Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli nʼkukalowa mʼphanga.+
57 Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,
Chifukwa ine ndathawira kwa inu.+
Ndathawira mumthunzi wa mapiko anu mpaka mavuto atadutsa.+
2 Ndikufuulira Mulungu Wamʼmwambamwamba,
Mulungu woona amene akuthetsa mavuto amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.
3 Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba nʼkundipulumutsa.+
Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake. (Selah)
Mulungu adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika ndi choonadi chake.+
4 Ndazunguliridwa ndi mikango.+
Ndikuyenera kugona pakati pa anthu amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,
Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,
Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+
Anakumba dzenje panjira yanga,
Koma agweramo okha.+ (Selah)
Ndidzakuimbirani nyimbo ndi zipangizo zoimbira.
8 Dzuka, iwe ulemerero wanga.
Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.
Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.+
9 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+
Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+