Amosi
8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinaona dengu la zipatso zamʼchilimwe.* 2 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani Amosi?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona dengu la zipatso zamʼchilimwe.” Kenako Yehova anandiuza kuti: “Mapeto a anthu anga Aisiraeli afika ndipo sindidzawakhululukiranso.+ 3 ‘Pa tsiku limenelo nyimbo za mʼkachisi zidzasanduka kulira mokweza,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Padzakhala mitembo yambiri yotayidwa paliponse+ moti kudzangoti zii!’
4 Tamvani izi, inu amene mumapondaponda anthu osauka,
Ndiponso amene mumapha anthu ofatsa mʼdzikoli.+
5 Inu amene mumanena kuti: ‘Kodi chikondwerero cha nthawi imene mwezi watsopano waoneka chitha liti+ kuti tiyambe kugulitsa mbewu zathu?
Sabata+ litha liti kuti tiyambe kutsatsa mbewu zathu,
Kuti tichepetse muyezo wa efa,*
Tiwonjezere kulemera kwa sekeli,*
Komanso kuti tibere anthu ndi masikelo athu achinyengo?+
6 Litha liti kuti tigule anthu ovutika ndi ndalama za siliva,
Anthu osauka pa mtengo wa nsapato,+
Ndiponso kuti tigulitse mbewu zachabechabe?’
7 Yehova, amene ndi ulemerero wa Yakobo,+ walumbira mogwirizana ndi dzina lake kuti:
‘Sindidzaiwala zochita zawo zonse.+
Dziko lonselo lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo,
Nʼkuwinduka, kenako nʼkuphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+
9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo,
Ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,
Ndiponso kuti mʼdzikolo mugwe mdima dzuwa lisanalowe.+
10 Ndidzasandutsa zikondwerero zanu kukhala maliro.+
Ndipo nyimbo zanu zonse zidzasanduka nyimbo zapamaliro.
Ndidzachititsa kuti anthu onse avale ziguduli ndipo mitu yonse idzametedwa mpala.
Ndidzachititsa kuti zikhale ngati maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekha.
Moti mapeto ake adzakhala ngati tsiku lowawa.’
11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwera
Pamene ndidzatumiza njala mʼdziko.
Osati njala ya chakudya kapena ludzu lofuna madzi,
Koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.+
12 Anthu adzayenda modzandira kuchokera kunyanja mpaka kukafika kunyanja,
Kuchokera kumpoto mpaka kukafika kumʼmawa.
Iwo adzayenda uku ndi uku pofunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.
13 Pa tsiku limenelo anamwali okongola ndiponso anyamata adzakomoka,
Iwo adzakomoka chifukwa cha ludzu.
14 Anthu amene amalumbira pa milungu yonama ya ku Samariya+ nʼkumati:
“Pali mulungu wako, iwe Dani,”+
Ndiponso “pali njira ya ku Beere-seba.”+
Adzagwa ndipo sadzadzukanso.’”+