Genesis
27 Tsopano Isaki anakalamba moti maso ake anasiya kuona. Ndiyeno anaitana mwana wake wamkulu Esau+ nʼkumuuza kuti: “Mwana wanga!” Iye anayankha kuti: “Ine bambo!” 2 Isaki anapitiriza kuti: “Taona, ine tsopano ndakalamba. Tsiku lililonse ndikhoza kufa. 3 Choncho tenga zida zako pompano. Utenge uta ndi kachikwama kako koikamo mivi ndipo upite kutchire ukandisakire nyama.+ 4 Udzaikonze bwino ngati mmene ndimaikondera muja nʼkundibweretsera. Ndikufuna ndidye kenako ndikudalitse ndisanafe.”
5 Koma pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau, Rabeka ankamvetsera. Ndiyeno Esau anapita kutchire kuti akaphe nyama nʼkubwera nayo.+ 6 Tsopano Rabeka anauza mwana wake Yakobo+ kuti: “Ndamva bambo ako akuuza mkulu wako Esau kuti, 7 ‘Ukandiphere nyama nʼkuiphika bwino. Ndiye udzandipatse kuti ndidye, kenako ndidzakudalitse pamaso pa Yehova ndisanafe.’+ 8 Tsopano mwana wanga, mvetsera mosamala ndipo uchite zimene ndikuuze.+ 9 Pita kuli ziwetoko ukatengeko ana a mbuzi awiri onenepa bwino. Ndikufuna ndiwakonzere bambo ako chakudya chokoma kwambiri chimene amakonda chija. 10 Ndiye ukapereke kwa bambo ako akadye, kuti akudalitse asanamwalire.”
11 Yakobo anayankha Rabeka mayi ake kuti: “Koma mʼbale wanga Esau ndi munthu wacheya,*+ pamene ine ndili ndi khungu losalala. 12 Nanga bambo akakandikhudza?+ Ndithu andiona ngati ndikungofuna kuwapusitsa ndipo ndidzibweretsera matemberero, osati madalitso.” 13 Koma mayi akewo anamuuza kuti: “Matemberero amenewo abwere kwa ine mʼmalo mwa iwe mwana wanga. Ingochita zimene ndakuuzazi. Pita ukanditengere ana a mbuziwo.”+ 14 Choncho iye anakawatenga nʼkubwera nawo kwa mayi ake. Mayi akewo anaphika nyamayo mopatsa mudyo mmene bambo ake ankaikondera. 15 Zitatero, Rabeka anatenga zovala zabwino kwambiri za mwana wake wamkulu Esau, zimene anali nazo mʼnyumba nʼkuveka mwana wake wamngʼono, Yakobo.+ 16 Anamuvekanso zikopa za ana a mbuzi aja, mʼmanja mwake ndi pakhosi pake pamene panalibe cheya.+ 17 Kenako anapatsa mwana wake Yakobo chakudya chokoma chimene anakonzacho, limodzi ndi mkate umene anaphika.+
18 Ndiyeno Yakobo anapita kumene kunali bambo ake nʼkunena kuti: “Bambo!” Ndipo Isaki anayankha kuti: “Ine pano! Ndiwe ndani kodi mwana wanga?” 19 Yakobo anauza bambo akewo kuti: “Ndine Esau, mwana wanu woyamba.+ Ndachita zonse zimene munandiuza. Dzukani, khalani pansi mudye nyama imene ndakupherani, kuti mundidalitse.”+ 20 Atamva zimenezi Isaki anafunsa mwana wake kuti: “Koma mwana wanga, waipeza bwanji mofulumira chonchi?” Iye anayankha kuti: “Yehova Mulungu wanu ndi amene waikusira kwa ine.” 21 Koma Isaki anauza Yakobo kuti: “Tayandikira ndikukhudze mwana wanga. Ndikufuna ndidziwe ngati ndiwedi mwana wanga Esau kapena ayi.”+ 22 Choncho Yakobo anafika pafupi ndi bambo ake Isaki. Atamukhudza ananena kuti: “Mawu akumveka kuti ndi a Yakobo, koma manja akumveka kuti ndi a Esau.”+ 23 Iye sanamuzindikire, chifukwa manja ake anali acheya ngati manja a Esau mʼbale wake. Choncho anamudalitsa.+
24 Kenako anamufunsanso kuti: “Koma ndiwedi mwana wanga Esau?” Iye anayankha kuti: “Eya ndi ineyo.” 25 Ndiyeno Isaki anati: “Mwana wanga, ndipatsire nyama imene wandipherayo kuti ndidye, kenako ndikudalitsa.” Choncho anamupatsira ndipo anadya. Anamupatsiranso vinyo ndipo iye anamwa. 26 Kenako bambo akewo anamuuza kuti: “Ndiyandikire mwana wanga, undikise.”*+ 27 Choncho anamuyandikira nʼkumukisa, ndipo anamva kafungo ka zovala zake.+ Kenako anamudalitsa kuti:
