Mmene Mungadziŵire ndi Kuthetsera Chofooka Chilichonse Chauzimu
Malinga ndi nthanthi ina Yachigiriki, Achilles ndiye anali msilikali wolimba mtima koposa mwa asilikali achigiriki m’Nkhondo ya Trojan, nkhondo yomenyana ndi mzinda wa Troy. Nthanoyo imati pamene Achilles anali wakhanda, amayi ake anam’miza m’madzi m’Mtsinje wa Styx, chotero anam’panga kukhala wosavulazika kusiyapo pamene amayi ake anam’gwira—pachitende. Pamenepo mpamene muvi woponyedwa ndi Paris, mwana wa Mfumu Priam ya mzinda wa Troy, unalasa ndi kupha Achilles.
Akristu ndi asilikali a Kristu, amene ali pankhondo yauzimu. (2 Timoteo 2:3) Paulo anafotokoza kuti: “Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m’zakumwamba.” Inde, adani athu si ena koma Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda.—Aefeso 6:12.
Mosakayikira, chikhala kuti sitikuthandizidwa ndi Yehova Mulungu, amene wanenedwa kukhala “wankhondo,” bwenzi tikugonja m’nkhondo imeneyi. (Eksodo 15:3) Kuti tidziteteze kwa adani athu aukaliwo, tapatsidwa zovala zauzimu za nkhondo. Ndiye chifukwa chake mtumwiyo anatilimbikitsa kuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”—Aefeso 6:11.
Ndithudi, zida zimene Yehova Mulungu watipatsa ndizo zabwino kwambiri, zotha kulaka chiukiro chilichonse chauzimu. Mutangoona mpambo umene Paulo anapereka: cha m’chiuno cha choonadi, cha pachifuŵa cha chilungamo, nsapato za uthenga wabwino, chikopa chachikulu cha chikhulupiriro, chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la mzimu. Kodi munthu angafunenso zida zabwino zoposa izi? Atavala zida zimenezi, msilikali wachikristu amakhala ndi mpata waukulu wopambana m’nkhondoyo, ngakhale adani ake atakhala oopsa motani.—Aefeso 6:13-17.
Ngakhale kuti zida zauzimu zochokera kwa Yehova ndizo zabwino kwambiri ndipo zimatiteteza, sitiyenera kuziona mopepuka. Pokumbukira Achilles amene akuti anali wosavulazika, kodi zingatheke kuti ifenso tingakhale ndi mbali ina yofooka, chitende cha Achilles chauzimu? Zimenezo zingakhale zakupha zinthu zitatigwera mwadzidzidzi.
Fufuzani Zida Zanu Zauzimu
Yemwe anapata mendulo ya golidi kaŵiri konse pa mpikisano wa Olympic m’maseŵero a ice skating, amene anaoneka kuti anali wathanzi labwino kwambiri, anakomoka mosayembekezereka ndi kumwalira pokonzekera mpikisano. Posapita nthaŵi nkhani ina yopangitsa munthu kuganiza mozama inalembedwa mu The New York Times niiti: “Theka la Aamereka 600,000 amene amadwala nthenda ya mtima chaka chilichonse sasonyeza zizindikiro za nthendayi.” Ndithudi, sitingadziŵe mmene thanzi lathu lilili mwa kungoona mmene tikumvera.
Ndi mmenenso thanzi lathu lauzimu lakhalira. Uphungu wa Baibulo ukuti: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:12) Ngakhale kuti zovala zathu zauzimu za nkhondo ndizo zabwino kwambiri, pangakhalebe zofooka. Zili choncho chifukwa chakuti timabadwira mu uchimo, ndipo uchimo wathuwo ndi kupanda kwathu ungwiro zingagonjetse mosavuta chosankha chathu cha kuchita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 51:5) Ngakhale titakhala ndi zolinga zabwino, mtima wathu wonyenga ungatinyenge mwa kupeka zifukwa zooneka ngati zabwino, kuti tinyalanyaze zofooka zathu ndi kudzinyenga mwa kuona ngati kuti zonse zili bwino.—Yeremiya 17:9; Aroma 7:21-23.
Ndiponso, tikukhala m’dziko mmene anthu amangosokoneza pakati pa choipa ndi chabwino. Chinthu chimakhala choipa kapena chabwino malinga ndi mmene munthuyo akuchionera. Malingaliro ameneŵa amachirikizidwa posatsa malonda, m’zosangulutsa zotchuka, ndi m’njira zofalitsira nkhani. Mosakayikira, ngati sitisamala, ifenso tingayambe kukhala ndi malingaliro amenewo, ndipo zovala zathu zauzimu za nkhondo zingayambe kuchepa mphamvu.
