Ekisodo
15 Pa nthawiyo Mose ndi Aisiraeli anaimbira Yehova nyimbo iyi:+
“Ndiimbira Yehova, chifukwa walemekezeka kwambiri.+
Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.+
2 Mphamvu ndi nyonga zanga ndi Ya,* chifukwa wandipulumutsa.+
Ameneyu ndi Mulungu wanga ndipo ndidzamʼtamanda.+ Ndi Mulungu wa bambo anga,+ ndipo ndidzamulemekeza.+
3 Yehova ndi msilikali wamphamvu.+ Dzina lake ndi Yehova.+
4 Magaleta a Farao ndi gulu lake lankhondo wawaponyera mʼnyanja.+
Asilikali odalirika a Farao amira mʼNyanja Yofiira.+
5 Mafunde amphamvu awakwirira. Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+
6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, ndi lamphamvu zochuluka.+
Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.
7 Ndi mphamvu zanu zazikulu mumagwetsa otsutsana nanu.+
Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.
8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu, madzi anaunjikana pamodzi.
Madzi oyenda anaima ngati khoma.
Mafunde amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.
9 Mdaniyo anati: ‘Ndiwathamangira nʼkuwapeza!
Ndigawa chuma chawo mpaka nditakhutira!
Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+
11 Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+
Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu?
Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+
12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko lapansi lawameza.+
13 Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.+
Ndi mphamvu zanu, mudzawatsogolera kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.
15 Pa nthawi imeneyo mafumu a ku Edomu adzachita mantha.
Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera.+
Anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+
16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+
Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala ngati mwala, osachita kanthu.
Mpaka anthu anu atadutsa, inu Yehova,
17 Mudzawabweretsa nʼkuwakhazikitsa mʼphiri limene ndi cholowa chanu.+
Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukhalemo, inu Yehova.
Malo opatulika amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.
18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.+
19 Mahatchi a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa mʼnyanja,+
Yehova wabweza madzi amʼnyanjamo nʼkuwamiza.+
Koma Aisiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+
20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, yemwe anali mchemwali wake wa Aroni, anatenga maseche mʼmanja mwake ndipo akazi ena onse ankamutsatira akuimba maseche nʼkumavina. 21 Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti:
“Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+
Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+
22 Kenako Mose anatsogolera Isiraeli kuchoka ku Nyanja Yofiira ndipo analowa mʼchipululu cha Shura. Iwo anayenda mʼchipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi. 23 Iwo anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Mara.* 24 Choncho anthu anayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Timwa chiyani?” 25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anamusonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko mʼmadzi moti madziwo anakhala okoma.
Pamalo amenewo Mulungu anawapatsa lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo kumeneko anawayesa.+ 26 Iye anawauza kuti: “Mukadzamvera ndi mtima wonse mawu a Yehova Mulungu wanu, nʼkuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani matenda aliwonse amene ndinagwetsera Aiguputo,+ chifukwa ine Yehova ndi amene ndikukuchiritsani.”+
27 Kenako anafika ku Elimu kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza. Choncho iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.