“Eya, kafungo ka mwana wanga kakununkhira ngati fungo labwino la munda umene Yehova waudalitsa. 28 Mulungu woona akupatse mame akumwamba,+ ndi nthaka yachonde ya dziko lapansi.+ Achulukitsenso zokolola zako ndi vinyo wako watsopano.+ 29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire. Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+
30 Isaki atangomaliza kudalitsa Yakobo, komanso Yakoboyo atangochoka kumene kunali Isaki bambo ake, Esau mʼbale wake anafika kuchokera kokasaka nyama.+ 31 Iyenso anakonzera bambo ake nyama ija mopatsa mudyo. Kenako anapita nayo kwa bambo ake nʼkuwauza kuti: “Bambo, dzukani mudye nyama imene ine mwana wanu ndakupherani, kuti mundidalitse.” 32 Ndiyeno Isaki, bambo ake, anati: “Nanga iwenso ndiwe ndani?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wanu, mwana wanu woyamba Esau.”+ 33 Pamenepo Isaki anayamba kunjenjemera kwambiri, ndipo anati: “Nanga amene wandiphera nyama nʼkundibweretsera uja ndi ndani? Ine ndadya kale iwe usanabwere, moti ndamudalitsa. Ndipo adzalandiradi madalitso amenewa!”
34 Atamva mawu a bambo akewa, Esau anayamba kulira ndi kukuwa mogonthetsa mʼkhutu, komanso mowawidwa mtima kwambiri. Iye anachonderera bambo ake kuti: “Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+ 35 Koma Isaki anamuuza kuti: “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo kuti adzalandire madalitso amene anali ako.” 36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano nʼkachiwiri akundichenjerera amene uja! Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo?*+ Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye ananenanso kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?” 37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsa abale ake onse kuti akhale atumiki ake. Komanso ndamudalitsa kuti akhale ndi zokolola zambiri ndiponso vinyo watsopano wambiri.+ Nanga chatsalanso nʼchiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”
38 Esau anafunsa bambo ake kuti: “Bambo, ngakhale dalitso limodzi silinatsaleko? Bambo ndidalitseni, inenso ndidalitseni chonde!” Atatero Esau analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.+ 39 Koma Isaki bambo ake anamuuza kuti:
“Taona, udzakhala kutali ndi nthaka yachonde, komanso kutali ndi mame akumwamba.+ 40 Pa nthawi yonse ya moyo wako uzidzadalira lupanga+ ndipo udzatumikira mʼbale wako.+ Koma ukadzatopa ndi goli lake, udzalithyola ndi kulichotsa mʼkhosi mwako.”+
41 Choncho, Esau anayamba kudana ndi Yakobo chifukwa cha madalitso amene bambo ake anamupatsa.+ Mumtima mwake ankanena kuti: “Masiku olira maliro a bambo anga ali pafupi.+ Pambuyo pake, ndidzamupha mʼbale wanga Yakobo.” 42 Rabeka atauzidwa zimene mwana wake wamkulu Esau ananena, nthawi yomweyo anaitanitsa mwana wake wamngʼono Yakobo nʼkumuuza kuti: “Mʼbale wako Esau akufuna akuphe pobwezera zimene unamuchitira.* 43 Choncho uchite zimene ndikuuze mwana wanga. Nyamuka, thawira kwa mchimwene wanga Labani, ku Harana.+ 44 Ukakhale naye kwa kanthawi, mpaka ukali wa mʼbale wako utatha. 45 Ukakhale kumeneko mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utaphwa komanso mpaka ataiwala zimene unamuchitira. Kenako ndidzatuma anthu kuti adzakutenge. Nanga nditaye ana awiri tsiku limodzi?”
46 Izi zitachitika, Rabeka ankauza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo chifukwa cha akazi a Chihetiwa.+ Ngati Yakobo nayenso angatenge mkazi pakati pa akazi a Chiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+