M’malo mogwera mumkhalidwe woopsa ngati umenewu, tiyenera kumvera uphungu wa Baibulo wakuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Tikatero, tidzatha kuona zofooka zilizonse zimene zingakhale zitayamba ndi kuchita zofunikira kuti tizithetse adani athu asanazione ndi kutiukira. Koma kodi kudziyesa kumeneku timakuchita motani? Kodi ndi zizindikiro zina zotani zimene tiyenera kufunafuna podziyesa tokha?
Kudziŵa Zizindikiro Zake
Chizindikiro chimodzi chofala chimene chingasonyeze kufooka kwauzimu ndicho kusoŵa changu cha phunziro laumwini. Ena amaona kuti ayenera kumaŵerenga kwambiri, koma amalepherabe kutero. M’moyo wamakono wotangwanitsawu, kuloŵa mumkhalidwe woipa umenewu n’kosavuta. Komabe, choipa kwambiri n’chakuti anthu nthaŵi zambiri amadzikhululukira kuti zinthu sizili zoipa kwenikweni, popeza amaŵerenga zofalitsa zofotokoza Baibulo nthaŵi zonse pamene angathe ndipo amapezekabe pamisonkhano ina yachikristu.
Malingaliro amenewo n’kudzinyenga chabe. Zili ngati munthu amene amaganiza kuti n’ngwotangwanitsidwa kwambiri moti sangakhale pansi bwinobwino ndi kudya chakudya, choncho amangodya mwa apa ndi apo ali kalikiliki ndi zochita zina. Ngakhale kuti sangafe ndi njala, angayambe kumadwaladwala posapita nthaŵi kaya nthaŵi itapitapo ndithu. Mofananamo, popanda kudya mokhazikika chakudya chauzimu chopatsa thanzi, posapita nthaŵi zovala zathu zauzimu za nkhondo zingaleluke mwina ndi mwina. Popeza kuti nthaŵi zonse timayang’anizana ndi manenanena ndi malingaliro a dziko, tingagonjetsedwe mosavuta ndi chiukiro chakupha cha Satana.
Chizindikiro china cha kufooka kwauzimu ndicho kutha kwa changu m’nkhondo yathu yauzimu. M’nthaŵi ya mtendere, msilikali samva kuvuta ndi kuopsa kwa nkhondo. Choncho mwina angachite ulesi kuti akhale wokonzeka. Ataitanidwa kunkhondo mwadzidzidzi, angakhale wosakonzeka. Ndi mmene mkhalidwe wauzimu wakhaliranso. Ngati tilola changu chathu kutha, tingakhale osakonzeka kulimbana ndi ziukiro zimene tingakumane nazo.
Koma kodi tingadziŵe bwanji kuti taloŵa mumkhalidwe umenewu? Tingadzifunse mafunso ena onga awa amene angasonyeze mmene zinthu zililidi: Kodi mmene ndimafunitsitsira kupita kokacheza ndi mmenenso ndimafunitsitsira kupita mu utumiki? Kodi ndimafunitsitsa kuthera nthaŵi ndili kukonzekera misonkhano monga momwe ndimafunitsitsira kupita kokagula zinthu kapena kuonerera TV? Kodi ndikuganiziranso zinthu zimene ndinali kulondola kapena mwayi umene ndinakana nditakhala Mkristu? Kodi ndimakhumbira zimene amati moyo wabwino umene ena akukhala? Ameneŵa ndi mafunso ochititsa kuganiza mozama, koma ndi othandiza pofuna kudziŵa chofooka chilichonse chauzimu pa zovala zathu zauzimu za nkhondo.
Popeza kuti zida zoteteza zimene tili nazo n’zauzimu, n’kofunika kuti mzimu wa Mulungu uziyenda mwaufulu m’moyo wathu. Zimenezi zimaonekera malinga ndi mmene timasonyezera zipatso za mzimu wa Mulungu m’zochita zathu zonse. Kodi mumakwiya mwinanso kukhumudwa msanga ena akachita kapena kunena kanthu kena kosakusangalatsani? Kodi mumavutika kulandira uphungu, kapena kodi nthaŵi zonse mumaganiza kuti ena akukunenani? Kodi mumadukidwa kwambiri ndi madalitso a ena kapena zimene ena akwaniritsa? Kodi mumavutika kugwirizana ndi ena, makamaka anzanu? Kudzipenda moona mtima kudzatithandiza kuona ngati moyo wathu uli wodzaza ndi zipatso za mzimu wa Mulungu kapena ngati ntchito za thupi zayamba kuonekera pang’onopang’ono.—Agalatiya 5:22-26; Aefeso 4:22-27.
