Nyimbo ya Davide.
15 Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?
Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+
2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,+
Amene amachita zinthu zabwino+
Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+
3 Iye sanena miseche ndi lilime lake,+
Sachitira mnzake choipa chilichonse,+
Ndipo sanyoza anzake.+
4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+
Koma amalemekeza anthu amene amaopa Yehova.
Sasintha zimene walonjeza ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+
5 Sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+
Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+
Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.+