Mutu 17
Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
1. Malinga n’kunena kwa Danieli chaputala 7, kodi ndi zochitika zodabwitsa zotani zimene zinaonekera kagulu ka anthu ochepa, opanda chida chilichonse m’tsiku lathu?
KAGULU ka anthu ochepa kopanda chida chilichonse kakuukiridwa moopsa ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse. Iwo akupulumuka osavulala m’pang’ono pomwe, m’malo mwake akupeza nyonga yoŵirikiza osati chifukwa cha mphamvu yawo, koma chifukwa chakuti Yehova Mulungu amawakonda. Danieli chaputala 7 ananeneratu zochitika zimenezi, zimene zinaoneka kumayambiriro kwa zaka za zana la 20. Kodi anthuwo anali ayani? Chaputala chimodzimodzicho cha Danieli chinawatcha “opatulika a Wam’mwambamwamba,” Yehova Mulungu. Chinaunikanso kuti anthu ameneŵa potsirizira pake akakhala olamulira mu Ufumu Waumesiya!—Danieli 7:13, 14, 18, 21, 22, 25-27.
2. (a) Kodi Yehova amamva bwanji ponena za atumiki ake odzozedwa? (b) Kodi n’chiyani chingakhale chanzeru kuchita masiku ano?
2 Monga taphunzirira m’Danieli chaputala 11, mfumu ya kumpoto idzakumana ndi chiwonongeko chake pambuyo pododometsa chitetezo cha m’dziko lauzimu la anthu okhulupirika ameneŵa. (Danieli 11:45; yerekezani ndi Ezekieli 38:18-23.) Inde, Yehova amateteza kwambiri odzozedwa ake okhulupirika. Salmo 105:14, 15 limatiuza kuti: “[Yehova] anadzudzula mafumu chifukwa cha iwoŵa; Ndi kuti musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.” Pamenepo, simukuvomereza kodi, kuti m’masiku ano ovuta, n’nkwanzeru kuti “khamu lalikulu” lomakulakulalo ligwirizane mwathithithi ndi opatulika ameneŵa? (Chivumbulutso 7:9; Zekariya 8:23) Yesu Kristu analangiza kuti anthu onga nkhosa akachitedi zimenezo. Akagwirizane ndi abale ake auzimu odzozedwa mwa kuwachirikiza m’ntchito yawo.—Mateyu 25:31-46; Agalatiya 3:29.
3. (a) N’chifukwa chiyani sikuli kwapafupi kupeza otsatira odzozedwa a Yesu ndi kugwirizana nawobe? (b) Kodi lemba la Danieli chaputala 12 litithandiza bwanji pambali imeneyi?
3 Komabe, Mdani wa Mulungu, Satana, wakhala akumenya nkhondo ndi mphamvu zake zonse kulimbana ndi odzozedwawo. Iye walimbikitsa chipembedzo chonyenga, akumadzaza dziko lonse ndi Akristu achiphamaso. Zotsatira zake n’zakuti anthu ambiri asokeretsedwa. Ena amangotaya mtima polephera kupeza anthu oimira chipembedzo choona. (Mateyu 7:15, 21-23; Chivumbulutso 12:9, 17) Ngakhale aja amene amakapeza “kagulu ka nkhosa” nagwirizana nako, ayenerabe kumenya nkhondo kuti asunge chikhulupiriro chawo, chifukwa dzikoli siligona poyesetsa kukokolola chikhulupiriro cha anthu. (Luka 12:32) Bwanji za inuyo? Kodi mwawapeza “opatulika a Wam’mwambamwamba,” ndipo kodi mumayanjana nawo? Kodi muli ndi umboni wodalirika woonetsa kuti amene mwapezawo alidi osankhidwa ndi Mulungu? Umboni woterowo ungalimbikitse chikhulupiriro chanu. Komanso ungakukonzekeretseni kuti muthandize ena kutseguka maso ndi kuona msokonezo wa zipembedzo womwe uli padziko lero. Pa Danieli chaputala 12 pali chuma chimenechi cha chidziŵitso chopatsa moyo.
KALONGA WAMKULU ACHITAPO KANTHU
4. (a) Kodi Danieli 12:1 ananeneratu zinthu ziŵiri zapadera zotani ponena za Mikaeli? (b) M’buku la Danieli, kodi mawu akuti mfumu ‘yaimirira’ kaŵirikaŵiri amatanthauza chiyani?
4 Pa Danieli 12:1 timaŵerenga kuti: ‘Nthaŵi yomweyi adzauka [“adzanyamuka,” NW] Mikaeli kalonga wamkulu [woimirira, NW] kutumikira ana a anthu a mtundu wako.’ Vesi limeneli limaneneratu zinthu ziŵiri zapadera ponena za Mikaeli: choyamba, iye ali “woimirira,” kutanthauza mkhalidwe wa zinthu umene wakhalapobe kwa nyengo yanthaŵi; chachiŵiri, “adzanyamuka,” kusonyeza kuti padzakhala chochitika chimene chidzaoneka m’kati mwa nyengo yanthaŵi imeneyo. Choyamba, tikufuna tidziŵe nyengo ya nthaŵi pamene Mikaeli ali “woimirira kutumikira ana a anthu [a Danieli].” Kumbukirani kuti dzina lakuti Mikaeli linapatsidwa kwa Yesu chifukwa cha udindo wake monga Wolamulira wakumwamba. Mawu akuti ‘kuimirira,’ akutikumbutsa mmene mawuŵa agwiritsidwira ntchito m’malo ena m’buku la Danieli. Kaŵirikaŵiri amanena za chinthu chimene mfumu yachita, monga kuyamba kulamulira monga mfumu.—Danieli 11:2-4, 7, 20, 21, NW.
