Genesis
30 Rakele ataona kuti sanaberekere Yakobo ana, anayamba kuchitira nsanje mchemwali wake. Iye anauza Yakobo kuti: “Mundipatse ana, apo ayi kuli bwino ndingofa.” 2 Pamenepo Yakobo anamupsera mtima kwambiri Rakele nʼkumuyankha kuti: “Kodi ine ndine Mulungu amene akukulepheretsa kuberekayo?” 3 Kenako Rakele anati: “Tengani kapolo wanga Biliha+ kuti mugone naye nʼcholinga choti andiberekere ana,* kuti inenso ndikhale ndi ana kudzera mwa iye.” 4 Choncho Rakele anapereka kapolo wake Biliha kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake, ndipo iye anagona naye.+ 5 Biliha anakhala woyembekezera ndipo patapita nthawi anamuberekera Yakobo mwana wamwamuna. 6 Ndiyeno Rakele anati: “Mulungu wakhala woweruza wanga komanso wamva mawu anga, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Nʼchifukwa chake Rakele anapatsa mwanayo dzina lakuti Dani.*+ 7 Biliha kapolo wa Rakele anakhalanso woyembekezera moti patapita nthawi anamuberekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 8 Ndiyeno Rakele anati: “Ndalimbana mwamphamvu ndi mchemwali wanga ndipo ndapambananso.” Choncho anapatsa mwanayo dzina lakuti Nafitali.*+
9 Leya ataona kuti wasiya kubereka, anapereka kapolo wake Zilipa kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.+ 10 Zilipa kapolo wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. 11 Zitatero Leya anati: “Ndachita mwayi!” Choncho anapatsa mwanayo dzina lakuti Gadi.*+ 12 Kenako Zilipa kapolo wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 13 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Ndasangalala kwambiri! Akazi adzanena kuti ndine wosangalala.”+ Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Aseri.*+
14 Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni+ anapita kutchire kukayenda. Kumeneko anapezako zipatso za mandereki,* ndipo anazitenga nʼkupita nazo kwa Leya mayi ake. Ndiyeno Rakele anapempha Leya kuti: “Chonde, undipatseko mandereki a mwana wakowa.” 15 Pamenepo, Leya anayankha Rakele kuti: “Kodi si zokwanira kuti unatenga mwamuna wanga?+ Ndiye pano ukufuna kutenganso mandereki a mwana wanga?” Choncho Rakele anati: “Chabwino, usiku walero mwamunayu agona ndi iwe kuti tisinthane ndi mandereki a mwana wakowa.”
16 Pamene Yakobo ankachokera kumunda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nʼkumuuza kuti: “Lero mugona ndi ine, chifukwa ndapereka mandereki a mwana wanga kwa Rakele kuti mugone ndi ine.” Usiku umenewo Yakobo anagonadi ndi Leya. 17 Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anakhala woyembekezera. Patapita nthawi, Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 5. 18 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Mulungu wandipatsa mphoto* chifukwa ndapereka kapolo wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Isakara.*+ 19 Leya anakhalanso woyembekezera, moti patapita nthawi anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 6.+ 20 Ndiyeno Leya anati: “Mulungu wandipatsadi mphoto yabwino. Tsopano mwamuna wanga ayamba kukondwera nane,+ chifukwa ndamuberekera ana aamuna 6.”+ Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Zebuloni.*+ 21 Kenako, Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamupatsa dzina lakuti Dina.+
22 Potsirizira pake, Mulungu anakumbukira Rakele ndipo anamva pemphero lake nʼkumuthandiza kuti ayambe kubereka.*+ 23 Rakele anakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna. Ndiyeno iye anati: “Mulungu wachotsa kunyozeka kwanga.”+ 24 Choncho Rakele anapatsa mwanayo dzina lakuti Yosefe,*+ ndipo anati: “Yehova wandiwonjezera mwana wina wamwamuna.”