Masitepe Othandiza Pofuna Kuthetsa Zofooka Zauzimu
Kupeza zizindikiro za zofooka zauzimu sindiko kuzivomereza ndi kuchitapo kanthu pofuna kuzithetsa. N’zomvetsa chisoni kuti ambiri amakonda kupereka zifukwa zodzikhululukira, kunyalanyaza, kuliona mopepuka vutolo, kapena kukana kuti ali ndi vuto. Zimenezotu n’zoopsa—ngati kupita kunkhondo mulibe zovala zina za nkhondo! Kuchita zimenezo kungatiike pangozi yovulazidwa ndi chiukiro cha Satana. M’malo mwake, mwamsanga tiyenera kutenga masitepe othandiza kuti tikonze zolakwa zilizonse zimene tingapeze. Kodi tingachite chiyani?—Aroma 8:13; Yakobo 1:22-25.
Kumenya nkhondo yauzimu—nkhondo yoloŵetsapo kulamulira maganizo ndi mtima wa Mkristu—tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti titchinjirize maganizo athu. Kumbukirani kuti pakati pa zovala zauzimu za nkhondo pali “cha pachifuŵa cha chilungamo,” chimene chimateteza mtima wathu, ndi “chisoti cha chipulumutso,” chimene chimateteza maganizo athu. Kuphunzira kugwiritsa ntchito bwino zogaŵira zimenezi n’kumene kungatipezetse chipambano m’malo mogonja.—Aefeso 6:14-17; Miyambo 4:23; Aroma 12:2.
Kuvala bwino “cha pachifuŵa cha chilungamo” kumafuna kuti nthaŵi zonse tizionetsetsa kuti tikukonda chilungamo ndipo tikudana ndi kusayeruzika. (Salmo 45:7; 97:10; Amosi 5:15) Kodi miyezo yathu yatsikira limodzi ndi miyezo ya dziko? Kodi tsopano tayamba kuona zinthu zimene poyamba zinali kutinyansa kapena kutikhumudwitsa—kaya zenizeni kapena zosonyezedwa pa TV ndi m’mafilimu, m’mabuku ndi m’magazini—kukhala zosangalatsa? Kukonda chilungamo kudzatithandiza kuona kuti zimene dziko limati ufulu ndiponso kudziŵa zinthu mwina kwenikweni ndizo chiwerewere ndi kudzikweza.—Aroma 13:13, 14; Tito 2:12.
Kuvala “chisoti cha chipulumutso” kumaphatikizapo kumaganizira kwambiri madalitso odabwitsa a m’tsogolo, osadzilola kusokonezedwa ndi kukongola ndi kusangalatsa kwa dzikoli. (Ahebri 12:1-3; 1 Yohane 2:16) Kukhala ndi malingaliro ameneŵa kudzatithandiza kuika zinthu zauzimu patsogolo m’malo mwa mapindu akuthupi kapena kudzipezera phindu. (Mateyu 6:33) Choncho, pofuna kutsimikizira kuti tavala bwino chovala cha nkhondo chimenechi, moona mtima tiyenera kudzifunsa kuti: Kodi ndikulondola chiyani m’moyo? Kodi ndili ndi zolinga zauzimu zenizeni? Kodi ndikutani pofuna kuzikwaniritsa? Kaya ndife otsalira mwa Akristu odzozedwa kapena a mu “khamu lalikulu,” tiyenera kutsanzira Paulo, amene anati: “Ine sindiŵerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiŵaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo.”—Chivumbulutso 7:9; Afilipi 3:13, 14.
Mafotokozedwe a Paulo a zovala zathu zauzimu za nkhondo akutha ndi uphungu wakuti: “Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse.” (Aefeso 6:18) Zimenezi zimasonyeza masitepe aŵiri othandiza amene tingatenge pofuna kuthetsa kapena kudzitchinjiriza ku chofooka chilichonse chauzimu: Khalani paunansi wabwino ndi Mulungu, ndipo khalani woyandikana kwambiri ndi Akristu anzanu.
Ngati tili ndi chizoloŵezi chopita kwa Yehova m’mapemphero ‘onse’ (kuvomereza machimo athu, kuchonderera chikhululukiro, kupempha chitsogozo, kum’thokoza chifukwa cha madalitso, zitamando zochokera pansi pa mtima) ndiponso “nthaŵi yonse” (poyera, mtseri, panokha, mosayembekezereka), timayandikana ndi Yehova. Chimenecho ndicho chitetezo chachikulu kwambiri chimene tingakhale nacho.—Aroma 8:31; Yakobo 4:7, 8.