5, 6. (a) Kodi Mikaeli ali woimirira m’nyengo iti ya nthaŵi? (b) Kodi Mikaeli “adzanyamuka” liti ndipo motani, ndipo zotsatira zake zikakhala zotani?
5 N’zoonekeratu kuti mngelo pano amanena za nyengo ya nthaŵi yotchulidwa penapake mu ulosi wa Baibulo. Yesu anatcha nthaŵiyo kuti “kufika [“kukhalapo,” NW]” kwake (Chigiriki, pa·rou·siʹa), pamene akalamulira monga Mfumu kumwamba. (Mateyu 24:37-39) Nyengo ya nthaŵi imeneyi imatchedwanso “masiku otsiriza” kapena “nthaŵi ya chimaliziro.” (2 Timoteo 3:1; Danieli 12:4, 9) Chiyambireni nyengoyo mu 1914, Mikaeli wakhala ali chiimirire monga Mfumu kumwamba.—Yerekezani ndi Yesaya 11:10; Chivumbulutso 12:7-9.
6 Nanga ndi liti pamene Mikaeli “adzanyamuka”? Ndi pamene adzaima kuti achite chinthu chapadera. Yesu adzachita zimenezo m’tsogolo. Chivumbulutso 19:11-16 chimafotokoza Yesu mwaulosi monga Mfumu yamphamvu Yaumesiya, atakwera kavalo potsogolera khamu lankhondo la angelo, ndi kuwononga adani a Mulungu. Danieli 12:1 akupitiriza kuti: “Ndipo padzakhala nthaŵi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthaŵi yomwe ija.” Monga Wakupha Wamkulu wa Yehova, Kristu adzawononga dongosolo lonse loipali la zinthu panthaŵi ya “masautso aakulu” [“chisautso chachikulu,” NW] onenedweratuwo.—Mateyu 24:21; Yeremiya 25:33; 2 Atesalonika 1:6-8; Chivumbulutso 7:14; 16:14, 16.
7. (a) Kodi okhulupirika onse ali ndi chiyembekezo chotani ponena za “nthaŵi ya masautso”? (b) Kodi buku la Yehova n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika kulembedwamo?
7 Kodi anthu okhulupirika zidzawayendera bwanji zinthu panthaŵi yoopsa imeneyi? Danieli anauzidwanso kuti: “Nthaŵi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene am’peza wolembedwa m’buku.” (Yerekezani ndi Luka 21:34-36.) Ndi buku lotani limenelo? Kwenikweni, limaimira chikumbumtima cha Yehova Mulungu cha aja amene amachita chifuniro chake. (Malaki 3:16; Ahebri 6:10) Aja olembedwa m’buku la moyo limeneli ndiwo anthu otetezeka koposa m’dzikoli, chifukwa chitetezo chawo chimachokera kwa Mulungu. Angakumane ndi chivulazo chotani, chikhoza kukonzedwa ndipo chidzatero. Ngakhale angamwalire isanafike “nthaŵi ya masautso,” amakhalabe osungika m’chikumbumtima chosalephera cha Yehova. Adzawakumbukira ndipo adzawaukitsa m’kati mwa Zaka Chikwi za Ulamuliro wa Yesu Kristu.—Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 20:4-6.
OPATULIKA ‘AUKA’
8. Kodi Danieli 12:2 amapereka chiyembekezo chosangalatsa chotani?
8 Chiyembekezo cha kuuka chilidi chotonthoza. Danieli 12:2 akukhudza nkhani imeneyo, akumati: “Ambiri a iwo ogona m’fumbi lapansi adzauka, ena kumka ku moyo wosatha, ndi ena ku manyazi ndi mnyozo wosatha.” (Yerekezani ndi Yesaya 26:19.) Mawu ameneŵa angatikumbutse za lonjezo lochititsa chidwi la Yesu Kristu la kuuka kwa onse. (Yohane 5:28, 29) Ha, kusangalatsa kwake chiyembekezo chimenecho! Tangoganizani za abwenzi ndi achibale athu okondedwa—amene panthaŵi ino ali m’manda atadzapatsidwa mwayi woti akhalenso ndi moyo! Koma lonjezo la m’buku la Danieli limanena makamaka za mtundu wina wa kuuka—iko kunachitika kale. Koma zimenezo n’kutheka?
9. (a) N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuyembekezera kuti Danieli 12:2 adzakwaniritsidwa m’masiku otsiriza? (b) Kodi ulosiwo umanena za kuuka kotani, ndipo timadziŵa bwanji zimenezo?
