Kwa Aefeso
3 Choncho, ine Paulo, ndili mʼndende+ chifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso chifukwa chothandiza inu, anthu a mitundu ina— 2 ndithudi, munamva kuti ndinalandira udindo wokuthandizani+ kuti mupindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, 3 ndiponso kuti anandiululira chinsinsi chopatulika, mogwirizana ndi zimene ndinalemba mwachidule mʼmbuyomu. 4 Choncho mukawerenga zimenezi mutha kuzindikira kuti chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu ndikuchimvetsa bwino. 5 Mʼmibadwo yamʼmbuyo, chinsinsi chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene Mulungu wachiululira panopa kwa atumwi ndi aneneri ake oyera kudzera mwa mzimu.+ 6 Chinsinsi chimenechi nʼchakuti anthu a mitundu ina amene ndi ogwirizana ndi Khristu Yesu, adzalandire cholowa chimene Khristu adzalandire, ndipo adzakhala mbali ya thupi.+ Iwo adzalandiranso zinthu zimene Mulungu watilonjeza chifukwa cha uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki wa zimenezi mogwirizana ndi mphatso yaulere ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, imene ndinapatsidwa pamene anandipatsa mphamvu yake.+
8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunaperekedwa kwa ine, munthu wamngʼono pondiyerekeza ndi wamngʼono kwambiri pa oyera onse.+ Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu, 9 ndiponso kuti ndithandize aliyense kuti aone mmene chinsinsi chopatulikacho+ chikuyendetsedwera. Kwa zaka zambiri, Mulungu amene analenga zinthu zonse, wakhala akubisa chinsinsi chimenechi. 10 Zinakhala choncho kuti kudzera mumpingo,+ maboma ndi maulamuliro amene ali mʼmalo akumwamba tsopano adziwe mbali zosiyanasiyana za nzeru za Mulungu.+ 11 Zimenezi nʼzogwirizana ndi cholinga chamuyaya chimene iye anakhala nacho chokhudza Khristu,+ yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhulawu ndiponso timatha kufika kwa Mulungu mosavuta+ komanso popanda kukayikira chifukwa timakhulupirira Yesu. 13 Choncho ndikukupemphani kuti musafooke poona mavuto amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu, popeza mavuto amene ndikukumana nawowa achititsa kuti mulandire ulemerero.+
14 Pa chifukwa chimenechi ndikupinda mawondo anga kwa Atate, 15 amene amapangitsa banja lililonse, kumwamba ndi padziko lapansi, kuti likhale ndi dzina. 16 Ndikupempha kuti Mulungu amene ali ndi ulemerero waukulu, akuloleni kuti munthu wanu wamkati akhale wamphamvu,+ pogwiritsa ntchito mphamvu imene mzimu wake umapereka. 17 Ndikupemphanso kuti mwa chikhulupiriro chanu, mʼmitima yanu mukhale Khristu komanso chikondi.+ Muzike mizu+ ndiponso mukhale okhazikika pamaziko,+ 18 nʼcholinga choti inu limodzi ndi oyera onse muthe kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwera ndi kuzama kwa choonadi, 19 ndiponso kuti mudziwe chikondi cha Khristu+ chimene chimaposa kudziwa zinthu, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse amene Mulungu amapereka.
20 Tsopano kwa iye amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,+ mogwirizana ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife,+ 21 kwa iye kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo komanso kudzera mwa Khristu Yesu, kumibadwo yonse mpaka muyaya. Ame.