Miyambo
26 Sinowo sayenera kugwa mʼchilimwe ndiponso mvula siyenera kugwa pa nthawi yokolola,
Chimodzimodzinso munthu wopusa, iye sayenera kulemekezedwa.+
2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira ndiponso namzeze amakhala ndi chifukwa choulukira.
Nalonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.*
3 Chikwapu nʼchokwapulira hatchi, zingwe nʼzomangira pakamwa pa bulu,+
Ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+
4 Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake,
Kuti iweyo usafanane naye.
6 Munthu amene amasiya ntchito yake mʼmanja mwa munthu wopusa
Ali ngati munthu amene wapundula mapazi ake nʼkudzivulaza yekha.*
7 Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusa+
Uli ngati miyendo* ya munthu wolumala amene akuyenda motsimphina.
9 Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusa
Uli ngati chitsamba chaminga chimene chili mʼmanja mwa munthu woledzera.
10 Wolemba ntchito munthu wopusa kapena anthu ongodutsa mʼnjira,
Ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa mwachisawawa nʼkuvulaza anthu.
12 Kodi waona munthu amene amaganiza kuti ndi wanzeru?+
Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.
14 Mofanana ndi chitseko chimene chimangozungulira pamene anachimangirira,
Waulesi nayenso amangotembenukatembenuka pabedi pake.+
15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,
Koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa chotopa kwambiri.+
16 Munthu waulesi amaganiza kuti ndi wanzeru kwambiri
Kuposa anthu 7 amene ayankha zanzeru.
17 Munthu wongodutsa amene amakwiya chifukwa cha mkangano* womwe si wake,+
Ali ngati munthu wogwira makutu a galu.
18 Munthu wamisala amene akuponya mivi yoyaka moto komanso mivi yakupha,
19 Akufanana ndi munthu amene amapusitsa mnzake nʼkunena kuti, “Inetu ndimangochita zocheza.”+
20 Ngati palibe nkhuni moto umazima,
Ndipo ngati palibe munthu wonenera anzake zoipa, mikangano imatha.+
21 Makala komanso nkhuni zimachititsa kuti moto uziyaka,
Mofanana ndi zimenezi munthu wokonda kuyambana ndi anthu amakolezera mikangano.+
24 Munthu amene amadana ndi ena amabisa chidanicho ndi milomo yake,
Koma mumtima mwake mumakhala chinyengo.
25 Ngakhale azilankhula mawu okoma, usamukhulupirire,
Chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.*
26 Ngakhale chidani chake chitaphimbika ndi chinyengo,
Zoipa zake zidzaululika mumpingo.