Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto
13 Aka nʼkachitatu tsopano kukonza ulendo wobwera kwanuko. “Muzitsimikizira nkhani iliyonse mutamva umboni* wochokera kwa mboni ziwiri kapena zitatu.”+ 2 Ngakhale kuti sindili kumeneko zili ngati ndili nanu limodzi kachiwiri. Ndipo ndikuchenjezeratu anthu amene anachimwa komanso ena onse, kuti ndikangobweranso kumeneko sindidzawalekerera. 3 Ndikutero chifukwa mukufuna umboni wotsimikizira kuti Khristu, yemwe si wofooka kwa inu koma ndi wamphamvu, akulankhuladi kudzera mwa ine. 4 Iye anaphedwa pamtengo chifukwa cha kufooka, koma ali ndi moyo chifukwa cha mphamvu ya Mulungu.+ Nʼzoona kuti ifenso ndife ofooka limodzi naye, koma tidzakhala naye limodzi+ chifukwa cha mphamvu ya Mulungu imene ikugwira ntchito mwa inu.+
5 Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.+ Kodi simukudziwa kuti ndinu ogwirizana ndi Yesu Khristu? Muyenera kudziwa zimenezi, kupatulapo ngati muli osavomerezeka. 6 Ndikukhulupirira kuti mudzazindikira kuti ndife ovomerezeka.
7 Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musachite cholakwa chilichonse. Cholinga chathu si choti tioneke kuti ndife ovomerezeka, koma kuti inuyo muzichita zabwino, ngakhale ifeyo titaoneka ngati osavomerezeka. 8 Chifukwa sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma zogwirizana ndi choonadi zokhazokha. 9 Timasangalala nthawi iliyonse imene ife tili ofooka inu nʼkukhala amphamvu. Ndipo chimene tikupempherera nʼchakuti musinthe zinthu zimene mukuyenera kusintha. 10 Nʼchifukwa chake ndikulemba zinthu zimenezi ndili kuno, kuti ndikadzabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwamphamvu, chifukwa Ambuye anandipatsa ulamulirowu+ kuti ndizikulimbikitsani, osati kukufooketsani.
11 Pomaliza abale, pitirizani kusangalala, kusintha maganizo, kulimbikitsidwa,+ kukhala ndi maganizo ogwirizana+ ndiponso kukhala mwamtendere.+ Mukatero, Mulungu amene ndi wachikondi komanso wamtendere+ adzakhala nanu. 12 Mupatsane moni mwachikondi. 13 Oyera onse akukupatsani moni.
14 Nonsenu mukhale ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu, chikondi cha Mulungu komanso madalitso a mzimu woyera.