25 Rakele atabereka Yosefe, nthawi yomweyo Yakobo anauza Labani kuti: “Ndiloleni ndizipita kwathu, kudziko lakwathu.+ 26 Ndipatseni akazi anga ndi ana anga kuti ndizipita chifukwa ndinakupatsani kale malipiro pokugwirirani ntchito mwakhama, ndipo inunso mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”+ 27 Koma Labani anauza Yakobo kuti: “Ngati wandikomera mtima, uzikhala konkuno. Ndawombeza ndipo ndapeza kuti* Yehova akundidalitsa chifukwa cha iwe.” 28 Anamuuzanso kuti: “Ndiuze malipiro ako ndipo ndikupatsa.”+ 29 Yakobo anayankha Labani kuti: “Inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani, ndiponso mmene ndasamalirira ziweto zanu.+ 30 Mukudziwa kuti ine ndisanabwere munali ndi ziweto zochepa, koma pano ziweto zanu zachuluka ndipo Yehova wakudalitsani kuchokera pamene ndinabwera kuno. Ndiye kodi ineyo ndidzayamba liti kugwirira ntchito banja langa?”+
31 Kenako Labani anati: “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha kuti: “Musandipatse kanthu. Koma mukachita zimene ndikupempheni pano, ndiyambiranso kuweta ziweto zanu, ndipo ndipitiriza kuziyangʼanira.+ 32 Ine ndipita kukayenda pakati pa ziweto zanu zonse lero. Inuyo mukapatule nkhosa iliyonse yamathothomathotho kapena yamawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaingʼono yamphongo yabulauni, ndi mbuzi iliyonse yaikazi yamawangamawanga kapena yamathothomathotho. Kuyambira panopa, ziweto zimene zizibadwa motere zizikhala malipiro anga.+ 33 Tsiku lililonse limene mudzabwere kudzaona malipiro anga, mudzaona chilungamo changa.* Mukadzapeza mbuzi iliyonse yaikazi yopanda mathothomathotho kapena mawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaingʼono yamphongo yomwe si yabulauni ili ndi ine, imeneyo ndiye kuti ndaba.”
34 Pamenepo Labani anati: “Chabwino, zikhale mmene waneneramo.”+ 35 Choncho tsiku limenelo, Labani anachotsa mbuzi zamphongo zamizeremizere ndi zamawangamawanga, ndiponso mbuzi zonse zazikazi zamathothomathotho ndi zamawangamawanga pakati pa ziweto zake. Anachotsanso iliyonse imene inali ndi banga loyera ndi nkhosa iliyonse yamphongo yaingʼono yabulauni, nʼkuzipereka kwa ana ake. 36 Atatero anapita ndi ziweto zakezo kumalo amene anali pamtunda woyenda masiku atatu kuchokera pamene panali Yakobo. Ndipo Yakobo anapitiriza kuweta ziweto zotsala za Labani.
37 Ndiyeno Yakobo anatenga timitengo tatiwisi ta mlanje, amondi ndi katungulume nʼkutisenda makungwa mwa apo ndi apo, mwakuti choyera chamkati mwake chinaonekera. 38 Kenako anaika timitengo timene anatisendasenda tija muzomwera madzi za ziweto. Anatiika mmenemo kuti ziweto zikabwera kudzamwa madzi, zazikazi zikaona timitengoto zizikonzekera kutenga bere.
39 Choncho ziweto zazikazi zikaona timitengoto zinkakonzekera kutenga bere. Zikatero, zinkaswa ana amizeremizere ndi amawangamawanga. 40 Kenako Yakobo anachotsapo nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono nʼkuziika pazokha. Atatero, anapatula nkhosa zonse zamizeremizere ndi zabulauni zimene zinali pakati pa ziweto za Labani. Kenako anatembenuza nkhosa zotsalazo kuti ziyangʼane zamizeremizere ndi zabulauni zija. Iye anaika ziweto zake pazokha, ndipo sanaziphatikize ndi ziweto za Labani. 41 Nthawi zonse ziweto zazikazi zamphamvu zikakonzekera kutenga bere, Yakobo ankaika timitengo tija mʼngalande momwera madzi kuti nkhosazo zitiyangʼane. 42 Koma nkhosazo zikakhala zofooka, iye sankaika timitengo tija momwera madzimo. Choncho nthawi zonse nkhosa zofooka zinkakhala za Labani koma zamphamvu zinkakhala za Yakobo.+
43 Yakobo anapeza chuma chambiri. Iye anali ndi ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna komanso ngamila ndi abulu.+