipanga pophatikiza ubweya wa nkhosa ndi ulusi wa thonje.+
12 Muzimanga ulusi mʼmakona 4 a chovala chanu.+
13 Mwamuna akatenga mkazi nʼkugona naye koma sakumukondanso,* 14 ndipo akumuimba mlandu wochita khalidwe loipa komanso wamuipitsira mbiri yake ponena kuti: ‘Ine ndinatenga mkazi uyu koma nditagona naye, sindinapeze umboni uliwonse woti anali namwali.’ 15 Zikatero bambo ndi mayi a mtsikanayo azipititsa umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali kwa akulu a mzinda, kugeti la mzindawo. 16 Bambo a mtsikanayo aziuza akuluwo kuti, ‘Ine ndinapereka mwana wanga wamkazi kwa mwamuna uyu kuti akhale mkazi wake koma akudana naye,* 17 ndipo akumuimba mlandu wochita khalidwe loipa ponena kuti: “Ndaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti mwana wanuyu anali namwali.” Koma umboni wosonyeza kuti mwana wanga anali namwali ndi uwu.’ Akatero azitambasula chofunda pamaso pa akulu a mzindawo. 18 Ndiyeno akulu+ a mzindawo azigwira mwamunayo nʼkumupatsa chilango.+ 19 Akatero azimulipiritsa masekeli* 100 asiliva, ndipo azipereka ndalamazo kwa bambo a mtsikanayo chifukwa waipitsa mbiri ya namwali wa mu Isiraeli.+ Mtsikanayo apitirize kukhala mkazi wake ndipo sadzaloledwa kumusiya masiku onse a moyo wake.
20 Koma ngati zatsimikizika kuti ndi zoona ndipo palibe umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali, 21 azibweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna amumzindawo azimuponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ pochita chiwerewere* mʼnyumba ya bambo ake.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+
22 Ngati mwamuna wapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, onse awiri, mwamuna amene amagona ndi mkaziyo komanso mkaziyo, azifera limodzi.+ Choncho muzichotsa oipawo mu Isiraeli.
23 Ngati namwali analonjezedwa ndi mwamuna kuti adzamukwatira, ndipo mwamuna wina wamupeza mumzinda nʼkugona naye, 24 onse awiri muziwapititsa kugeti la mzindawo nʼkuwaponya miyala kuti afe. Mtsikanayo afe chifukwa chakuti sanakuwe mumzindawo ndipo mwamunayo afe chifukwa waipitsa mkazi wa mnzake.+ Choncho muzichotsa oipawo pakati panu.
25 Koma ngati mwamunayo anapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo nʼkumugwiririra, mwamunayo afe yekha. 26 Mtsikanayo musamuchite chilichonse. Iye sanachite tchimo loyenera imfa. Mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukira mnzake nʼkumupha.+ 27 Chifukwa chakuti anamupeza kuthengo, ndipo mtsikanayo anakuwa koma panalibe womupulumutsa.
28 Ngati mwamuna wakumana ndi namwali amene sanalonjezedwe ndi mwamuna kuti adzamukwatira ndipo wamugwira nʼkugona naye, ndiyeno agwidwa,+ 29 mwamunayo azipereka masekeli 50 asiliva kwa bambo a mtsikanayo, ndipo azikhala mkazi wake.+ Chifukwa chakuti wamuchititsa manyazi, sadzaloledwa kumusiya masiku onse a moyo wake.
30 Pasapezeke mwamuna aliyense wokwatira mkazi wa bambo ake kuti asachititse manyazi bambo akewo.”*+