9 Taganizirani za nkhani yonse. Monga taonera, vesi loyamba la chaputala 12 limanenanso za nyengo yonse ya masiku otsiriza, osati kokha za mapeto enieni a dongosolo ili la zinthu. Ndi iko komwe, mbali yaikulu ya chaputalacho ikukwaniritsidwa m’kati mwa nthaŵi ya chimaliziro, osati m’paradaiso wapadziko lapansi akudzayo. Kodi m’kati mwa nyengo imeneyi kwakhalapo kuuka kwa akufa kulikonse? Mtumwi Paulo analemba za kuuka kwa “iwo a Kristu” kuti kudzachitika m’nthaŵi ya “kubwera kwake [“kukhalapo kwake,” NW].” Komabe, aja amene akuukitsidwa kuti akakhale ndi moyo kumwamba amaukitsidwa “osavunda.” (1 Akorinto 15:23, 52) Palibe aliyense wa iwo amaukitsidwa “ku manyazi ndi mnyozo wosatha” konenedweratu pa Danieli 12:2. Kodi palinso kuuka kwa mtundu wina? M’Baibulo, kuuka kwa akufa nthaŵi zina kumakhala ndi tanthauzo lauzimu. Mwachitsanzo, mabuku a Ezekieli ndi Chivumbulutso onse ali ndi mauthenga aulosi amene amatanthauza kudzuka kwauzimu, kapena kuuka kwa akufa kwauzimu.—Ezekieli 37:1-14; Chivumbulutso 11:3, 7, 11.
10. (a) Kodi otsalira odzozedwa anaukitsidwa m’ganizo lotani m’nthaŵi ya chimaliziro? (b) Kodi ena mwa odzozedwa odzutsidwawo anadzitengera motani “manyazi ndi mnyozo wosatha”?
10 Kodi kwakhalapo kudzutsidwa kwauzimu kwa atumiki a Mulungu odzozedwa m’nthaŵi ino ya chimaliziro? Inde! Chinali chochitika chenicheni chapadera mu 1918, pamene kagulu kochepa ka otsalira a Akristu okhulupirika anakumana ndi chiukiro choopsa chimene chinasokoneza dongosolo la utumiki wawo wapoyera. Kenako, mosayembekezereka, anakhalanso amoyo mwauzimu mu 1919. Zochitika zimenezi zimayenerana ndi malongosoledwe a kuuka koloseredwa pa Danieli 12:2. Ena ‘anauka’ mwauzimu panthaŵiyo ndi pambuyo pake. Koma n’zachisoni kuti si onse anakhalabe amoyo mwauzimu. Aja amene anakana Mfumu Yaumesiya pambuyo poti aukitsidwa, nasiyanso utumiki wa Mulungu, anadzitengera “manyazi ndi mnyozo wosatha” zotchulidwa pa Danieli 12:2. (Ahebri 6:4-6) Komabe, odzozedwa okhulupirika, potengera mwayi moyo wawo watsopano wauzimu, anachirikiza Mfumu Yaumesiya mokhulupirika. Potsirizira pake, malinga n’kunena kwa ulosi, kukhulupirika kwawo kumawatsogolera ku “moyo wosatha.” Lerolino, timawazindikira chifukwa cha nyonga yawo yauzimu pokumana ndi chitsutso.
‘AŴALA NGATI NYENYEZI’
11. Kodi “aphunzitsiwo” ndani lero, ndipo amaŵala ngati nyenyezi m’lingaliro lotani?
11 Mavesi aŵiri otsatira a Danieli chaputala 12 amatithandizanso kuzindikira “opatulika a Wam’mwambamwamba.” M’vesi 3 mngeloyo akuuza Danieli kuti: “Aphunzitsi adzaŵala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi ku nthaŵi za nthaŵi.” Kodi ‘aphunzitsiwo’ ndani lero? Apanso, umboni ukuloza “opatulika a Wam’mwambamwamba” omwewo. Ndi iko komwe, ndaninso wina, kupatulapo otsalira odzozedwa okhulupirika, amene ali ndi chidziŵitso chozindikira kuti Mikaeli, Kalonga Wamkulu, wakhala ali chiimire monga Mfumu chiyambireni 1914? Mwa kulalikira mfundo za choonadi ngati zimenezi komanso mwa kusunga khalidwe lachikristu, iwo ‘aonekera monga mauniko’ m’dzikoli la mdima wauzimu. (Afilipi 2:15; Yohane 8:12) Ponena za iwo, Yesu analosera kuti: “Pomwepo olungamawo adzaŵalitsa monga dzuŵa, mu Ufumu wa Atate wawo.”—Mateyu 13:43.
12. (a) M’nthaŵi ya chimaliziro, kodi odzozedwa atenga mbali motani m’ntchito ‘yotembenuza ambiri kuti atsate chilungamo’? (b) Kodi odzozedwawo adzatembenuza motani ambiri kuti atsate chilungamo ndi ‘kuŵala ngati nyenyezi’ m’kati mwa Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi?
