1 Mbiri
7 Ana a Isakara analipo 4: Tola, Puwa, Yasubi ndi Simironi.+ 2 Ana a Tola anali Uzi, Refaya, Yerieli, Yahamai, Ibisamu ndi Semuyeli. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo. Pa mbadwa za Tola panali asilikali amphamvu ndipo mʼmasiku a Davide, asilikaliwa analipo 22,600. 3 Mwana wa Uzi anali Izirahiya ndipo ana a Izirahiya anali Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse 5 anali atsogoleri a mabanja awo. 4 Pa mbadwa za anthu amenewa, motsatira nyumba za makolo awo, panali asilikali okonzeka kumenya nkhondo okwana 36,000, chifukwa anali ndi akazi ndi ana ambiri. 5 Abale awo a mabanja onse a Isakara, anali asilikali amphamvu okwana 87,000 pamndandanda wa mayina awo wotsatira makolo awo.+
6 Ana a Benjamini+ analipo atatu: Bela,+ Bekeri+ ndi Yediyaeli.+ 7 Ana a Bela analipo 5: Eziboni, Uzi, Uziyeli, Yerimoti ndi Iri. Iwo anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, asilikali amphamvu ndipo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo, analipo 22,034.+ 8 Ana a Bekeri anali Zemira, Yowasi, Eliezere, Elioenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. 9 Pamndandanda wa mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo, mogwirizana ndi mbadwa zawo, panali asilikali amphamvu okwana 20,200. 10 Mwana wa Yediyaeli+ anali Bilihani. Ana a Bilihani anali Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisi ndi Ahisahara. 11 Onsewa anali ana a Yediyaeli, atsogoleri a nyumba za makolo awo. Iwo anali asilikali amphamvu 17,200, okonzeka kupita ku nkhondo.
12 Mabanja a Supimu ndi Hupimu anali mbadwa za Iro+ ndipo mabanja a Husimu anali mbadwa za Aheri.
13 Ana a Nafitali+ anali Yazieli, Guni, Yezera ndi Salumu ndipo anali mbadwa za Biliha.+
14 Mwana wa Manase,+ yemwe mkazi wake wamngʼono* wa Chisiriya anamʼberekera, anali Asiriyeli. (Mkaziyo anabereka Makiri,+ bambo wa Giliyadi. 15 Makiri anapezera akazi Hupimu ndi Supimu ndipo dzina la mchemwali wake linali Maaka.) Mwana wake wachiwiri anali Tselofekadi,+ koma Tselofekadi anali ndi ana aakazi okhaokha.+ 16 Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina loti Peresi. Mchimwene wake wa Peresi anali Seresi ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rekemu. 17 Mwana wa Ulamu anali Bedani. Amenewa anali ana a Giliyadi. Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. 18 Mchemwali wake wa Giliyadi anali Hamoleketi. Iye anabereka Isihodi, Abi-ezeri ndi Mala. 19 Ana a Semida anali Ahiyani, Sekemu, Liki ndi Aniamu.
20 Mwana wa Efuraimu+ anali Sutela.+ Sutela anabereka Beredi, Beredi anabereka Tahati, Tahati anabereka Eleada, Eleada anabereka Tahati, 21 Tahati anabereka Zabadi ndipo Zabadi anabereka Sutela. Efuraimu anaberekanso Ezeri ndi Eleadi. Iwo anaphedwa ndi anthu a ku Gati+ amene anabadwira mʼdzikolo, chifukwa anapita kukatenga ziweto zawo. 22 Bambo wawo Efuraimu anawalira kwa masiku ambiri ndipo abale ake ankabwera kudzamʼtonthoza. 23 Kenako Efuraimu anagona ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anatenga pakati nʼkubereka mwana wamwamuna. Koma Efuraimu anapatsa mwanayo dzina lakuti Beriya,* chifukwa mkaziyo anabereka pa nthawi imene tsoka linagwera nyumba ya Efuraimu. 24 Mwana wake wamkazi anali Seera ndipo iye anamanga mzinda wa Beti-horoni Wakumunsi+ ndi Wakumtunda+ komanso mzinda wa Uzeni-seera. 25 Efuraimu anabereka Refa ndi Resefe. Resefe anabereka Tela, Tela anabereka Tahani, 26 Tahani anabereka Ladani, Ladani anabereka Amihudi, Amihudi anabereka Elisama, 27 Elisama anabereka Nuni ndipo Nuni anabereka Yoswa.*+
28 Cholowa chawo ndiponso malo awo okhala anali Beteli+ ndi midzi yake yozungulira. Kumʼmawa kunali Naarani, kumadzulo kunali Gezeri ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Sekemu ndi midzi yake yozungulira mpaka kukafika ku Aya* ndi midzi yake yozungulira. 29 Pafupi ndi mbadwa za Manase panali Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, Megido+ ndi midzi yake yozungulira ndiponso Dori+ ndi midzi yake yozungulira. Mbadwa za Yosefe mwana wa Isiraeli zinkakhala mʼmizinda imeneyi.
30 Ana a Aseri anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya+ ndipo mchemwali wawo anali Sera.+ 31 Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli, yemwe anali bambo wa Birizaiti. 32 Hiberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Sua mchemwali wawo. 33 Ana a Yafuleti anali Pasaki, Bimali ndi Asivati. Amenewa anali ana a Yafuleti. 34 Ana a Semeri* anali Ahi, Roga, Yehuba ndi Aramu. 35 Ana a mchimwene wake Helemu* anali Zofa, Imina, Selesi ndi Amali. 36 Ana a Zofa anali Suya, Harineferi, Suwali, Beri, Imura, 37 Bezeri, Hodi, Samima, Silisa, Itirani ndi Beera. 38 Ana a Yeteri anali Yefune, Pisipa ndi Era. 39 Ana a Ula anali Ara, Hanieli ndi Riziya. 40 Onsewa anali ana a Aseri, atsogoleri a nyumba za makolo awo, asilikali amphamvu ochita kusankhidwa. Iwo anali akuluakulu a atsogoleri ndipo pamndandanda wa mayina awo wotsatira makolo awo+ analipo amuna 26,000+ okonzeka kumenya nkhondo.