Miyambo
2 Anthu okhala mʼdziko akamachimwa,* dzikolo limasintha akalonga pafupipafupi,+
Koma kalonga akamathandizidwa ndi munthu wozindikira komanso wodziwa zinthu, amakhala nthawi yaitali.+
3 Munthu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+
Ali ngati mvula imene imakokolola chakudya chonse.
4 Anthu amene asiya chilamulo amatamanda munthu woipa,
Koma amene amasunga chilamulo amakwiyira anthu amene asiya chilamulowo.+
6 Munthu wosauka amene amachita zinthu mokhulupirika,
Ali bwino kuposa munthu wolemera amene amachita zachinyengo.+
7 Mwana womvetsa zinthu amatsatira malamulo,
Koma amene amakonda kucheza ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+
8 Munthu amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja+ ndi katapira,
Chuma chakecho chidzapita kwa munthu amene amakomera mtima anthu osauka.+
10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima kuti azichita zinthu zoipa, adzagwera mʼdzenje lake lomwe,+
Koma anthu osalakwa adzalandira zinthu zabwino.+
11 Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru,+
Koma munthu wosauka amene ndi wozindikira amamufufuza nʼkudziwa zoona zake.+
12 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, anthu amasangalala kwambiri,*
Koma anthu oipa akayamba kulamulira, anthu amabisala.+
13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+
Koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.+
14 Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake,*
Koma amene amaumitsa mtima wake adzakumana ndi tsoka.+
15 Mtsogoleri woipa amene akulamulira anthu onyozeka+
Ali ngati mkango wobangula komanso chimbalangondo chimene chakonzekera kugwira nyama.
16 Mtsogoleri wosazindikira amagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika,+
Koma amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo adzatalikitsa moyo wake.+
17 Munthu amene ali ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu, adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.*+
Aliyense asamuthandize.
18 Amene amayenda mosalakwitsa kanthu adzapulumutsidwa,+
Koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mwadzidzidzi.+
19 Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chambiri,
Koma amene akutanganidwa ndi zinthu zopanda phindu adzakhala pa umphawi waukulu.+
20 Munthu wokhulupirika adzalandira madalitso ambiri,+
Koma amene akufuna kulemera mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
Koma munthu akhoza kuchita zinthu zolakwika pofuna kupeza kachidutswa ka chakudya.
22 Munthu wadyera amayesetsa kuti apeze chuma,
Osadziwa kuti umphawi udzamugwira.
23 Amene amadzudzula munthu,+ pambuyo pake adzakondedwa kwambiri+
Kuposa munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamaso.
24 Wobera bambo ake ndi mayi ake nʼkumanena kuti, “Si kulakwa,”+
Amakhala ngati mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+
25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,
Koma aliyense amene amadalira Yehova zinthu zidzamuyendera bwino.*+
26 Aliyense amene amadalira mtima wake ndi wopusa,+
Koma amene amachita zinthu mwanzeru adzapulumuka.+