12 Danieli 12:3 amatiuzanso za ntchito imene Akristu odzozedwa ameneŵa akatanganidwa nayo m’nthaŵi ya chimaliziro. Iwo ‘akatembenuza ambiri atsate chilungamo.’ Otsalira odzozedwawo anayamba kusonkhanitsa otsala a kagulu ka 144,000 oloŵa nyumba anzake a Kristu. (Aroma 8:16, 17; Chivumbulutso 7:3, 4) Pamene ntchitoyo inamalizidwa mwachionekere pakatikati pa ma 1930, iwo tsopano anayamba kusonkhanitsa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Ameneŵanso amasonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Pachifukwa chimenecho, iwo ali ndi khalidwe labwino pamaso pa Yehova. Pofika m’mamiliyoni tsopano, amanyadira chiyembekezo chawo chodzapulumuka chiwonongeko chikudzacho cha dziko loipali. M’kati mwa Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, Yesu limodzi ndi mafumu ndi ansembe anzake okwanira 144,000 adzagwiritsa ntchito pamlingo wonse mapindu a dipolo kwa anthu omvera, ndi kuthandiza onse osonyeza chikhulupiriro mwa kuwachotsera mbali iliyonse ya tchimo la kwa Adamu. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 7:13, 14; 20:5, 6) M’lingaliro lake lenileni, odzozedwa panthaŵiyo adzatenga mbali m’ntchito ‘yotembenuza ambiri kuti akatsate chilungamo’ ndipo ‘adzaŵala ngati nyenyezi’ kumwamba. Kodi mumachiona kukhala chamtengo wapatali chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi m’boma laulemerero lakumwamba la Kristu ndi olamulira anzake? Ulidi mwayi wosaneneka, kutenga nawo mbali “opatulikawo” polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu!—Mateyu 24:14.
‘ATHAMANGA CHAUKO NDI CHAUKO’
13. Kodi mawu a buku la Danieli anakhomeredwa chizindikiro m’lingaliro lotani kuti akhale chinsinsi?
13 Chilengezo cha mngelo kwa Danieli, chimene chinayambira pa Danieli 10:20, tsopano chikutha ndi mawu aŵa: “Koma iwe Danieli, tsekera mawu aŵa, nukhomere chizindikiro buku, mpaka nthaŵi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziŵitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Zambiri zimene Danieli anauziridwa kulemba zinatsekeredwa ndi kukhomeredwa chizindikiro kuti anthu asathe kuzizindikira. Eya, Danieli mwiniyo anadzalemba kuti: “Ndinachimva ichi, koma osachizindikira.” (Danieli 12:8) M’lingaliro limeneli, buku la Danieli linakhalabe lokhomeredwa chizindikiro zaka mazanamazana. Nanga lero bwanji?
14. (a) M’kati mwa “nthaŵi ya chimaliziro,” kodi ndayani akhala ‘akuthamanga chauko ndi chauko,’ ndipo akhala akuthamanga kuti? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova wadalitsa ‘kuthamanga kumeneko’?
14 Ifetu tili ndi mwayi wokhala mu “nthaŵi ya chimaliziro” yoloseredwa m’buku la Danieli. Malinga ndi ulosiwo, okhulupirika ambiri ‘athamanga chauko ndi chauko’ m’masamba a Mawu a Mulungu. Zotsatira zake? Ndi dalitso la Yehova, chidziŵitso choona chachulukadi. Mboni za Yehova zokhulupirika zodzozedwa zadalitsidwa ndi chidziŵitso chozitheketsa kuzindikira kuti Mwana wa munthu anakhala Mfumu mu 1914, kuzindikira zilombo za mu ulosi wa Danieli, ndi kuchenjeza za “chonyansa chopululutsa”—kungotchulapo zitsanzo zochepa chabe. (Danieli 11:31) Choncho, kuchuluka kwa chidziŵitso kumeneku ndi umboni winanso wozindikiritsa “opatulika a Wam’mwambamwamba.” Koma Danieli analandira umboni winanso.
‘AMWAZIDWA’
15. Kodi mngeloyo tsopano akufunsa funso lotani, ndipo funso limenelo lingatikumbutse za ndani?
15 Mudzakumbukira kuti Danieli analandira mauthenga ameneŵa kwa angelo iye ali m’mpepete mwa “mtsinje waukulu” wa Hidikeli, wotchedwanso Tigirisi. (Danieli 10:4) Tsopano iye akuona angelo atatu nati: “Pamenepo ine Danieli ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo aŵiri ena, wina m’mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m’mphepete mwa mtsinje tsidya lija. Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?” (Danieli 12:5, 6) Funso limene mngelo anafunsa pano lingatikumbutsenso za “opatulika a Wam’mwambamwamba.” Kumayambiriro kwa “nthaŵi ya chimaliziro,” mu 1914, iwo anafunitsitsa kudziŵa yankho la funso lakuti kodi akayembekezera kufikira liti kuti malonjezo a Mulungu akwaniritsidwe. Yankho la funso limeneli limasonyeza kuti ulosiwo umanena za iwo makamaka.
16. Kodi mngeloyo akupereka ulosi wotani, ndipo akugogomeza motani chitsimikizo cha kukwaniritsidwa kwake?
16 Nkhani ya Danieli ikupitiriza kuti: “Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthaŵi, ndi nthaŵi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.” (Danieli 12:7) Imeneyi ndi nkhani yaikulu kwambiri. Mngeloyo akukweza manja ake onse aŵiri polumbira, mwina kuti kulumbira ndi manjako kuoneke kwa angelo onse aŵiri okhala kumbali zonse za mtsinje waukuluwo. Mwa kutero, iye akugogomeza chitsimikizo cha kukwaniritsidwa kwa ulosiwo. Nangano nthaŵi zoikika zimenezi zikhalapo liti? Yankho lake si lapatali mmene mungaganizire.
17. (a) Ndi mbali zofanana zotani zimene zilipo m’maulosi olembedwa pa Danieli 7:25, Danieli 12:7, ndi Chivumbulutso 11:3, 7, 9? (b) Kodi nthaŵi zitatu ndi theka zimenezi ndi utali wotani?
