Ekisodo
14 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti abwerere nʼkumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, koma moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.+ Mumange msasa wanu pafupi ndi nyanja, patsogolo pa Baala-zefoni. 3 Kenako Farao adzanena kuti, ‘Aisiraeli asokonezeka ndipo akungoyendayenda mʼdziko lathu. Iwo asochera mʼchipululu.’ 4 Ine ndidzalola kuti Farao aumitse mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao ndi gulu lake lonse lankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo.
5 Kenako mfumu ya Iguputo inauzidwa kuti Aisiraeli athawa. Nthawi yomweyo mtima wa Farao ndi atumiki ake unasinthanso ataganizira za Aisiraeli,+ moti anati: “Nʼchifukwa chiyani tachita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani talola kuti akapolo athu Aisiraeli achoke?” 6 Choncho anakonzekeretsa magaleta* ake ankhondo nʼkutenganso asilikali ake.+ 7 Anatenga magaleta ake abwino kwambiri 600 ndi magaleta ena onse a Iguputo, ndipo mʼmagaleta onsewo munakwera asilikali. 8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake, ndipo anathamangira Aisiraeli pamene iwo ankatuluka mʼdzikomo molimba mtima.*+ 9 Aiguputo ankawathamangira,+ ndipo magaleta onse a Farao, asilikali apamahatchi ndi gulu lake lankhondo anawayandikira. Aisiraeliwo anali atamanga msasa mʼmphepete mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.
10 Farao atafika pafupi, Aisiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Choncho Aisiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+ 11 Iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere mʼchipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi? Nʼchifukwa chiyani watitulutsa mu Iguputo? 12 Kodi zimene tinkakuuza ku Iguputo kuja si zimenezi? Kodi sitinakuuze kuti, ‘Tisiye tizitumikira Aiguputoʼ? Chifukwa ndi bwino kuti tizitumikira Aiguputo kusiyana nʼkuti tifere mʼchipululu.”+ 13 Atatero Mose anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Limbani mtima ndipo muona mmene Yehova akupulumutsireni lero.+ Chifukwa Aiguputo amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso mpaka kalekale.+ 14 Yehova adzakumenyerani nkhondo,+ ndipo inu mudzangokhala phee, osachita chilichonse.”
15 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundidandaulira? Auze Aisiraeli kuti anyamuke. 16 Ndipo iweyo, utenge ndodo yako nʼkutambasula dzanja lako kuloza panyanja kuti nyanjayo igawanike. Ukatero Aisiraeli adutsa pakati panyanja, panthaka youma. 17 Koma ine ndilola kuti Aiguputo aumitse mitima yawo, moti atsatira Aisiraeli panyanjapo. Ndichita zimenezi kuti ndilemekeze dzina langa pogonjetsa Farao, gulu lake lonse lankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+ 18 Ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.”+
19 Ndiyeno mngelo wa Mulungu woona+ amene ankayenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka nʼkupita kumbuyo kwawo. Ndipo chipilala cha mtambo chija chinachoka kutsogolo nʼkukaima kumbuyo kwawo.+ 20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unkachititsa mdima, ndipo mbali ina unkawaunikira usiku.+ Choncho gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.
21 Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvu yakumʼmawa igawe nyanjayo usiku wonse nʼkuumitsa pansi pake.+ Choncho madziwo anagawanika.+ 22 Zitatero Aisiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma,+ madziwo ataima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 23 Ndiyeno Aiguputo anawathamangira, ndipo mahatchi onse a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi anayamba kuwalondola pakati pa nyanja.+ 24 Ndiyeno chakumʼbandakucha,* Yehova ali mʼchipilala cha mtambo ndi cha moto chija,+ anayangʼana gulu la Aiguputo ndipo anachititsa kuti Aiguputowo asokonezeke. 25 Iye ankagulula mawilo a magaleta awo moti ankawayendetsa movutikira. Ndipo Aiguputo ankanena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+
26 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza panyanja kuti madzi abwerere nʼkumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.” 27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja, ndipo kutatsala pangʼono kucha nyanjayo inayamba kubwerera mʼmalo mwake. Pamene Aiguputo ankathawa kuti madziwo asawapeze, Yehova anakankhira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+ 28 Madzi amene anabwererawo anamiza magaleta ankhondo, asilikali apamahatchi ndi gulu lonse lankhondo la Farao, amene analondola Aisiraeli mʼnyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+
29 Koma Aisiraeli anayenda panthaka youma pakati pa nyanja,+ ndipo madzi anaima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 30 Choncho pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa Aisiraeli mʼmanja mwa Aiguputo,+ ndipo Aisiraeli anaona Aiguputo atafa mʼmphepete mwa nyanja. 31 Aisiraeli anaonanso mphamvu* zazikulu zimene Yehova anagwiritsa ntchito pogonjetsa Aiguputo. Ndipo Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.+