Genesis
20 Tsopano Abulahamu anasamutsa msasa wake+ nʼkupita kudziko la Negebu ndipo anayamba kukhala pakati pa Kadesi+ ndi Shura.+ Pamene ankakhala* ku Gerari,+ 2 Abulahamu anabwerezanso kunena za Sara mkazi wake kuti: “Uyu ndi mchemwali wanga.”+ Choncho Abimeleki* mfumu ya ku Gerari atamva zimenezo, anatuma antchito ake kuti akamutenge Sara.+ 3 Pambuyo pake Mulungu anafikira Abimeleki usiku mʼmaloto nʼkumuuza kuti: “Ufatu iwe chifukwa mkazi amene watengayu+ ndi wokwatiwa.”+ 4 Koma Abimeleki anali asanagone ndi Sara. Choncho iye anati: “Yehova, kodi muwononga mtundu womwe ndi wosalakwa?* 5 Kodi mwamunayu sanandiuze yekha kuti, ‘Uyu ndi mchemwali wangaʼ? Ndipo kodi mkaziyunso sananene yekha kuti, ‘Uyu ndi mchimwene wangaʼ? Zimenezitu ndachita popanda mtima wanga kunditsutsa, komanso mosadziwa kuti ndikulakwa.” 6 Kenako Mulungu woona anamuuza mʼmalotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi, ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire. Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu. 7 Tsopano bweza mkaziyo kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri,+ ndipo adzakupempherera+ moti udzakhala ndi moyo. Koma ukapanda kumubweza, udziwe kuti iweyo ndi anthu ako onse ndithu mufa.”
8 Abimeleki anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkuitana antchito ake onse ndipo anawauza zinthu zonsezi moti anthuwo anachita mantha kwambiri. 9 Kenako Abimeleki anaitana Abulahamu nʼkumufunsa kuti: “Nʼchiyani watichitirachi? Ndakuchimwira chiyani ine, kuti ubweretse tchimo lalikulu chonchi pa ine ndi ufumu wanga? Zimene wandichitirazi nʼzosayenera.” 10 Abimeleki anapitiriza kufunsa Abulahamu kuti: “Cholinga chako chinali chiyani makamaka pochita zimenezi?”+ 11 Abulahamu anayankha kuti: “Ndinachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu akuno saopa Mulungu, andipha chifukwa cha mkazi wangayu.’+ 12 Komabe, ndi mchemwali wangadi ameneyu. Bambo athu ndi amodzi, tinangosiyana mayi, ndipo ndinamukwatira.+ 13 Mulungu atandiuza kuti ndichoke kunyumba ya bambo anga+ kuti ndiyambe kuyendayenda, ndinauza mkazi wangayu kuti: ‘Undisonyeze chikondi chokhulupirika pochita izi: Kulikonse kumene tizipita, uziuza anthu kuti: “Uyu ndi mchimwene wanga.”’”+
14 Ndiyeno Abimeleki anatenga nkhosa, ngʼombe ndiponso antchito aamuna ndi aakazi nʼkumupatsa Abulahamu. Anamubwezeranso Sara mkazi wake. 15 Abimeleki anamuuzanso kuti: “Dziko lonseli ndi langa. Ungathe kukhala kulikonse kumene ungakonde.” 16 Kenako Abimeleki anauza Sara kuti: “Ndalama zasiliva 1,000 izi ndikuzipereka kwa mchimwene wakoyu.+ Zikhale umboni wotsimikizira kwa onse amene muli nawo, ndi kwa wina aliyense, kuti ndiwe wosalakwa ndipo sukuyenera kuimbidwa mlandu.” 17 Kenako Abulahamu anayamba kumupempherera kwa Mulungu woona. Choncho Mulungu anachiritsa Abimeleki, mkazi wake komanso akapolo ake aakazi, moti iwo anayamba kubereka ana. 18 Zinatero chifukwa Yehova anachititsa kuti akazi onse amʼnyumba ya Abimeleki asabereke chifukwa cha Sara mkazi wa Abulahamu.+