Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika
1 Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano*+ komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate komanso Ambuye Yesu Khristu kuti:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zikhale nanu.
2 Nthawi zonse timathokoza Mulungu tikamakutchulani nonsenu mʼmapemphero athu.+ 3 Timachita zimenezi chifukwa nthawi zonse timakumbukira ntchito zanu zachikhulupiriro, ntchito zanu zachikondi komanso kupirira kwanu chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho+ mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu. 4 Chifukwa tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti iye ndi amene anakusankhani. 5 Tikutero chifukwa pamene tinkalalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinkangolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwera ndi mzimu woyera komanso tinalalikira motsimikiza mtima kwambiri. Inunso mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani. 6 Munalandira mawuwo ndi chimwemwe chimene mzimu woyera+ umapereka ngakhale kuti munali pamavuto aakulu. Pamenepa munatsanzira ifeyo+ komanso munatsanzira Ambuye,+ 7 moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.
8 Sikuti mawu a Yehova* ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha, koma kwina kulikonse chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Chifukwa iwo akunenabe za mmene ife tinakumanirana ndi inu koyamba komanso mmene inu munasiyira mafano anu nʼkutembenukira kwa Mulungu,+ kuti muzitumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10 Munatembenukiranso kwa Mulungu kuti muziyembekezera Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwerawo.+