Ekisodo
6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awalole kuchoka, ndipo dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awathamangitse mʼdziko lake.”+
2 Kenako Mulungu anauza Mose kuti: “Ine ndine Yehova. 3 Ndinkaonekera kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.+ 4 Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene ankakhalamo ngati alendo.+ 5 Tsopano ine ndamva kubuula kwa Aisiraeli, amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+
6 Choncho uwauze Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndidzakupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani ndipo ndidzakulanditsani kuti musakhalenso akapolo awo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula* komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+ 7 Choncho ndidzakutengani kuti mukhale anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani. 8 Ine ndidzakulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira* kuti ndidzalipereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+
9 Kenako Mose anapereka uthenga umenewu kwa Aisiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11 “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo, ukamuuze kuti alole Aisiraeli kutuluka mʼdziko lake.” 12 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu Aisiraeli sanandimvere,+ ndiye Farao akandimvera bwanji? Pajatu ndimalankhula movutikira.”*+ 13 Koma Yehova anauzanso Mose ndi Aroni malamulo oti apereke kwa Aisiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse Aisiraeli mʼdziko la Iguputo.
14 Atsogoleri a mafuko a Aisiraeli ndi awa: Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Rubeni.
15 Ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wa Chikanani.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Simiyoni.
16 Mayina a ana aamuna a Levi,+ mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo ndi awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137.
17 Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi, mogwirizana ndi mabanja awo.+
18 Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.
19 Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi.
Amenewa anali mabanja a Alevi mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+
20 Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mchemwali wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anamʼberekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137.
21 Ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri.
22 Ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana+ ndi Sitiri.
23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mchemwali wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anamʼberekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+
24 Ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa anali mabanja a Kora.+
25 Ndipo Eleazara+ mwana wa Aroni, anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anamʼberekera Pinihasi.+
Amenewa ndi atsogoleri a mabanja amʼfuko la Levi, mogwirizana ndi mabanja awo.+
26 Umenewu ndi mzere wobadwira wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti: “Tulutsani Aisiraeli mʼdziko la Iguputo mʼmagulumagulu.”*+ 27 Anali Mose ndi Aroni+ amene analankhula ndi Farao mfumu ya Iguputo kuti atulutse Aisiraeli mu Iguputo.
28 Pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose mʼdziko la Iguputo, 29 Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova. Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.” 30 Ndiye Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira,* ndiye Farao akandimvera bwanji?”+