17 Ulosi umenewu ukufanana kwambiri ndi maulosi ena aŵiri. Woyamba, umene tinaupenda m’Mutu 9 wa buku lino, umapezeka pa Danieli 7:25; ndipo winawo uli pa Chivumbulutso 11:3, 7, 9. Taonani zina mwa mbali zofananazo. Uliwonse ukunena za nthaŵi ya chimaliziro. Maulosi onse aŵiriwo akunena za atumiki opatulika a Mulungu, akumasonyeza kuti iwowo akuzunzidwa mpaka kulepheretsedwa kwakanthaŵi kugwira ntchito yawo yolalikira poyera. Ulosi uliwonse umasonyeza kuti atumiki a Mulungu adzuka kenako ayambiranso ntchito yawo, kulepheretsa cholinga cha ozunzawo. Ndipo ulosi uliwonse umatchula nyengo ya nthaŵi imene opatulikawo akakumana ndi zovuta. Maulosi onse aŵiriwo a pa Danieli (7:25 ndi 12:7) amanena za “nthaŵi, ndi nthaŵi zina, ndi nusu.” Akatswiri a Baibulo ambiri amavomereza kuti zimenezi zimatanthauza nthaŵi zitatu ndi theka. Chivumbulutso chimatchulanso nyengo imodzimodziyo monga miyezi 42, kapena masiku 1,260. (Chivumbulutso 11:2, 3) Zimenezi zikutsimikizira kuti nthaŵi zitatu ndi theka za m’buku la Danieli ndizo zaka zitatu ndi theka, chaka chilichonse chikumakhala ndi masiku 360. Koma kodi masiku 1,260 ameneŵa anayamba liti?
18. (a) Malinga n’kunena kwa Danieli 12:7, n’chiyani chikasonyeza pothera pake pa masiku 1,260? (b) Nanga “mphamvu ya anthu opatulika” inamwazidwa liti, ndipo zinachitika motani? (c) Kodi masiku 1,260 anayamba liti, ndipo ndi motani mmene odzozedwa ‘analoserera m’chiguduli’ m’kati mwa nyengo imeneyo?
18 Ulosi umenewo umatchula pamene masiku 1,260 akathera—kuti “atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo.” Pakatikati pa 1918, mamembala otsogolera bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society, kuphatikizapo pulezidenti wake, J. F. Rutherford, anaimbidwa milandu yowanamizira, naweruzidwa kumangidwa zaka zambiri, ndipo anapita kundende. Opatulika a Mulungu anaonadi ntchito yawo ‘ikumwazidwa,’ ndi mphamvu yawo ikuthyoledwa. Kuŵerenga chafutambuyo zaka zitatu ndi theka kuchokera pakatikati pa 1918 timafika kumapeto kwa 1914. Panthaŵi imeneyo kagulu kochepako ka odzozedwa kanali kukonzekera chizunzo. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inaulika, ndipo chitsutso pa ntchito yawo chinakulakulabe. M’chaka cha 1915, lemba lawo la chaka anatenga funso limene Kristu anafunsa otsatira ake kuti: “Kodi mukhoza kumwera chikho changa?” (Matthew 20:22, King James Version) Malinga ndi ulosi wa pa Chivumbulutso 11:3, nyengo ya masiku 1,260 imene inayambayo inali nthaŵi yolira kwa odzozedwawo—kunali ngati anali kunenera m’chiguduli. Chizunzo chinafika poipa. Ena amaponyedwa m’ndende, ena amamenyedwa ndi magulu achiwawa, ndipo ena amazunzidwa. Ambiri anathedwa nzeru ndi imfa ya pulezidenti woyamba wa Sosaite C. T. Russell, mu 1916. Kodi n’chiyani chikachitika panthaŵi yamdima imeneyi pamene opatulikawo anaphedwa monga gulu lolalikira?
19. Kodi ulosi wa pa Chivumbulutso chaputala 11 umatitsimikizira motani kuti odzozedwawo sakanakhalitsidwa chete kwa nthaŵi yaitali?
19 Ulosi wofanana wa pa Chivumbulutso 11:3, 9, 11 umasonyeza kuti zitaphedwa ‘mboni ziŵirizo,’ zinagona mu imfa kanthaŵi—masiku atatu ndi theka—kufikira zitadzutsidwa. Mofananamo, ulosi wa Danieli chaputala 12 umasonyeza kuti opatulikawo sakakhala chete mpaka kalekale, chifukwa anali ndi ntchito yowonjezereka patsogolo pawo.
‘ATSUKIDWA, KUYERETSEDWA, NDI KUYENGEDWA’
20. Malinga n’kunena kwa Danieli 12:10, ndi madalitso otani amene anadza pa odzozedwawo pambuyo pokumana ndi zovuta zimenezo?
