Deuteronomo
26 “Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu, ndipo mukakalitengadi nʼkumakhalamo, 2 mukatenge zina mwa zipatso zoyambirira pa zokolola* zonse zamʼmunda mwanu zimene mudzakolole mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukaziike mʼdengu nʼkupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuika dzina lake.+ 3 Muzikapita kwa wansembe amene azidzatumikira masiku amenewo nʼkumuuza kuti, ‘Lero ndikuvomereza pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti ndalowadi mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo athu kuti adzatipatsa.’+
4 Ndiyeno wansembeyo azikalandira dengulo mʼmanja mwanu nʼkuliika pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 5 Kenako muzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Bambo anga anali munthu wongoyendayenda wa Chiaramu*+ ndipo anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa amʼbanja lawo+ nʼkukakhala kumeneko monga mlendo. Koma ali kumeneko anakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu.+ 6 Ndipo Aiguputo anayamba kutizunza komanso kutipondereza, moti ankatigwiritsa ntchito yowawa yaukapolo.+ 7 Choncho tinayamba kufuulira Yehova, Mulungu wa makolo athu, ndipo Yehova anamva mawu athu nʼkuona masautso athu, mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu.+ 8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula,+ zinthu zochititsa mantha, zizindikiro ndiponso zodabwitsa.+ 9 Ndiyeno anatibweretsa kumalo ano nʼkutipatsa dziko ili, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za mʼdziko limene Yehova anandipatsa.’+
Ndipo muzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkugwada pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 11 Mukatero muzikasangalala chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu wapereka kwa inuyo ndi anthu a mʼnyumba yanu, komanso kwa Mlevi ndi mlendo amene akukhala pakati panu.+
12 Mukamaliza kusonkhanitsa chakhumi+ chonse cha zokolola zanu mʼchaka chachitatu, chaka chopereka chakhumi, muzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye ndipo azidzadya nʼkukhuta mʼmizinda yanu.*+ 13 Kenako muzidzanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Ndachotsa zinthu zonse zopatulika mʼnyumba mwanga nʼkuzipereka kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati pathu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye,+ mogwirizana ndi zimene munandilamula. Sindinaphwanye kapena kunyalanyaza malamulo anu. 14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nthawi imene ndinali pa chisoni,* kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka zina mwa zinthu zimenezi chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga ndipo ndachita zonse zimene munandilamula. 15 Tsopano yangʼanani pansi kuchokera kumwamba, kumalo anu oyera okhalako, ndipo mudalitse anthu anu Aisiraeli ndi dziko limene mwatipatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ mogwirizana ndi zimene munalumbira kwa makolo athu.’+
16 Lero Yehova Mulungu wanu akukulamulani kuti muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi. Choncho muzisunga ndi kutsatira zimenezi ndi mtima wanu wonse+ komanso moyo wanu wonse. 17 Lero Yehova wakutsimikizirani kuti adzakhala Mulungu wanu ngati mukuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malangizo ake,+ malamulo ake+ ndi zigamulo zake+ ndiponso ngati mukumvera mawu ake. 18 Ndipo lero mwatsimikizira Yehova kuti mudzakhala anthu ake komanso chuma chake chapadera,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani. Ndiponso mwamutsimikizira kuti mudzasunga malamulo ake onse. 19 Zikadzatero adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga.+ Zimenezi zidzachititsa kuti mutamandidwe, mutchuke komanso kuti mulandire ulemerero mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.”