Amosi
8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinaona dengu la zipatso za m’chilimwe.*+ 2 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani+ Amosi?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona dengu la zipatso za m’chilimwe.”+ Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Mapeto afika pa anthu anga Aisiraeli.+ Sindidzawamveranso chisoni.+ 3 ‘Pa tsiku limenelo nyimbo za m’kachisi zidzasanduka kulira kofuula,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Padzakhala mitembo yambiri+ ndipo munthu adzataya mitemboyo panja, pamalo pena paliponse, moti kudzangoti zii!’
4 “Tamverani izi amuna inu, inu amene mukufuna kumeza munthu wosauka+ ndiponso amene mukufuna kufafaniza anthu ofatsa padziko lapansi.+ 5 Inu mukunena kuti: ‘Kodi mwezi watsopano utha liti+ kuti tiyambe kugulitsa chakudya?*+ Komanso sabata+ litha liti kuti tiyambe kuchepetsa muyezo wogulitsira zinthu,+ kukweza mtengo ndi kubera wogula mwa kugwiritsa ntchito masikelo achinyengo?+ 6 Kodi sabata litha liti kuti tigule anthu onyozeka ndi ndalama zasiliva, kuti tigule munthu wosauka pa mtengo wa nsapato ndiponso kuti tigulitse mbewu zachabechabe?’+
7 “Yehova, amene ndi ulemerero wa Yakobo, walumbira pa dzina lake+ kuti, ‘Sindidzaiwala ntchito zawo zonse.+ 8 Pa chifukwa chimenechi dziko lidzagwedezeka,+ ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalira.+ Dziko lonselo lidzasefukira ngati mtsinje wa Nailo ndi kuwinduka, ndipo kenako lidzaphwa ngati mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+
9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,+ ndiponso kuti m’dziko mugwe mdima dzuwa lisanalowe. 10 Ndidzasandutsa zikondwerero zanu kukhala maliro+ ndipo nyimbo zanu zonse zidzakhala nyimbo zoimba polira. Ndidzachititsa kuti anthu onse avale ziguduli* ndipo mitu yonse idzametedwa mpala.+ Ndidzachititsa kuti zochitika pa tsikulo zikhale ngati maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo amene wamwalira,+ moti tsiku la mapeto a zinthu zonsezi lidzakhala lowawa.’
11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwera pamene ndidzatumiza njala m’dziko. Njala imeneyo siidzakhala ya chakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.+ 12 Anthu adzayenda modzandira kuchokera kunyanja mpaka kukafika kunyanja, kuchokera kumpoto mpaka kukafika kum’mawa. Iwo adzakhala akuyendayenda pofunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.+ 13 Pa tsiku limenelo anamwali okongola ndiponso anyamata adzakomoka chifukwa cha ludzu.+ 14 Iwo amalumbira pa milungu yonama ya ku Samariya,*+ ya ku Dani,+ ndi ya ku Beere-seba.*+ Ndithu, anthu amenewa adzagwa ndipo sadzadzukanso.’”+