Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
85 Inu Yehova, dziko lanu mwalisonyeza kukoma mtima.+
Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ukapolo.+
2 Munakhululukira anthu anu zolakwa zawo.
Munawakhululukira machimo awo onse.+ (Selah)
3 Munabweza mkwiyo wanu wonse,
Ndipo simunasonyeze mkwiyo wanu waukulu.+
4 Tibwezeretseni mwakale, inu Mulungu amene mumatipulumutsa,
Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+
5 Kodi mutikwiyira mpaka kalekale?+
Kodi mudzapitiriza kusonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?
6 Kodi simutipatsanso mphamvu
Kuti anthu anu asangalale chifukwa cha inu?+
7 Tisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika inu Yehova,+
Ndipo mutipulumutse.
8 Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanene,
Chifukwa adzanena za mtendere kwa anthu ake,+ kwa okhulupirika ake.
Koma iwo asayambenso kudzidalira kwambiri ngati kale.+
9 Ndithudi, iye ndi wokonzeka kupulumutsa amene amamuopa,+
Kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
10 Chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika zidzakumana.
Chilungamo ndi mtendere zidzakisana.+
11 Kukhulupirika kudzaphuka padziko lapansi,
Ndipo chilungamo chidzayangʼana pansi kuchokera kumwamba.+
12 Ndithudi, Yehova adzapereka zinthu zabwino,+
Ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.+
13 Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+
Ndipo chidzapanga njira kuti mapazi a Mulungu azidutsamo.