20 Monga taonera kale, Danieli analemba zinthu zimenezi koma sanathe kuzimvetsa. Chikhalirechobe, ayenera kuti anazizwa ngati opatulikawo akamalizidwa ndi ozunzawo, chifukwa anafunsa kuti, “Chitsiriziro cha izi n’chiyani?” Mngeloyo anayankha kuti: “Pita Danieli, pakuti mawuwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa [“nadzayengedwa,” NW] ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.” (Danieli 12:8-10) Ndithudi, panali chiyembekezo chotsimikizirika kwa opatulikawo! M’malo mowonongedwa, iwo akayeretsedwa, akakhala ndi khalidwe labwino pamaso pa Yehova Mulungu monga dalitso. (Malaki 3:1-3) Chidziŵitso chawo m’zinthu zauzimu chikawakhozetsa kukhalabe oyera pamaso pa Mulungu. Mosiyana ndi iwo, anthu oipa akakana kuzindikira zinthu zauzimu. Koma kodi zonsezi zinayenera kuchitika liti?
21. (a) Kodi nyengo ya nthaŵi yonenedweratu pa Danieli 12:11 ikayamba pochitika mikhalidwe yotani? (b) Kodi “nsembe yachikhalire” inali chiyani, ndipo inachotsedwa liti? (Onani bokosi la patsamba 298.)
21 Danieli anauzidwa kuti: “Kuyambira nthaŵi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana aŵiri kudza makumi asanu ndi anayi.” Choncho nyengo ya nthaŵi imeneyi inayenera kuyamba pamene mikhalidwe inayake itayamba. “Nsembe yachikhalire,” kapena “nsembe yopitirira”a inayenera kuchotsedwa. (Danieli 12:11, NW, mawu am’munsi) Ndi nsembe yotani imene mngeloyo amanena? Si nsembe za nyama zoperekedwa pakachisi aliyense wa padziko lapansi. Eya, ngakhale kachisi wa ku Yerusalemu anali chabe ‘wakutsanza woonayo’—woonayo anali kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova, amene anayamba kugwira ntchito pamene Kristu anakhazikitsidwa monga Mkulu wa Ansembe mu 29 C.E.! M’kachisi wauzimu ameneyu, amene akuimira makonzedwe a Mulungu a kulambira koyera, simufunikira nsembe za uchimo zopitirira, chifukwa ‘Kristu anaperekedwa nsembe kamodzi kusenza machimo a ambiri.” (Ahebri 9:24-28) Komabe, Akristu oona onse amapereka nsembe m’kachisi ameneyu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa Iye [Kristu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Choncho mkhalidwe woyamba wa ulosi umenewu—kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire”—unakhalapo pakatikati pa 1918 pamene ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuferatu.
22. (a) Kodi “chonyansa” chopululutsa n’chiyani, ndipo chinakhazikitsidwa liti? (b) Kodi nyengo ya nthaŵi yonenedweratu pa Danieli 12:11 inayamba liti, ndipo inatha liti?
22 Bwanji nanga za mkhalidwe wachiŵiri—‘kuimikidwa,’ kapena kukhazikitsidwa, kwa “chonyansa chakupululutsa”? Monga tinaonera pofotokoza Danieli 11:31, chonyansa chimenechi poyamba chinali bungwe lotchedwa League of Nations limene linadzatulukiranso pambuyo pake monga United Nations. Mabungwe onse aŵiriwo n’ngonyansa m’ganizo lakuti akhala akulengezedwa monga chiyembekezo chokha chopezera mtendere padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezo, m’mitima ya ambiri, mabungwe ameneŵa kwenikweni alanda malo Ufumu wa Mulungu! Bungwe la League of Nations linalengezedwa mwalamulo mu January 1919. Panthaŵiyo, mikhalidwe yonse iŵiri ya pa Danieli 12:11 inachitika. Choncho, masiku 1,290 anayamba kumayambiriro kwa 1919 ndipo anapitirira mpaka m’chilimwe cha 1922.
23. Kodi opatulika a Mulungu anapita bwanji patsogolo pokhala ndi khalidwe loyeretsedwa m’kati mwa masiku 1,290 onenedweratu pa Danieli chaputala 12?
23 M’kati mwa nthaŵi imeneyo, kodi opatulikawo anapita patsogolo pankhani ya kuyeretsedwa ndi kutsukidwa pamaso pa Mulungu? Anatero kumene! M’March 1919, pulezidenti wa Watch Tower Society ndi anzake anatulutsidwa m’ndende. Pambuyo pake anamasulidwa ku milandu yonse yowanamizira. Pozindikira kuti ntchito yawo inali isanathebe, anakangalikanso mwachangu, nalinganiza msonkhano waukulu mu September 1919. M’chaka chimenechonso, inzake ya magazini ya Nsanja ya Olonda inayamba kufalitsidwa. Poyamba inali kutchedwa The Golden Age, (tsopano Galamukani!) Nthaŵi zonse yachirikiza Nsanja ya Olonda povumbula mopanda mantha mikhalidwe yovunda ya dzikoli ndi kuthandiza anthu a Mulungu kukhalabe oyera. Pofika kumapeto kwa masiku 1,290 onenedweratuwo, opatulika anali m’kati mwa kuyeretsedwa ndi kubwezeretsedwa ku mkhalidwe wawo wabwino. Mu September 1922, pafupi kwenikweni ndi pothera nyengo imeneyi, iwo anakhala ndi msonkhano wapadera kwambiri ku Cedar Point, Ohio, U.S.A. Msonkhanowo unapereka chisonkhezero chachikulu pa ntchito yolalikira. Komabe, panafunikira kupitabe patsogolo. Zimenezo zikachitika m’nyengo yotsatira yoikidwiratu.
