Esitere
7 Kenako mfumu ndi Hamani+ anafika kuphwando limene Mfumukazi Esitere anakonza. 2 Pa tsiku lachiwiri la phwando, pamene ankamwa vinyo, mfumu inafunsanso Esitere kuti: “Ukufuna chiyani Mfumukazi Esitere? Chilichonse chimene ukufuna ndikupatsa. Ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumu wangawu, ndikupatsa.”+ 3 Mfumukazi Esitere anayankha kuti: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndiponso ngati mungandichitire chifundo, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso muteteze anthu a mtundu wanga.+ 4 Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa+ kuti tonse tiphedwe.+ Tikanagulitsidwa kuti tikhale akapolo aamuna ndi aakazi, sindikanalankhula kanthu. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike, chifukwa libweretsanso mavuto kwa inu mfumu.”
5 Zitatero, Mfumu Ahasiwero anafunsa Mfumukazi Esitere kuti: “Wachita zimenezo ndi ndani? Ali kuti munthu amene walimba mtima kuchita zimenezo?” 6 Esitere anati: “Munthu wake ndi Hamani ali apayu, mdani wathu ndiponso munthu woipa.”
Hamani anachita mantha chifukwa cha mfumu ndi mfumukazi. 7 Ndiyeno mfumu inanyamuka paphwandolo itakwiya kwambiri nʼkupita kumunda wamaluwa wapanyumba ya mfumu. Zitatero Hamani ananyamuka kuti achonderere Mfumukazi Esitere kuti ipulumutse moyo wake, chifukwa anadziwa kuti mfumu yatsimikiza kuti imupatse chilango. 8 Kenako mfumu inabwera kuchokera kumunda wamaluwa uja nʼkulowanso mʼnyumba imene munali phwando la vinyo. Ndipo inapeza Hamani atadzigwetsa pampando wokhala ngati bedi pamene panali Esitere. Choncho mfumu inati: “Kodi akufunanso kugwirira mfumukazi mʼnyumba mwanga momwe?” Mfumu itangolankhula zimenezi, anthu anamuphimba nkhope Hamani. 9 Ndiyeno Haribona,+ mmodzi mwa nduna zapanyumba ya mfumu, anati: “Hamani anapanganso mtengo woti apachikepo Moredikayi,+ amene anapereka lipoti lomwe linapulumutsa mfumu.+ Mtengowo ndi wautali mikono 50* ndipo uli kunyumba kwa Hamani.” Zitatero mfumu inati: “Kamʼpachikeni pamtengo womwewo.” 10 Choncho Hamani anamupachika pamtengo umene anakonzera Moredikayi, ndipo mkwiyo wa mfumu unatha.