Esitere
8 Pa tsikuli, Mfumu Ahasiwero anapereka kwa Mfumukazi Esitere nyumba ya Hamani,+ yemwe anali mdani wa Ayuda.+ Ndipo Moredikayi anapita kwa mfumu chifukwa Esitere anali atafotokozera mfumuyo chibale chomwe chinali pakati pawo.+ 2 Kenako mfumu inavula mphete yake yodindira+ imene inalanda Hamani nʼkuipereka kwa Moredikayi. Ndiyeno Esitere anaika Moredikayi kuti aziyangʼanira nyumba ya Hamani.+
3 Kuwonjezera pamenepo, Esitere analankhulanso ndi mfumu. Iye anagwada pamapazi a mfumuyo ndipo anachonderera kuti mfumu isinthe chiwembu chimene Hamani, mbadwa ya Agagi, anakonzera Ayuda.+ 4 Ndiyeno mfumu inaloza Esitere ndi ndodo yachifumu yagolide+ ndipo Esitere anadzuka nʼkuima pamaso pa mfumu. 5 Kenako Esitere ananena kuti: “Ngati mungavomereze mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima, komanso ngati inu mfumu mukuona kuti nʼzoyenera ndipo mukusangalala nane, palembedwe lamulo lofafaniza zimene zinalembedwa mʼmakalata amene munthu wachiwembu Hamani,+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ analemba pofuna kupha Ayuda amene ali mʼzigawo zanu zonse mfumu. 6 Ndidzapirira bwanji kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndipo ndidzapirira bwanji kuona abale anga akuphedwa?”
7 Choncho Mfumu Ahasiwero anauza Mfumukazi Esitere ndi Moredikayi Myuda kuti: “Nyumba ya Hamani ndaipereka kwa Esitere,+ ndipo Hamaniyo ndinalamula kuti apachikidwe pamtengo+ chifukwa anakonza chiwembu choti aphe Ayuda. 8 Ndiye inu lembani makalata mʼmalo mwa Ayuda. Mulembe mʼdzina la mfumu zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino ndipo mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu. Chifukwa nʼzosatheka kufafaniza lamulo limene lalembedwa mʼdzina la mfumu nʼkudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+
9 Choncho pa nthawiyi anaitana alembi a mfumu. Limeneli linali tsiku la 23 la mwezi wachitatu womwe ndi mwezi wa Sivani.* Iwo analemba zonse zimene Moredikayi analamula Ayuda kuti achite. Makalatawo analinso opita kwa masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi akalonga amʼzigawo zonse+ kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya, zigawo 127. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu akumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Nawonso Ayuda anawalembera mogwirizana ndi kalembedwe kawo ndiponso chilankhulo chawo.
10 Moredikayi analemba makalatawo mʼdzina la Mfumu Ahasiwero nʼkuwadinda ndi mphete yodindira ya mfumu.+ Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa anthu operekera makalata okwera pamahatchi. Iwo anapita pamahatchi aliwiro amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu. 11 Mʼmakalatawo mfumu inapereka chilolezo kwa Ayuda mʼmizinda yosiyanasiyana kuti asonkhane nʼcholinga choti adziteteze komanso aphe asilikali a gulu lililonse kapena chigawo chilichonse amene angawaukire, kuphatikizapo akazi ndi ana nʼkutenga zinthu zawo.+ 12 Zimenezi zinkayenera kuchitika mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku la 13 lomwelo la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 13 Zimene analemba mʼmakalatawo anazipereka kuti zikhale lamulo mʼzigawo zonse. Analengeza kwa anthu a mitundu yonse nʼcholinga choti Ayuda akonzekere kudzabwezera adani awo pa tsiku limeneli.+ 14 Anthu operekera makalatawo anapita mofulumira atakwera pamahatchi amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu ndipo anachita zimenezi chifukwa cha lamulo la mfumu. Lamuloli linaperekedwanso kunyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
15 Ndiyeno Moredikayi anachoka pamaso pa mfumu atavala chovala chachifumu chansalu yabuluu ndi yoyera. Analinso atavala chipewa chachikulu chachifumu chagolide ndiponso mkanjo wa nsalu yabwino kwambiri yaubweya wa nkhosa wapepo.+ Ndipo anthu amumzinda wa Susani* anafuula chifukwa chosangalala. 16 Ayuda anaona kuti imeneyi inali nkhani yabwino moti anayamba kusangalala ndi kukondwera ndipo anthu ankawalemekeza. 17 Mʼzigawo zonse ndiponso mʼmizinda yonse kumene lamulo la mfumu linafika, Ayuda ankasangalala, kukondwera ndiponso kuchita phwando komanso zikondwerero. Anthu ambiri amʼdzikomo anayamba kunena kuti ndi Ayuda+ chifukwa ankaopa kwambiri Ayudawo.