1 Atesalonika
1 Ine Paulo, pamene ndili limodzi ndi Silivano+ ndi Timoteyo,+ ndikulembera mpingo wa Atesalonika wogwirizana+ ndi Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu, kuti:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere+ zikhale nanu.
2 Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu.+ 3 Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro,+ ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra chifukwa cha chiyembekezo+ chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate. 4 Pakuti tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti Mulunguyo ndiye anakusankhani.+ 5 Chifukwa pamene tinali kulalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unakukhudzani kwambiri, komanso unabwera limodzi ndi mphamvu+ ya mzimu woyera, ndipo unachititsa kuti mukhale otsimikiza+ mtima kwambiri. Ndipo inuyo mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.+ 6 Choncho munatsanzira+ ifeyo komanso munatsanzira Ambuye,+ pakuti munalandira mawuwo ndi chimwemwe cha mzimu woyera+ ngakhale kuti munali m’masautso+ ambiri, 7 moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.
8 Ndipotu, si kuti mawu a Yehova+ ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha ayi, koma kwina kulikonse chikhulupiriro+ chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Pakuti iwo amanena mmene ife tinafikira pakati panu koyamba. Amanenanso mmene inu munatembenukira kwa Mulungu, kusiya mafano+ anu kuti mutumikire Mulungu wamoyo+ ndi woona,+ 10 ndi kuyembekezera+ Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa.+ Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo ukubwerawo.+