Genesis
28 Ndiyeno Isaki anaitana Yakobo nʼkumudalitsa ndipo anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+ 2 Upite ku Padani-aramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani+ mchimwene wa mayi ako. 3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+ 4 Adzakupatsa iwe ndi mbadwa* zako madalitso amene analonjeza Abulahamu,+ kuti dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli, limene Mulungu anapatsa Abulahamu, lidzakhale lako.”+
5 Choncho Isaki anatumiza Yakobo ndipo iye ananyamuka kupita ku Padani-aramu. Anapita kwa Labani mwana wa Betuele, wa Chiaramu.+ Labaniyo anali mchimwene wake wa Rabeka+ amene anali mayi ake a Yakobo ndi Esau.
6 Esau anaona kuti Isaki wadalitsa Yakobo ndiponso kuti wamʼtumiza ku Padani-aramu kukatenga mkazi kumeneko. Anaona kuti pomudalitsa anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.”+ 7 Anaonanso kuti Yakobo wamvera bambo ake ndi mayi ake ndipo wapita ku Padani-aramu.+ 8 Zitatero Esau anazindikira kuti Isaki bambo ake ankanyansidwa ndi ana aakazi a ku Kanani.+ 9 Choncho Esau anapita kwa Isimaeli* nʼkukatengako mkazi wina kuwonjezera pa akazi amene anali nawo. Mkaziyo dzina lake anali Mahalati ndipo anali mchemwali wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu.+
10 Yakobo anachoka ku Beere-seba nʼkupitiriza ulendo wake wopita ku Harana.+ 11 Atafika pamalo ena, anaganiza zogona pamenepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Choncho anatenga mwala umodzi pamalopo ndipo anautsamira nʼkugona.+ 12 Kenako anayamba kulota. Mʼmalotowo anaona masitepe* ochokera padziko lapansi mpaka kumwamba, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pamasitepewo.+ 13 Pamwamba pa masitepewo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:
“Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ 14 Mbadwa zako ndithu zidzachuluka ngati mchenga wapadziko lapansi+ ndipo ana ako adzafalikira kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera. Komanso kudzera mwa iwe ndi mwa mbadwa zako, mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa ndithu.+ 15 Ine ndili ndi iwe. Ndikuyangʼanira kulikonse kumene ungapite ndipo ndidzakubwezera kudziko lino.+ Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjeza.”+
16 Kenako Yakobo anadzuka nʼkunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo ano, koma ine sindinadziwe.” 17 Iye anachita mantha nʼkunenanso kuti: “Malo ano ndi oopsa! Ndithu malo ano ndi nyumba ya Mulungu,+ ndiponso ndi khomo lakumwamba.”+ 18 Choncho Yakobo anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutenga mwala umene anautsamira uja. Atatero anauimika monga mwala wachikumbutso ndipo anauthira mafuta pamwamba pake.+ 19 Kenako, malowo anawapatsa dzina lakuti Beteli.* Koma poyamba dzina la mzindawo linali Luzi.+
20 Yakobo analonjeza kuti: “Mulungu akapitiriza kukhala nane komanso kunditeteza pa ulendo wangawu, ndiponso akadzandipatsa chakudya ndi zovala, 21 komanso ndikadzabwerera mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga. 22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatse, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi.”