1 Samueli
4 Samueli analankhula ndi Aisiraeli onse.
Kenako Aisiraeli anapita kukamenyana ndi Afilisiti ndipo anamanga msasa pafupi ndi Ebenezeri. Koma Afilisiti anamanga msasa ku Afeki. 2 Afilisitiwo anayalana atakonzekera kumenyana ndi Aisiraeli. Nkhondoyo sinawayendere bwino Aisiraeli, moti anagonjetsedwa ndi Afilisiti. Pa nkhondoyi Afilisiti anapha asilikali a Chiisiraeli pafupifupi 4,000. 3 Anthuwo atabwerera kumsasa, akulu a Isiraeli ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani lero Yehova walola kuti Afilisiti atigonjetse?*+ Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova ku Silo+ tizikhala nalo, kuti litipulumutse mʼmanja mwa adani athu.” 4 Choncho anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinihasi,+ analinso komweko limodzi ndi likasa la pangano la Mulungu woona.
5 Likasa la pangano la Yehova litangofika mumsasa, Aisiraeli onse anafuula mosangalala, moti dziko linagwedezeka. 6 Afilisiti atamva phokosolo anafunsa kuti: “Kodi phokosoli, lomwe likumveka mumsasa wa Aheberi ndi la chiyani?” Kenako anamva kuti Likasa la Yehova labwera mumsasawo. 7 Afilisitiwo anachita mantha ndipo anati: “Mulungu wafika mumsasa wawo.”+ Ndiyeno anati: “Tsoka latigwera, chifukwa zoterezi sizinayambe zachitikapo. 8 Apa ndiye zativuta ndithu. Ndi ndani atipulumutse mʼmanja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anapha Aiguputo ambirimbiri mʼchipululu.+ 9 Limbani mtima ndi kuchita zinthu mwachamuna inu Afilisiti, kuti Aheberi asatilamulire ngati mmene ife tinachitira ndi iwowo.+ Chitani zinthu mwachamuna ndi kumenya nkhondo.” 10 Choncho Afilisiti anamenyadi nkhondo ndipo Aisiraeli anagonja+ moti aliyense anathawira kutenti yake. Aisiraeli amene anaphedwa anali ambiri. Panaphedwa asilikali oyenda pansi okwana 30,000. 11 Komanso Likasa la Mulungu linalandidwa, ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana a Eli, anaphedwa.+
12 Tsiku limenelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathamanga kuchoka kumalo ankhondowo kukafika ku Silo, atangʼamba zovala zake ndiponso atadzithira dothi kumutu.+ 13 Atafika, anapeza Eli atakhala pampando mʼmbali mwa msewu, maso ali kunjira, chifukwa ankachita mantha kwambiri akaganizira za Likasa la Mulungu woona.+ Munthuyo analowa mumzindawo kukanena za nkhondoyo, ndipo anthu onse amumzindawo anayamba kulira. 14 Eli atamva kulira kwa anthuwo, anafunsa kuti: “Kodi anthuwo akulira chiyani?” Kenako mwamuna uja anathamanga kukauza Eli nkhaniyi. 15 (Eli anali ndi zaka 98, ndipo maso ake ankaoneka ngati akuyangʼana koma sankaona chilichonse.)+ 16 Munthu uja anauza Eli kuti: “Ine ndikuchokera kunkhondo ndipo ndachokako chothawa lero lomwe.” Choncho Eli anamufunsa kuti: “Kwachitika zotani mwana wanga?” 17 Munthu amene anabwera ndi uthengayo anati: “Aisiraeli athawa Afilisiti, ndipo agonjetsedwa koopsa.+ Ana anunso awiri, Hofeni ndi Pinihasi, aphedwa.+ Komanso Likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+
18 Munthuyo atangotchula za Likasa la Mulungu woona, Eli, yemwe anali pageti anagwa chagada kuchoka pampando. Khosi lake linathyoka ndipo anafa chifukwa anali wokalamba ndiponso wonenepa kwambiri. Eli anaweruza Isiraeli kwa zaka 40. 19 Mpongozi wake, mkazi wa Pinihasi, anali woyembekezera ndipo anali pafupi kubereka. Atamva kuti Likasa la Mulungu woona lalandidwa komanso apongozi ake ndi mwamuna wake afa, matenda anamuyamba mwadzidzidzi ndipo anabereka mwana. 20 Mkaziyu atatsala pangʼono kumwalira, amayi amene anaima pambali pake anamuuza kuti: “Usaope, wabereka mwana wamwamuna.” Koma iye sanayankhe komanso sanachite chilichonse. 21 Iye anapatsa mwanayo dzina lakuti Ikabodi*+ nʼkunena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.”+ Ananena zimenezi chifukwa cha Likasa la Mulungu woona limene linali litalandidwa ndiponso chifukwa cha zimene zinachitikira apongozi ake ndi mwamuna wake.+ 22 Ananena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina, chifukwa Likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+