CHIMWEMWE CHA OPATULIKAWO
24, 25. (a) Ndi nyengo ya nthaŵi yotani imene inanenedweratu pa Danieli 12:12, ndipo zikuoneka kuti inayamba liti, ndipo inatha liti? (b) Kodi mkhalidwe wauzimu wa otsalira odzozedwa unali wotani kumayambiriro kwa masiku 1,335?
24 Mngelo wa Yehova akumaliza ulosi wake wonena za opatulikawo ndi mawu aŵa: “Wodala iye amene ayembekeza, nafikira ku masiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.” (Danieli 12:12) Mngeloyo sakupereka njira iliyonse yodziŵira pamene nyengoyi ikayamba kapena pothera pake. Koma mbiri imasonyeza kuti inangotsatizana ndi nyengo yoyambayo. Ngati zili choncho, ndiye kuti inayambira m’chilimwe cha 1922 mpaka kumayambiriro kwa nyengo yachisanu mu 1926. Kodi opatulikawo anakhala mumkhalidwe wachimwemwe pakutha nyengoyo? Inde, anatero m’njira zofunika zauzimu.
25 Ngakhale utapita msonkhano waukulu wa mu 1922 (wosonyezedwa patsamba 302), ena mwa opatulika a Mulungu anali kusirirabe zinthu zakumbuyo. Mabuku omwe ankawagwiritsabe ntchito kwambiri pamisonkhano anali Baibulo ndi mavoliyumu otchedwa Studies in the Scriptures (Maphunziro a M’Malemba), olembedwa ndi C. T. Russell. Panthaŵiyo, ambiri anali ndi ganizo lakuti 1925 chinali chaka choyamba kuuka akufa ndi kubwezeretsa Paradaiso padziko lapansi. Motero, ambiri anali kutumikira ndi deti loikika m’maganizo. Mpaka ena amachita kunyadira pokana kugwira nawo ntchito yolalikira poyera. Umenewu sunali mkhalidwe wopatsa chimwemwe ayi.
26. Pamene masiku 1,335 anali m’kati, kodi mkhalidwe wauzimu wa odzozedwa unasintha motani?
26 Komabe, m’kati mwa masiku 1,335, zonsezi zinayamba kusintha. Ulaliki unapita patsogolo, pamene makonzedwe anakhazikitsidwa akuti wina aliyense azitenga nawo mbali mu utumiki wakumunda. Misonkhano inasanjidwa yophunzira Nsanja ya Olonda mlungu ndi mlungu. Kope ya March 1, 1925, inali ndi nkhani yapadera kwambiri yakuti “Kubadwa kwa Mtundu,” ndipo inamveketsa bwino kwa anthu a Mulungu zimene zinachitika m’nyengo ya 1914 mpaka 1919. Chitadutsa chaka cha 1925, opatulikawo sanatumikirenso Mulungu ali ndi deti loikika m’maganizo. M’malo mwake, nkhani yaikulu tsopano inali kuyeretsa dzina la Yehova. Kuposa ndi kale lonse, choonadi chofunika chimenechi chinagogomezedwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 1, 1926, m’nkhani yakuti “Ndani Adzalemekeza Yehova?” Pamsonkhano waukulu wa m’May 1926, buku lakuti Deliverance (Kulanditsidwa) linatuluka. (Onani tsamba 302.) Limeneli linali limodzi la mpambo wa mabuku atsopano amene analoŵa m’malo mwa mabuku otchedwa Studies in the Scriptures (Maphunziro a M’Malemba). Opatulika sanasirirenso zakumbuyo. Anayang’ana m’tsogolo ndi chidaliro kaamba ka ntchito inali patsogolo. Choncho molingana ndi ulosi, mmene masiku 1,335 amatha, opatulikawo anali mumkhalidwe wachimwemwe.
27. Kodi kuona mfundo zazikulu za Danieli chaputala 12 kumatithandiza motani kuwazindikira motsimikiza odzozedwa a Yehova?
27 Zoona, sikuti onse anapirirabe m’nyengo yamgwedegwede imeneyi. Mosakayikira, ndiye chifukwa chake mngeloyo anagogomeza kufunika kwa “kuyembekeza.” Amene anapirira ndi kuyembekezerabe anadalitsika kwakukulu. Kuona mfundo zazikulu za Danieli chaputala 12 kumasonyeza bwino zimenezo. Monga kunanenedweratu, odzozedwawo anadzutsidwa, kapena kuukitsidwa, m’ganizo lauzimu. Anapatsidwa chidziŵitso chapadera cha Mawu a Mulungu, napatsidwanso mphamvu ‘yothamangira chauko ndi chauko’ m’Mawuwo, akumatsogoleredwa ndi mzimu woyera, povumbula zinsinsi zakalekale. Yehova anawayeretsa ndi kuwapangitsa kuŵala mwauzimu, ngati nyenyezi zonyezimira. M’kupita kwa nthaŵi, iwonso anabweretsa ambiri kumkhalidwe wolungama pamaso pa Yehova Mulungu.
28, 29. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima za chiyani pamene “nthaŵi ya chimaliziro” ikufika kumathero ake?
