Oweruza
7 Kenako Yerubaala,+ kapena kuti Gidiyoni, ndi anthu onse amene anali naye, anadzuka mʼmawa nʼkumanga msasa pa Kasupe wa Harodi. Msasa wa Amidiyani unali chakumpoto, mʼchigwa, kuphiri la More. 2 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene uli nawowa ndi ambiri kuti ndipereke Amidiyani mʼmanja mwawo,+ chifukwa Isiraeli angadzitame pamaso panga nʼkumanena kuti, ‘Ndinadzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.’+ 3 Tsopano lengeza kwa anthu onse kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha kapena kunjenjemera abwerere kunyumba.’”+ Choncho Gidiyoni anayesa anthuwo ndipo anthu 22,000 anabwerera nʼkutsala anthu 10,000.
4 Komabe, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Anthu amene atsalawa adakali ambiri. Pita nawo kumadzi kuti ndikawayese kumeneko. Amene ndikakuuze kuti, ‘Uyu apite nawe,’ ukapite naye, koma amene ndikakuuze kuti, ‘Uyu asapite,’ usakapite naye.” 5 Choncho Gidiyoni anauza anthuwo kuti apite kumadzi.
Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Aliyense amene akamwe madzi potunga madziwo ndi manja, ukamuike kumbali ina. Ndipo aliyense amene akamwe madzi atagwada nʼkuwerama, ukamuike kumbali inanso.” 6 Ndipo anthu amene anamwa madzi ndi manja analipo 300. Koma ena onse anamwa atagwada nʼkuwerama.
7 Ndiyeno Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Ndidzakupulumutsani pogwiritsa ntchito amuna 300 amene amwa madzi ndi manja awo, ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu.+ Koma ena onsewo abwerere kunyumba.” 8 Choncho, iye anabweza amuna ena onse a Isiraeli nʼkutsala ndi amuna 300 aja. Iwo anatenga chakudya ndi malipenga a nyanga ya nkhosa kwa anthu amene ankabwererawo. Msasa wa Amidiyani unali kumunsi kwawo, mʼchigwa.+
9 Usiku umenewo Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Nyamuka, pita kumsasa wa Amidiyani kukamenyana nawo, chifukwa ndawapereka mʼmanja mwako.+ 10 Koma ngati ukuchita mantha kupita kukamenyana nawo, upiteko kaye ndi mtumiki wako, Pura. 11 Ukakafika, ukamvetsere zolankhula zawo. Ukakatero ukalimba mtima* ndipo udzapitadi kumsasawo kukamenyana nawo.” Kenako Gidiyoni ndi mtumiki wake Pura, anatsetserekera kumunsi pafupi kwambiri ndi asilikali amene anali mumsasawo.
12 Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kumʼmawa+ anadzaza mʼchigwa chonse chifukwa anali ambiri ngati dzombe. Ngamila zawo zinali zosawerengeka,+ zambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 13 Gidiyoni atafika kumsasawo, anamva wina akufotokozera mnzake zimene analota kuti: “Tamvera zimene ndalota ine. Ndalota mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mkatewo unafika nʼkuwomba tenti ina moti tentiyo inagwa.+ Mkatewo unagadabuza tentiyo mpaka kuphwasuka.” 14 Pamenepo mnzakeyo anayankha kuti: “Si china ayi. Imeneyi ndi nkhondo ya Gidiyoni+ mwamuna wa ku Isiraeli, mwana wa Yowasi. Mulungu wapereka Amidiyani ndi msasa wathu wonse mʼmanja mwake.”+
15 Gidiyoni atangomva malotowo ndi tanthauzo lake,+ analambira Mulungu. Kenako anabwerera kumsasa wa Isiraeli nʼkunena kuti: “Tiyeni, Yehova wapereka msasa wa Amidiyani mʼmanja mwanu.” 16 Ndiyeno amuna 300 aja anawagawa mʼmagulu atatu. Aliyense anamupatsa lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi mtsuko waukulu wopanda kanthu, ndipo mʼmitsukomo anaikamo zounikira. 17 Kenako anawauza kuti: “Muone zimene ndikuchita, ndipo nanunso muchite zomwezo. Ndikakafika mʼmalire a msasa, zimene ine ndikachite, nanunso mukachite zomwezo. 18 Ndikakaliza lipenga la nyanga ya nkhosa pamodzi ndi anthu onse a mʼgulu langa, nanunso mukalize malipenga anu kuzungulira msasa wonse, ndipo mukafuule kuti, ‘Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!’”
19 Gidiyoni ndi amuna 100 amene anali naye anafika kumalire a msasa ulonda wapakati pa usiku* ukungoyamba kumene. Pa nthawiyi nʼkuti atangosintha kumene alonda ena apamsasa. Ndiyeno analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ nʼkuphwanya mitsuko yaikulu imene inali mʼmanja mwawo.+ 20 Atatero magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa nʼkuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Ananyamula zounikira kudzanja lawo lamanzere ndipo ankaliza malipenga omwe anali kudzanja lawo lamanja, nʼkuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova komanso ya Gidiyoni!” 21 Pa nthawi yonseyi nʼkuti aliyense ataimirira pamalo ake kuzungulira msasawo ndipo asilikali onse a Amidiyani anayamba kuthawa kwinaku akufuula.+ 22 Amuna 300 aja anapitiriza kuliza malipenga, ndipo Yehova anachititsa Amidiyani kuukirana okhaokha mumsasa wonsewo.+ Asilikaliwo anathawa mpaka kukafika ku Beti-sita ndi ku Zerera mpaka kumalire kwa mzinda wa Abele-mehola+ pafupi ndi Tabati.
23 Komanso, anasonkhanitsa amuna a mu Isiraeli kuchokera mʼmafuko a Nafitali, Aseri ndi Manase yense,+ ndipo anathamangitsa Amidiyani. 24 Gidiyoni anatumiza uthenga kudera lonse lamapiri la Efuraimu, wakuti: “Pitani ku Beti-bara ndi kumtsinje wa Yorodano, ndipo mukaike amuna mʼmalo owolokera kuti Amidiyani asadutse.” Choncho, amuna onse a Efuraimu anasonkhana ndipo anatseka malo owolokera Yorodano ndi mitsinje yake ingʼonoingʼono mpaka ku Beti-bara. 25 Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi. Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitiriza kuthamangitsa Amidiyani+ ndipo anabweretsa mutu wa Orebi ndi wa Zeebi kwa Gidiyoni mʼchigawo cha Yorodano.