2 Mbiri
25 Amaziya anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadani.+ 2 Amaziya anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova, koma osati ndi mtima wonse. 3 Ndiyeno ufumu wakewo utangokhazikika, anapha atumiki ake amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+ 4 Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo, mʼbuku la Mose, pamene Yehova analamula kuti: “Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita. Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+
5 Kenako Amaziya anasonkhanitsa Ayuda nʼkuwauza kuti aime motsatira nyumba za makolo awo. Anawaika mʼmagulu a anthu 1,000 ndiponso mʼmagulu a anthu 100 limodzi ndi atsogoleri awo, a mafuko a Yuda ndi Benjamini.+ Iye anawalemba mayina anthuwo, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo+ ndipo anapeza kuti panali asilikali ophunzitsidwa bwino* komanso oyenera kupita kunkhondo okwana 300,000, oti angathe kunyamula mkondo waungʼono ndi chishango chachikulu. 6 Komanso analemba ganyu asilikali amphamvu a ku Isiraeli okwana 100,000, pamtengo wa matalente a siliva* 100. 7 Koma munthu wa Mulungu woona anapita kwa Amaziya nʼkumuuza kuti: “Inu mfumu, musalole kuti asilikali a Isiraeli apite nanu limodzi, chifukwa Yehova sali ndi Aisiraeli+ kapenanso mbadwa za Efuraimu. 8 Inuyo mupite nokha kukamenya nkhondo ndipo limbani mtima. Kupanda kutero Mulungu woona angachititse kuti mugonje kwa adani anu, chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu zomuthandiza+ munthu kapena zomʼchititsa kugonja.” 9 Ndiyeno Amaziya anafunsa munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Nanga matalente 100 amene ndapereka kwa asilikali a ku Isiraeli aja?” Munthu wa Mulungu woonayo anayankha kuti: “Yehova akhoza kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.”+ 10 Choncho Amaziya anauza asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efuraimu aja kuti abwerere kwawo. Koma asilikaliwo anawakwiyira kwambiri Ayuda moti anabwerera kwawo atapsa mtima kwambiri.
11 Ndiyeno Amaziya analimba mtima nʼkutsogolera asilikali ake kupita kuchigwa cha Mchere.+ Kumeneko anapha anthu okwana 10,000 a ku Seiri.+ 12 Panalinso anthu 10,000 amene Ayuda anawagwira amoyo. Anthu amenewa anapita nawo pathanthwe lomwe linali pamwamba kwambiri nʼkuyamba kuwaponya kuchokera pathanthwepo ndipo onsewo ananyenyekanyenyeka. 13 Koma asilikali amene Amaziya anawabweza kuti asapite naye kunkhondo aja,+ anayamba kuukira mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya+ mpaka ku Beti-horoni,+ ndipo anapha anthu 3,000 amʼmizindayo nʼkutenga zinthu zambiri.
14 Koma pobwerera kuchokera kokapha Aedomu, Amaziya anatenga milungu ya anthu a ku Seiri nʼkukaiika pamalo ena kuti ikhale milungu yake.+ Kenako anayamba kuigwadira ndiponso kupereka nsembe zautsi kwa milunguyo. 15 Choncho Yehova anakwiyira kwambiri Amaziya ndipo anatumiza mneneri kukamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukutsatira milungu yomwe sinapulumutse anthu awo mʼmanja mwanu?”+ 16 Mneneriyo atanena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Usiyiretu kunena zimenezi.+ Ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndikudziwa kuti Mulungu wakonza zoti akuwonongeni chifukwa cha zimene mwachitazi ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+
17 Atafunsa nzeru kwa alangizi ake, Amaziya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa Yehoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Isiraeli wakuti: “Bwera tidzamenyane.”+ 18 Yehoasi mfumu ya Isiraeli atamva anayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakutchire ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo nʼkupondaponda chitsamba chamingacho. 19 Ukunena kuti, ‘Ine ndagonjetsa Edomu.’+ Choncho wayamba kukula mtima ndipo ukufuna kulemekezedwa. Khala mʼnyumba* mwako momwemo. Nʼchifukwa chiyani ukuputa tsoka chonsecho iwe ndi Ayudawo mugonja?”
20 Koma Amaziya sanamvere,+ popeza Mulungu woona ndi amene anachititsa zimenezi kuti awapereke mʼmanja mwa adani,+ chifukwa iwo anatsatira milungu ya Edomu.+ 21 Choncho Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anapita ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anakumana nʼkuyamba kumenyana ku Beti-semesi+ mʼdziko la Yuda. 22 Pankhondoyo, Ayuda anagonjetsedwa ndi Aisiraeli moti aliyense anathawira kunyumba* kwake. 23 Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, mwana wa Yehoahazi* ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya nʼkupita naye ku Yerusalemu ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Geti la Efuraimu+ mpaka pa Geti la Pakona.+ Anagumula mpata waukulu pafupifupi mamita 178.* 24 Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense komanso ziwiya zonse zimene anazipeza mʼnyumba ya Mulungu woona ndi* Obedi-edomu ndiponso chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Anagwiranso anthu ena ndipo kenako anabwerera ku Samariya.
25 Amaziya+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, anakhalabe ndi moyo zaka 15 pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli.+ 26 Nkhani zina zokhudza Amaziya, kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Yuda ndi a Isiraeli. 27 Amaziya atasiya kutsatira Yehova, anthu anamʼkonzera chiwembu+ ku Yerusalemu ndipo iye anathawira ku Lakisi. Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko nʼkukamuphera komweko. 28 Atatero anamunyamula pamahatchi nʼkukamuika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mumzinda wa Yuda.