Numeri
14 Kenako gulu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anapitiriza kulira usiku wonse.+ 2 Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni,+ ndipo gulu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera mʼchipululu muno. 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+ 4 Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+
5 Mose ndi Aroni atamva zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi pamaso pa gulu lonse la Aisiraeli. 6 Ndipo Yoswa+ mwana wa Nuni ndi Kalebe+ mwana wa Yefune, amene anakazonda nawo dzikolo, anangʼamba zovala zawo. 7 Iwo anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Dziko limene tinakalowamo nʼkulizonda ndi dziko labwino kwambiri.+ 8 Ngati Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsadi mʼdzikolo nʼkulipereka kwa ife, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 9 Koma chofunika nʼchakuti musapandukire Yehova, ndipo anthu amʼdzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo, koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope.”
10 Koma gulu lonselo linayamba kunena zoti liwaponye miyala.+ Kenako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisiraeli onse+ pamwamba pa chihema chokumanako.
11 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza mpaka liti?+ Kodi adzayamba liti kundikhulupirira pambuyo pa zizindikiro zonse zimene ndachita pakati pawo?+ 12 Ndiwagwetsera mliri ndi kuwawononga, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwowa.”+
13 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene anthuwa munawalanditsa mʼmanja mwawo pogwiritsa ntchito mphamvu zanu, adzamva zimenezi.+ 14 Iwo akamva adzauza anthu amʼdziko lino, amenenso amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ komanso kuti mumaonekera kwa iwo pamasomʼpamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo, pamene usiku mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto.+ 15 Mukapha anthu onsewa kamodzinʼkamodzi,* mitundu imene yamva za inu idzanena kuti: 16 ‘Yehova analephera kufikitsa anthuwo kudziko limene anawalumbirira, choncho anangowaphera mʼchipululu.’+ 17 Chonde Yehova, tsopano sonyezani kuti mphamvu zanu ndi zazikulu mogwirizana ndi mmene munalonjezera kuti: 18 ‘Yehova ndi wosakwiya msanga, ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.*+ Amakhululukira zolakwa ndi machimo, koma sadzalekerera wolakwa osamupatsa chilango. Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.’+ 19 Chonde, khululukani zolakwa za anthuwa mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chachikulu, ngati mmene mwakhala mukuwakhululukira kuchokera ku Iguputo mpaka pano.”+
20 Ndiyeno Yehova anati: “Chabwino, ndawakhululukira mogwirizana ndi zimene wanena.+ 21 Komanso, pali ine Mulungu wamoyo, dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi ulemerero wa Yehova.+ 22 Komabe anthu onse amene aona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, komanso zimene ndachita mʼchipululu, koma apitiriza kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, ndipo sanamvere mawu anga,+ 23 sadzaliona mʼpangʼono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+ 24 Koma chifukwa choti mtumiki wanga Kalebe+ anali wosiyana ndi ena,* ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse, ndithu ndidzamulowetsa mʼdziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzatenga dzikolo kukhala lawo.+ 25 Popeza Aamaleki ndi Akanani+ akukhala kuchigwa, mawa mubwerere nʼkuyamba ulendo wopita kuchipululu kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.”+
26 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 27 “Kodi gulu la anthu oipa amenewa lingʼungʼudza motsutsana nane mpaka liti?+ Ndamva kungʼungʼudza kumene Aisiraeli akuchita motsutsana nane.+ 28 Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzakuchitirani mogwirizana ndi zimene ndamva mukulankhula.+ 29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30 Nonsenu simudzalowa mʼdziko limene ndinalumbira* kuti mudzakhalamo,+ kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
31 Koma ana anu amene munati adzatengedwa ndi adani,+ amenewo ndi amene ndidzawalowetse mʼdzikolo ndipo adzadziwa dziko limene inu mwalikana.+ 32 Koma inuyo mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno. 33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu kwa zaka 40,+ ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu,* mpaka womalizira kufa wa inu atagona mʼmanda mʼchipululu muno.+ 34 Mudzalangidwa mogwirizana ndi kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, kwa masiku 40.+ Mudzalangidwa kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi, kuti mudziwe kuipa kotsutsana ndi ine.*
35 Ine Yehova ndalankhula. Zimene ndidzachitire gulu lonse la anthu oipali, amene asonkhana kuti atsutsane ndi ine ndi izi: Onse adzafera mʼchipululu muno ndipo adzathera momwe muno.+ 36 Komanso amuna amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo, omwe anabweretsa lipoti loipa nʼkupangitsa kuti anthu onse adandaule motsutsana ndi Mose,+ 37 amuna amene anadzanena zoipa zokhazokha zokhudza dzikolo, Yehova adzawapatsa chilango ndipo adzafa.+ 38 Koma Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene anali mʼgulu la anthu amene anakazonda dziko, adzakhalabe ndi moyo ndithu.”’”+
39 Mose atawauza Aisiraeli onse mawu amenewa, anthu onse anayamba kulira kwambiri. 40 Komanso, iwo anadzuka mʼmawa kwambiri kuti apite kudera lamapiri lija, ndipo anati: “Ife takonzeka kuti tipite kumalo amene Yehova ananena, chifukwa tachimwa.”+ 41 Koma Mose anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya lamulo la Yehova? Zimenezo sizikuthandizani. 42 Musapite kumeneko chifukwa Yehova sali nanu ndipo adani anuwo akakugonjetsani.+ 43 Kumeneko mukakumana ndi Aamaleki komanso Akanani,+ ndipo akakuphani ndi lupanga. Yehova sapita nanu kumeneko chifukwa mwasiya kutsatira Yehova.”+
44 Komabe anthuwo anadzikuza ndipo ananyamuka nʼkupita kudera lamapiri kuja,+ koma Mose limodzi ndi likasa la pangano la Yehova sanachoke pakati pa msasa.+ 45 Zitatero Aamaleki ndi Akanani omwe ankakhala kudera lamapirilo anatsika nʼkuyamba kuwapha ndi kuwabalalitsa mpaka ku Horima.+