Zekariya
4 Mngelo amene ankalankhula ndi ine uja anabwerera nʼkundidzutsa ngati akudzutsa munthu amene akugona. 2 Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”
Ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7,+ inde nyale 7, ndipo nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zilinso ndi mapaipi 7. 3 Pafupi ndi choikapo nyalecho pali mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli kumanja kwa mbale yolowa ija ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”
4 Kenako ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?” 5 Mngeloyo anafunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?”
Ndinayankha kuti: “Sindikudziwa mbuyanga.”
6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 7 Ngakhale Zerubabele+ atakumana ndi chopinga chachikulu ngati phiri, chidzasalazidwa nʼkukhala malo afulati.+ Iye adzabweretsa mwala wotsiriza ndipo anthu adzafuula kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”
8 Ndinamvanso mawu a Yehova akuti: 9 “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa inu. 10 Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Popeza anthu adzasangalala ndipo adzaona chingwe choyezera cha mmisiri womanga, mʼdzanja la Zerubabele. Nyale 7 zimenezi* ndi maso a Yehova amene akuyangʼana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+
11 Ndiyeno ndinafunsa mngelo uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kumanja ndipo wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12 Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi* ziwiri za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide mʼmbale yolowa kudzera mʼmapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?”
13 Iye anandifunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?”
Ndinayankha kuti: “Ayi mbuyanga.”
14 Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi odzozedwa awiri amene amaima kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+