Danieli
12 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,*+ kalonga wamkulu+ amene waimirira kuti athandize anthu a mtundu wako,* adzaimirira. Ndiyeno padzafika nthawi yamasautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kudzafika nthawi imeneyo. Pa nthawi imeneyo anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzakhala litalembedwa mʼbuku, adzapulumuka.+ 2 Anthu ambiri amene agona munthaka adzadzuka. Ena adzalandira moyo wosatha koma ena adzachititsidwa manyazi komanso adzadedwa mpaka kalekale.
3 Anthu ozindikira adzawala kwambiri ngati kuwala kwa kuthambo. Ndipo amene akuthandiza anthu ambiri kuti akhale olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka muyaya.
4 Koma iwe Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo umate bukuli mpaka nthawi yamapeto.+ Anthu ambiri adzaphunzira bukuli mokwanira* ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”+
5 Ndiyeno ineyo Danieli nditayangʼana, ndinaona angelo ena awiri ataimirira. Mngelo mmodzi anaima mʼmbali mwa mtsinje tsidya lino ndipo wina anaima tsidya linalo.+ 6 Kenako mmodzi mwa angelowo anafunsa munthu amene anavala nsalu uja,+ amene anaimirira pamwamba pa madzi amumtsinjewo, kuti: “Kodi padzatenga nthawi yaitali bwanji kuti zinthu zodabwitsazi zikwaniritsidwe zonse?” 7 Kenako ndinamva munthu amene anavala nsalu uja, amene anali pamwamba pa madzi amumtsinje akuyankha. Iye anakweza mʼmwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere nʼkulumbira pa Mulungu amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzadutsa nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.* Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya mphamvu za anthu oyera,+ zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”
8 Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.+ Choncho ndinafunsa kuti: “Inu mbuyanga, kodi zinthu zimenezi zidzatha bwanji?”
9 Iye anandiyankha kuti: “Pita Danieli, chifukwa mawuwa akuyenera kusungidwa mwachinsinsi ndi kumatidwa mpaka nthawi yamapeto.+ 10 Anthu ambiri adzadzitsuka, adzadziyeretsa ndipo adzayengedwa.+ Anthu oipa adzachita zinthu zoipa ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa, koma anthu ozindikira adzawamvetsetsa.+
11 Kuchokera pa nthawi imene nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zidzachotsedwe, ndiponso pamene chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko chidzaikidwe,+ padzadutsa masiku 1,290.
12 Wosangalala ndi munthu amene akuyembekezera* mpaka kufika kumapeto kwa masiku 1,335.
13 Koma iwe Danieli upirire mpaka mapeto ndipo udzapuma. Ndiyeno pamapeto amasikuwo udzauka kuti ulandire gawo lako.”+