1 Samueli
12 Pomaliza, Samueli anauza Aisiraeli onse kuti: “Ndachita zonse zimene* munandiuza, ndipo ndakusankhirani mfumu yoti izikulamulirani.+ 2 Tsopano mfumu ija ndi imeneyi, yomwe ikukutsogoleraniyi.*+ Koma ine ndakalamba ndipo tsitsi langa lachita imvi. Ana anga aamuna ndi awa muli nawowa+ ndipo ine ndakutsogolerani kuyambira ndili kamnyamata mpaka lero.+ 3 Ine ndaima pano. Mupereke umboni pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa wake:+ Kodi alipo amene ndinamʼtengera ngʼombe kapena bulu wake?+ Nanga alipo amene ndinamʼchitirapo zachinyengo kapena kumʼpondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisachite chilungamo?+ Ngati ndinachitapo zimenezi, ndine wokonzeka kukubwezerani.”+ 4 Iwo anayankha kuti: “Simunatichitire zachinyengo, simunatipondereze komanso simunalandire chilichonse kwa ife.” 5 Atatero, iye anawayankha kuti: “Yehova ndi mboni yokutsutsani ndipo nayenso wodzozedwa wake ndi mboni lero kuti simunandipeze ndi mlandu uliwonse.”* Iwo anati: “Inde, iye ndi mboni.”
6 Choncho Samueli anauza anthuwo kuti: “Yehova, amene anagwiritsa ntchito Mose ndi Aroni, amenenso anatulutsa makolo anu mʼdziko la Iguputo,+ ndi mboni. 7 Tsopano bwerani pafupi kuti ndikuweruzeni pamaso pa Yehova mogwirizana ndi ntchito zonse zolungama zimene Yehova wachitira inuyo komanso makolo anu.
8 Yakobo atangofika ku Iguputo,+ makolo anu nʼkuyamba kupempha Yehova kuti awathandize,+ Yehova anatumiza Mose+ ndi Aroni kuti atsogolere makolo anu pochoka ku Iguputo kuti azikhala mʼdzikoli.+ 9 Koma iwo anaiwala Yehova Mulungu wawo ndipo iye anawapereka*+ kwa Sisera+ mkulu wa asilikali a Hazori, komanso kwa Afilisiti+ ndi kwa mfumu ya Mowabu,+ ndipo onsewa anamenyana nawo. 10 Choncho analirira Yehova kuti awathandize+ ndipo anati, ‘Tachimwa,+ chifukwa tasiya Yehova nʼkuyamba kutumikira Abaala+ ndi zifaniziro za Asitoreti.+ Tsopano tipulumutseni kwa adani athu kuti tizikutumikirani.’ 11 Kenako Yehova anatumiza Yerubaala,+ Bedani, Yefita+ ndi Samueli+ ndipo anakupulumutsani kwa adani anu onse okuzungulirani kuti mukhale pa mtendere.+ 12 Mutaona kuti Nahasi,+ mfumu ya Aamoni, wabwera kudzamenyana nanu, munayamba kundiuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu basi,’+ ngakhale kuti Mfumu yanu ndi Yehova Mulungu wanu.+ 13 Tsopano mfumu imene mwasankha ndi imeneyi, mfumu imene munapempha. Yehova wakusankhirani mfumu yoti izikulamulirani.+ 14 Ngati mudzaopa Yehova,+ kumutumikira+ ndiponso kumumvera,+ ngati simudzasiya malamulo a Yehova komanso ngati inuyo ndi mfumu yanu mudzatsatira Yehova Mulungu wanu, zili bwino. 15 Koma mukasiya kumvera Yehova ndiponso kutsatira malamulo a Yehova, dzanja la Yehova lidzakulangani inuyo komanso abambo anu.+ 16 Tsopano bwerani apa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova achite. 17 Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Ndipemphera kwa Yehova kuti abweretse mabingu ndi mvula. Zikatero mudziwa ndiponso kuzindikira kuti mwachita zoipa kwambiri pamaso pa Yehova popempha kuti mukhale ndi mfumu.”+
18 Choncho Samueli anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anabweretsa mabingu ndi mvula tsiku limenelo. Anthu onse anachita mantha kwambiri ndi Yehova ndiponso Samueli. 19 Zitatero, anthu onse anauza Samueli kuti: “Tipempherereni ife atumiki anu kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa sitikufuna kufa. Tawonjezera choipa china pa machimo athu popempha kuti tikhale ndi mfumu.”
20 Koma Samueli anawauza kuti: “Musachite mantha. Nʼzoona kuti mwachita zoipa zonsezi. Koma ngakhale zili choncho, musasiye kutsatira Yehova.+ Muzitumikira Yehova ndi mtima wanu wonse.+ 21 Musapatuke nʼkuyamba kutsatira milungu yopanda pake*+ yomwe ndi yosathandiza+ komanso singakupulumutseni chifukwa ndi yopanda pake.* 22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya anthu ake,+ popeza Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+ 23 Komanso nʼzosatheka kuti ineyo ndichimwire Yehova posiya kukupemphererani. Ndipo ndipitiriza kukulangizani za njira yabwino ndi yolondola. 24 Koma muziopa Yehova+ nʼkumamutumikira mokhulupirika* komanso ndi mtima wanu wonse. Kumbukirani zinthu zazikulu zimene wakuchitirani.+ 25 Koma mukamachita zoipa mopanda manyazi, mudzasesedwa,+ inuyo pamodzi ndi mfumu yanu.”+