28 Pokhalapo zizindikiro zonsezi zowadziŵira “opatulika a Wam’mwambamwamba,” kodi pangakhale chifukwa chilichonse chodzikhululukira nacho cholepherera kuwazindikira komanso kuyanjana nawo? Madalitso odabwitsa ali m’tsogolo kaamba ka khamu lalikulu, limene likugwirizana ndi kagulu ka odzozedwa komacheperachepera potumikira Yehova. Tonsefe tiyenera kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. (Habakuku 2:3) M’tsiku lathu lino, Mikaeli, Kalonga Wamkulu, wakhala ali chiimire kwa zaka zambiri kaamba ka anthu a Mulungu. Posachedwa pompa adzachitapo kanthu monga wakupha wosankhidwa ndi Mulungu kuti adzawononge dongosolo la zinthu lilipoli. Podzatero iye, kodi ife zidzatiyendera bwanji?
29 Yankho pa funso limenelo lidzadalira chosankha chathu pakali pano, kukhala ndi moyo wokhulupirika tsopano kapena ayi. Pofuna kulimbikitsa chosankha chathu chochita zimenezo pamene “nthaŵi ya chimaliziro” ikufika kumapeto, tiyeni tipende vesi lomaliza la buku la Danieli. Kupenda vesi limeneli m’mutu wotsatira kudzatithandiza kuona mmene Danieli anaimira pamaso pa Mulungu wake ndi mmene adzaimira pamaso pa Iye m’tsogolo.
[Mawu a M’munsi]
a Baibulo lachigiriki lotchedwa Septuagint limangoti “nsembe.”
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi Mikaeli ali “woimirira” m’nyengo ya nthaŵi iti, ndipo “adzanyamuka” liti?
• Kodi Danieli 12:2 amanena za kuuka kotani?
• Kodi ndi madeti ati amene amasonyeza poyambira ndi pothera pa
nthaŵi zitatu ndi theka zotchulidwa pa Danieli 12:7?
masiku 1,290 onenedweratu pa Danieli 12:11?
masiku 1,335 oloseredwa pa Danieli 12:12?
• Kodi kupenda Danieli chaputala 12 kumatithandiza motani kuzindikira alambiri oona a Yehova?
[Bokosi pamasamba 298]
KUCHOTSEDWA KWA NSEMBE YACHIKHALIRE
M’buku la Danieli, mawu akuti “nsembe yachikhalire” amapezeka kasanu. Amanena za nsembe zachitamando—“chipatso cha milomo”—zimene atumiki a Yehova Mulungu amapereka kwa iye nthaŵi zonse. (Ahebri 13:15) Kuchotsedwa kwake konenedweratu kumatchulidwa pa Danieli 8:11, 11:31, ndi 12:11.
M’kati mwa nkhondo ziŵirizo za padziko lonse, anthu a Yehova anazunzidwa koopsa mu ulamuliro wa “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera.” (Danieli 11:14, 15) Kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire” kunachitika chakumapeto kwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse pamene ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuferatu chapakatikati pa 1918. (Danieli 12:7) M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, “nsembe yachikhalire” ‘inachotsedwanso’ kwa masiku 2,300 ndi Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America. (Danieli 8:11-14; onani Mutu 10 wa buku lino.) Inachotsedwanso ndi “ankhondo” a Nazi kwa nyengo ya nthaŵi imene utali wake sunatchulidwe m’Malemba.—Danieli 11:31; onani Mutu 15 wa buku lino.
[Tchati/Zithunzi patsamba 301]
NYENGO ZA NTHAŴI ZAULOSI ZA M’BUKU LA DANIELI
Nthaŵi zisanu ndi ziŵiri October 607 B.C.E. kufika
(zaka 2,520): October 1914 C.E.
Danieli 4:16, 25 (Ufumu Waumesiya ukhazikitsidwa.
Onani Mutu 6 wa buku lino.)
Nthaŵi zitatu ndi theka December 1914 mpaka
(Masiku 1,260): June 1918 (Akristu odzozedwa avutitsidwa.
Danieli 7:25; 12:7 Onani Mutu 9 wa buku lino.)
Madzulo 2,300 ndi June 1 kapena 15, 1938, mpaka
m’maŵa: October 8 kapena 22, 1944
Danieli 8:14 (“Khamu lalikulu” lionekera, liŵirikiza.
Onani Mutu 10 wa buku lino.)
Masabata 70 (zaka 490): 455 B.C.E. mpaka 36 C.E.
Danieli 9:24-27 (Kufika kwa Mesiya ndi
utumiki wake wapadziko.
Onani Mutu 11 wa buku lino.)
Masiku 1,290: January 1919 mpaka
Danieli 12:11 September 1922
(Akristu odzozedwa auka
napita patsogolo mwauzimu.)
Masiku 1,335: September 1922 mpaka
Danieli 12:12 May 1926 (Akristu odzozedwa apeza
mkhalidwe wachimwemwe.)
[Zithunzi patsamba 287]
Atumiki otsogolera a Yehova anawakoloŵeka milandu yachinyengo ndi kuwatumiza kundende ya ku Atlanta, Georgia, U.S.A. Kuyambira kulamanja: (okhala pansi) A. H. Macmillan, J. F. Rutherford, W. E. Van Amburgh; (oimirira) G. H. Fisher, R. J. Martin, G. DeCecca, F. H. Robison, ndi C. J. Woodworth
[Zithunzi patsamba 299]
Misonkhano yaikulu yapadera inachitika ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., mu 1919 (pamwambapo) ndi mu 1922 (pamunsipa)
[Chithunzi chachikulu patsamba 302]