Oweruza
3 Yehova analola mitundu yotsatirayi kukhalabe mʼdzikoli nʼcholinga choti ayese Aisiraeli onse amene anali asanaonepo nkhondo zimene mtunduwo unamenya ku Kanani.+ 2 (Anachita zimenezi kuti mibadwo ya Aisiraeli imene sinaonepo nkhondo, iphunzire ndi kudziwa kumenya nkhondo.) 3 Mitundu yake inali olamulira 5 a Afilisiti,+ Akanani onse, Asidoni+ komanso Ahivi+ okhala mʼphiri la Lebanoni,+ kuchokera kuphiri la Baala-herimoni mpaka ku Lebo-hamati.*+ 4 Mulungu anagwiritsa ntchito mitunduyi poyesa Aisiraeli kuti aone ngati adzamvere malamulo amene Yehova anapereka kwa makolo awo kudzera mwa Mose.+ 5 Choncho Aisiraeli ankakhala pakati pa Akanani,+ Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 6 Aisiraeli ankakwatira ana aakazi a Akanani ndipo ana awo aakazi ankawapereka kwa ana aamuna a Akananiwo, ndipo Aisiraeli anayamba kulambira milungu ya Akanani.+
7 Choncho Aisiraeli anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova ndipo anaiwala Yehova Mulungu wawo. Iwo ankalambiranso Abaala+ ndi mizati yopatulika.*+ 8 Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli, moti anawapereka* kwa Kusani-risataimu, mfumu ya Mesopotamiya.* Aisiraeli anatumikira Kusani-risataimu zaka 8. 9 Aisiraeli atafuulira Yehova kuti awathandize,+ Yehova anawapatsa munthu woti awapulumutse.+ Munthu wake anali Otiniyeli,+ mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. 10 Mzimu wa Yehova unkamuthandiza+ ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Mesopotamiya* mʼmanja mwake, moti anamugonjetsa. 11 Zitatero dziko linakhala pa mtendere zaka 40. Kenako Otiniyeli, mwana wa Kenazi, anamwalira.
12 Aisiraeli anayambiranso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Choncho Yehova analola Egiloni mfumu ya Mowabu+ kuti azipondereza Aisiraeli, chifukwa anachita zoipa pamaso pa Yehova. 13 Kuwonjezera apo, anachititsa kuti Aamoni+ ndi Aamaleki+ alimbane ndi Aisiraeli. Iwo anamenyana ndi Aisiraeliwo nʼkulanda mzinda wa mitengo ya kanjedza.+ 14 Aisiraeli anatumikira Egiloni, mfumu ya Mowabu zaka 18.+ 15 Kenako Aisiraeli anafuulira Yehova kuti awathandize.+ Choncho Yehova anawapatsa mpulumutsi,+ Ehudi+ mwana wa Gera. Ehudi anali munthu wamanzere+ ndipo anali wa fuko la Benjamini.+ Patapita nthawi, Aisiraeli anatumiza msonkho wawo kwa Egiloni mfumu ya Mowabu, ndipo Ehudi ndi amene anakapereka. 16 Ehudi anali atapanga lupanga lakuthwa konsekonse, lotalika mkono umodzi,* ndipo analimangirira mʼchiuno kumanja, mkati mwa chovala chake. 17 Atafika kwa Egiloni mfumu ya Mowabu, anapereka msonkho uja. Egiloni anali munthu wonenepa kwambiri.
18 Ehudi atapereka msonkhowo, iye ndi anthu amene ananyamula msonkhowo ananyamuka nʼkumapita. 19 Koma atafika pamafano osema amene anali ku Giligala,+ anabwerera kwa mfumu nʼkunena kuti: “Pepanitu mfumu, ndili ndi uthenga wachinsinsi woti ndikuuzeni.” Choncho mfumuyo inati: “Tipatseni mpata!” Itanena zimenezi, atumiki onse a mfumuyo anatuluka. 20 Ehudi anayandikira mfumuyo ili yokhayokha mʼchipinda chozizira bwino chapadenga. Ndiyeno ananena kuti: “Uthenga umene ndili nawo ndi wochokera kwa Mulungu.” Atatero, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu. 21 Ndiyeno Ehudi, pogwiritsa ntchito dzanja lamanzere, anasolola lupanga lomwe linali mʼchiuno mwake kumanja nʼkubaya nalo Egiloni mʼmimba. 22 Lupangalo linalowa ndi chogwirira chomwe ndipo mafuta anaphimba lupangalo chifukwa sanalizule mʼmimba mwakemo, ndipo chimbudzi chinayamba kutuluka. 23 Zitatero Ehudi anatulukira pawindo, koma anasiya atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapadenga. 24 Iye atatuluka, atumiki a Egiloni anafika ndipo anapeza kuti zitseko za chipinda chapadenga ndi zokhoma. Ndiyeno anati: “Ayenera kuti akudzithandiza mʼchipinda chozizira bwino chamkati.” 25 Iwo anadikira mpaka kutaya mtima chifukwa anaona kuti mfumu sikutsegula zitseko za chipinda chapadenga. Choncho anatenga kiyi nʼkutsegula zitsekozo ndipo anangoona mbuye wawo ali kwala pansi, atafa.
26 Iwo akuganizaganiza zimene zachitika, Ehudi anathawa, ndipo anadutsa pamafano osema+ nʼkukafika bwinobwino ku Seira. 27 Atafika kumeneko analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ mʼdera lamapiri la Efuraimu.+ Ndiyeno Aisiraeli anatsika naye limodzi kuchoka mʼdera lamapirilo ndipo iye ankawatsogolera. 28 Kenako anawauza kuti: “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka adani anu Amowabu mʼmanja mwanu.” Atatero, anamʼtsatira kukatsekereza Amowabu pamalo owolokera mtsinje wa Yorodano, ndipo sanalole aliyense kuwoloka. 29 Pa nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000.+ Onse anali asilikali amphamvu komanso olimba mtima, koma panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+ 30 Choncho pa tsiku limenelo, Aisiraeli anagonjetsa Amowabu, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere zaka 80.+
31 Pambuyo pa Ehudi panabwera Samagara+ mwana wa Anati. Ameneyu anapha amuna 600 a Chifilisiti+ ndi ndodo yotosera ngʼombe pozitsogolera.+ Ameneyunso anapulumutsa Isiraeli.