Komanso, tikulangizidwa kupempherera “oyera mtima onse,” ndiko kuti, Akristu anzathu. Mwina m’mapemphero athu tingakumbukire abale athu auzimu a kumayiko akutali amene akuvutika ndi chizunzo kapena ndi zovuta zina. Koma bwanji za Akristu amene timagwira nawo ntchito ndi kuyanjana nawo tsiku ndi tsiku? Kulinso bwino kuwapempherera, monga momwe Yesu anapempherera ophunzira ake. (Yohane 17:9; Yakobo 5:16) Mapemphero oterowo amatiyandikizitsa kwa wina ndi mnzake ndi kutilimbitsa kuti tilimbane ndi ziukiro za “woipayo.”—2 Atesalonika 3:1-3.
Pomalizira pake, nthaŵi zonse muzikumbukira uphungu wachikondi wa mtumwi Petro wakuti: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero; koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:7, 8) N’kosavuta kulola zophophonya zaumunthu—za anthu ena ndi zathu zomwe—kuloŵa m’mitima yathu ndi m’maganizo mwathu ndi kukhala zopinga ndi miyala yokhumudwitsa. Satana amadziŵa bwino kuti anthu ali ndi chofooka chimenechi. Machenjera ake ena ndiwo kupatutsa anthu ndi kuwagonjetsa. Choncho, tiyenera kufulumira kukwirira machimo oterowo ndi chikondi chachikulu pa wina ndi mnzake ndi ‘kusam’patsa malo Mdyerekezi.’—Aefeso 4:25-27.
Khalani Wolimba Mwauzimu Tsopano
Mukadziŵa kuti simunapese bwino kapena kuti tayi yanu yakhota, kodi mumatani? Nthaŵi zambiri mumadzikonza msangamsanga. Ndi ochepa amene angangonyalanyaza zolakwika zimenezo, akumati maonekedwe akunja alibe kanthu. Tiyeni tichitepo kanthu mwamsanga chotero pa zofooka zathu zauzimu. Kusaoneka bwino kwakuthupi kungapangitse anthu kutiyang’ana modabwa, koma zolakwa zauzimu zosawongoleredwa zingapangitse Yehova kusakondwera nafe.—1 Samueli 16:7.
Mwachikondi, Yehova watipatsa zonse zofunikira kuti atithandize kuzula zofooka zilizonse zauzimu ndi kukhalabe olimba mwauzimu. Mwa misonkhano yachikristu, zofalitsa zofotokoza Baibulo, ndi Akristu anzathu ofikapo ndiponso osamala, nthaŵi zonse amatipatsa zikumbutso ndi zitsogozo pa zimene tiyenera kuchita. Zili kwa ife kuzilandira ndi kuzigwiritsa ntchito. Zimenezi zimafuna kuyesetsa ndi kudzilanga. Koma kumbukirani zimene mtumwi Paulo ananena moona mtima kuti: “Ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:26, 27.
Khalani chire, ndipo musalole konse kukhala ndi chitende cha Achilles chauzimu. M’malo mwake, modzichepetsa ndi molimba mtima tiyeni tichitepo kanthu tsopano kuti tidziŵe ndi kuthetsa zofooka zilizonse zauzimu zimene tili nazo.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
“DZIYESENI NOKHA, NGATI MULI M’CHIKHULUPIRIRO, DZITSIMIKIZENI NOKHA.”—2 Akorinto 13:5.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
“DIKIRANI M’MAPEMPHERO; KOPOSA ZONSE MUKHALE NACHO CHIKONDANO CHENICHENI MWA INU NOKHA; PAKUTI CHIKONDANO CHIKWIRIRITSA UNYINJI WA MACHIMO.”—1 Petro 4:7, 8.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]
DZIFUNSENI KUTI . . .
◆ Kodi ndimafunitsitsa kuthera nthaŵi ndili kukonzekera misonkhano monga momwe ndimafunitsitsira kupita kokagula zinthu kapena kuonerera TV?
◆ Kodi ndimakhumbira zimene amati moyo wabwino umene ena akukhala?
◆ Kodi ndimakwiya msanga ena akachita kapena kunena kanthu kena kosandisangalatsa?
◆ Kodi ndimavutika kulandira uphungu, kapena kodi nthaŵi zonse ndimaganiza kuti ena akundinena?
◆ Kodi sindigwirizana kwambiri ndi ena?
◆ Kodi miyezo yanga yatsikira limodzi ndi miyezo ya dziko?
◆ Kodi ndili ndi zolinga zauzimu zenizeni?
◆ Kodi ndikutani pofuna kukwaniritsa zolinga zanga zauzimu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Achilles: Kuchokera m’buku lakuti Great Men and Famous Women (Amuna ndi Akazi Otchuka); Asilikali a Roma ndi patsamba 21: Historic Costume in Pictures/Dover Publications, Inc., New York