1 Samueli
19 Kenako Sauli anauza mwana wake Yonatani komanso atumiki ake onse kuti akufuna kupha Davide.+ 2 Popeza kuti Yonatani, mwana wa Sauli, ankakonda kwambiri Davide,+ iye anauza Davide kuti: “Bambo anga akufuna kukupha. Chonde mawa mʼmawa usamale. Udzapite kukabisala ndipo ukakhale komweko. 3 Ine ndipita nawo kutchire kumene ukabisaleko ndipo ndikaima pafupi ndi bambo anga. Bambo anga ndikalankhula nawo za iwe, ndipo zilizonse zimene zikachitike, ndidzakuuza ndithu.”+
4 Choncho Yonatani analankhula zabwino za Davide+ kwa Sauli bambo ake. Iye anawauza kuti: “Mfumu isachimwire mtumiki wake Davide, chifukwa iye sanakulakwireni, ndipo wakhala akukuchitirani zinthu zabwino kwambiri. 5 Iye anaika moyo wake pangozi* nʼkupha Mfilisiti uja,+ moti Yehova anapulumutsa Aisiraeli.* Inuyo munaona zimenezi ndipo munasangalala. Ndiye nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira magazi osalakwa, popha Davide popanda chifukwa?”+ 6 Sauli anamvera zimene Yonatani ananena, ndipo anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, Davide saphedwa.” 7 Zitatero, Yonatani anaitana Davide nʼkumufotokozera zonse. Kenako, Yonatani anatenga Davide nʼkupita naye kwa Sauli ndipo Davide anapitiriza kukhala ndi Sauli ngati poyamba.+
8 Patapita nthawi, nkhondo inayambanso ndipo Davide anapita kukamenyana ndi Afilisiti. Iye anapha Afilisiti ambiri ndipo Afilisiti otsala anagonja nʼkuthawa.
9 Ndiyeno mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamubwerera Sauli+ ali mʼnyumba mwake mkondo uli mʼmanja. Pa nthawiyi nʼkuti Davide akumuimbira nyimbo ndi zeze.+ 10 Sauli anafuna kubaya Davide ndi mkondo kuti amukhomerere kukhoma. Koma Davide anauzinda moti mkondowo unalasa khoma. Usiku umenewo Davide anathawa. 11 Kenako Sauli anatumiza anthu kuti akazungulire nyumba ya Davide kuti mʼmawa mwake amuphe.+ Koma Mikala mkazi wa Davide anauza Davideyo kuti: “Ngati suthawa* usiku uno, mawa uphedwa.” 12 Nthawi yomweyo, Mikala anathandiza Davide kuti atulukire pawindo nʼkuthawa. 13 Ndiyeno Mikala anatenga fano la terafi* nʼkuliika pabedi. Iye anaika neti yaubweya wa mbuzi pamene Davide ankatsamiritsa mutu wake ndipo anafunditsa fanolo chovala.
14 Sauli anatuma anthu kuti akamutenge Davide, koma Mikala anawauza kuti: “Wadwala.” 15 Choncho Sauli anatuma anthuwo kuti akaone Davide ndipo anawauza kuti: “Mubwere naye kuno pabedi lakelo kuti adzaphedwe.”+ 16 Anthuwo atalowa, anapeza fano la terafi* lili pabedi, neti yaubweya wa mbuzi ili pamene pakanakhala mutu wa Davide. 17 Zitatero Sauli anafunsa Mikala kuti: “Nʼchifukwa chiyani wandipusitsa chonchi nʼkuthawitsa mdani wanga?”+ Mikala anayankha Sauli kuti: “Anandiuza kuti, ‘Ndisiye ndithawe! Apo ayi, ndikupha.’”
18 Davide anathawa nʼkukafika kwa Samueli ku Rama+ ndipo anafotokozera Samueli zonse zimene Sauli anamuchitira. Kenako Davide ndi Samueli anachoka nʼkukakhala ku Nayoti.+ 19 Patapita nthawi, anthu anauza Sauli kuti: “Davide alitu ku Nayoti, ku Rama.” 20 Nthawi yomweyo, Sauli anatumiza anthu kuti akagwire Davide. Anthuwo ataona aneneri achikulire akulosera, Samueli ataimirira nʼkumawatsogolera, iwo analandira mzimu wa Mulungu ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri.
21 Sauli atauzidwa zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza anthu ena, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. Zitatero, Sauli anatumiza gulu lina lachitatu, koma nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. 22 Kenako nayenso Sauli ananyamuka kupita ku Rama. Atafika pachitsime chachikulu chimene chili ku Seku, anafunsa kuti: “Kodi Samueli ndi Davide ali kuti?” Anthu anayankha kuti: “Ali ku Nayoti,+ ku Rama.” 23 Sauli akupitiriza ulendo wake wopita ku Nayoti, ku Rama, nayenso analandira mzimu wa Mulungu ndipo anayamba kuchita zinthu ngati mneneri mpaka kukafika ku Nayoti, ku Rama. 24 Sauli nayenso anavula zovala zake, ndipo anayambanso kuchita zinthu ngati mneneri pafupi ndi Samueli. Iye anagona pomwepo ali wosavala* masana onse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amanena kuti: “Kodi Sauli nayenso ndi mneneri?”+