Ekisodo
24 Kenako Mulungu anauza Mose kuti: “Kwera mʼphiri upite kwa Yehova, iweyo, Aroni, Nadabu, Abihu+ ndi akulu 70 a Isiraeli, ndipo mukagwade chapatali. 2 Mose yekha akayandikire kwa Yehova, koma enawo asakayandikire. Anthu ena onse asakwere mʼphiri.”+
3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu nʼkuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Atatero anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+ 4 Choncho Mose analemba mawu onse a Yehova.+ Ndiyeno anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkukamanga guwa lansembe ndi zipilala 12 zoimira mafuko 12 a Isiraeli, mʼmunsi mwa phiri. 5 Kenako anatuma Aisiraeli achinyamata ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza komanso anapereka ngʼombe kuti zikhale nsembe zamgwirizano+ zoperekedwa kwa Yehova. 6 Ndiyeno Mose anatenga hafu ya magazi nʼkuwaika mʼmbale zolowa, ndipo hafu inayo anawaza paguwa lansembe. 7 Kenako anatenga buku la pangano nʼkuwerengera anthuwo mokweza.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+ 8 Choncho Mose anatenga magaziwo nʼkuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapangana nanu mogwirizana ndi mawu onsewa.”+
9 Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera mʼphirimo, 10 ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake pankaoneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, yoyera ngati kumwamba.+ 11 Mulungu sanawononge atsogoleri a Aisiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona ndipo anadya ndi kumwa.
12 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kwera mʼphiri muno ufike kwa ine ndipo ukhalebe momʼmuno. Ndikupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+ 13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka,+ ndipo Mose anakwera mʼphiri la Mulungu woona.+ 14 Koma Mose anauza akuluwo kuti: “Tidikireni pompano mpaka titabwerako.+ Muli ndi Aroni ndi Hura,+ ndiye aliyense amene ali ndi mlandu wofuna kuweruzidwa azipita kwa iwowa.”+ 15 Kenako Mose anakwera mʼphirimo, mtambo utakuta phirilo.+
16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakuta phirilo kwa masiku 6. Pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo. 17 Kwa Aisiraeli amene ankaona zimenezi, ulemerero wa Yehova unkaoneka ngati moto wolilima pamwamba pa phiri. 18 Kenako Mose analowa mumtambomo nʼkukwera mʼphirimo.+ Mose anakhala mmenemo masiku 40, masana ndi usiku.+