Katungulume—Zipatso Zonga Ntedza
KUCHOKERA pa malo anga openyerera bwino pamwambamwamba pa phiri, ndikuwona m’pambo wa zisumbu zoyera zomwazikana ponseponse pansi pa chigwa chowoneka chobiriwira ndi chotsiira. Kuyang’anitsitsa kwapafupi kuvumbula kuti chimene chiwoneka patali kukhala monga munda wa mbuluwuli zoyera chiri, mchenicheni, zikwi za mitengo umodzi ndi umodzi, uliwonse wodzala ndi maluŵa oyera okhala ndi upofu wosalimba pakati womwe umadzaza mpweya ndi kununkhira kwawo kochulukira. Zosangalatsa zimenezi zomwe zimachititsa nthumazi malingaliro anga zimalongosola bwino koposa munda wa mitengo ya katungulume wokhala ndi maluŵa okwanira mkati mwa nthaŵi yoyambirira ya ngululu.
Ndakhala wosangalala ndi kuyang’ana kodzetsa m’pumulo kumeneku chiyambire ubwana wanga chifukwa chakuti ndinaleredwa m’munda wa mitengo ya katungulume mu mzinda waung’ono wa California. Banja langa linasungidwa kukhalapo kwake ndi moyo mwa kulima munda wa katungulume ndi kukolola zipatso zokoma zimenezi.
“Zipatso?” Inu mungafunse motero. “Kodi katungulume sintedza?” Chabwino, inde kapena ayi. Ngakhale umalingaliridwa mofala kukhala ntedza, katungulume ali, molongosoka, chipatso. Iri mbali ya banja ku imene mitengo ya zipatso zoulungana zimatenga chiyambi chake, zotchedwa kuti banja la rose. Zipatso zoulungana zimaphatikizapo mapichesi, apricots, ndi plums. Nthaŵi yotsatira pamene mudzakhala ndi pichesi youlungana m’dzanja lanu, mukapenyetsetse mmene limafananira ndi chikamba cha katungulume mu ukulu ndi m’kapangidwe. Zisweni zonse ziŵiri ndipo mudzapeza kuti nthanga zake zirinso zolingana. Komabe, kokha katungulume ndiye afunikira kudyedwa, popeza kuti kudya nthanga za zipatso zonga ngati mapichesi kungakudwalitseni.
Katungulume mu Mbiri Yakale
Magwero ambiri ya katungulume amabwerera kumbuyo ku Asia Minor ndi gawo la Mediterranean. Mchenicheni, kalelo nthaŵi pamene Kristu asanadze, anthu okhala ku Middle East anali kugwiritsira ntchito katungulume monga mbali ya nthaŵi zonse ya kadyedwe kawo, ndipo kaamba ka chifukwa chabwino.
Katungulume wodzaza m’manja samapereka kokha chakudya chokoma cha mwamsanga, komanso chopatsa thanzi. Katungulume ali ndi zinthu zomanga thupi zofunika, ndiponso ndi unyinji wapadera wa zotetezera matenda zofunika ndi zolimbitsa. Ichi chikalongosola chifukwa chimene katungulume anali kuwonedwa wa mtengo wapatali koposa monga chinthu cha nthaŵi zonse mu kadyedwe ka anthu okhala ku Middle East, ndi chifukwa chimene pamene Chinasala chinakulitsa malire ake m’nthaŵi ya Mbadwo wa Pakati, kulima kwa katungulume kunatsatira.
Zobzyala za Chisilamu zinafalikira mu Spain ndiyeno pambuyo pake mu Dziko Latsopano kupyola mu kupita patsogolo kwa alendo a mamishoni a Chispanish a ku California. Tsopano, zaka 200 pambuyo pake, katungulume wakhala mitengo yolima yaikulu ya California, ndipo dziko ilo lenilo liri limodzi la maiko olima katungulume otsogolera m’dziko.
Kugwiritsira Ntchito kwa Miphika Yochinjiriza
Mkati mwa nthaŵi ya kumasula maluŵa, kuphukira kwa maluŵa a katungulume kumakhala pa ngozi ya kuvulazidwa kutawonetsedwa kwa nthaŵi yaitali ku malo ozizira koposa. Mu nthaŵi za kumbuyo, kuti achinjirize kuvulazidwa kwa zophukira zosalimbazi, miphika yochinjirizira inagwiritsiridwa ntchito kupereka chitetezero molimbana ndi chisanu. Miphika yokhala ndi mafuta otentha imeneyi inaikidwa m’mbali ya mitengo yondandalitsidwa pa nthaŵi zosiyanasiyana. Ngakhale kuti mphukira zochepa za katungulume zinapindula mokulira kuchokera ku kuphimba koyera, kwa utsi wakuda umene unatulutsidwa, anthu okhala kumaloko sanatero!
Tangolingalirani kupita kukagona waudongo ndiyeno kuuka m’mamawa ndi nkhope yanu yophimbidwa ndi nkhungu lakuda lalikulu lomwe linalowerera m’mpuno mwanu ndipo ngakhale kulowanso mu zikhadabo zanu! Palibe mazenera otsekedwa ndi zitseko kapena kuchuluka kwa sopo ndi madzi komwe kukanatisunga ife audongo mkati mwa kumenyana kwa miphika yochinjiriza molimbana ndi chisanu.
Mwachisangalalo, ngakhale ziri tero, zinthu zasintha. Minda ina ya mitengo ikali kugwiritsirabe ntchito miphika yochinjirizira, koma njira zina zikugwiritsiridwa ntchito bwino lomwe tsopano, ku chikondwerero cha nzika zokhala m’midzi yolima katungulume.
Phokoso la Kugwa kwa Katungulume
Njira yotutira katungulume yasinthanso m’kupita kwa zaka. Ogwira ntchito olembedwa, omwe anasonkhanitsa zomenyera za m’mpira ankakwera mofulumira mu mitengo ndi kumenya nthambi, kupangitsa katungulume kugwera mu nsalu za chiguduli zoyalidwa m’munsi ndi phokoso lalikulu. Ndiyeno nsaluzo zinkakokedwa ndi kavalo kapena trakita ku mtengo wotsatira ndipo m’chitidwewu unabwerezedwanso. Pamene nsaluzo zinali zolemera kwambiri kuzikoka, katungulume anakaikidwa mu matumba opangidwa ndi luzi ndipo ndi kuperekedwa ku chiwiya chopunthirapo kuti akayeretsedwe.
Lerolino, mosiyanako, makina amagwiritsiridwa ntchito kugwedeza mitengo, kusonkhanitsa katungulume, ndipo ngakhale kusiyanitsa zosafunika za fumbi ndi zikamba kuchokera ku zipatso. Atate wanga anali m’modzi wa oyambirira kupanga makina omwe ankakoka mpweya wambiri kuti alekanitse zosafunika zambiri kuchoka ku chipatso cha katungulume chenichenicho.
Pambuyo pake, katungulume weniweniyo amagwera kupyola mu mbali ya makina omwe amachita mchitidwe wonsewu paokha. Kumeneko amaswedwa, kuyeretsedwa, kusankhidwa molingana ndi ukulu wake kulekanitsidwa ndi diso la magetsi, ndi kupatsidwa chiyang’aniro chotsirizira.
Chimene chimachitika chotsatira ku akatungulume ena chiri chochititsa nthumazi ndi chodzetsa chilakolako. Tangolingalirani, katungulume wopanda kanthu kukometseredwa mwadzidzidzi ndi kununkhira konga kwa ntedza, adiyo kapena anyenzi, kapena kupakidwa shuga, kuikidwa mchere, kukazingidwa, kapena kupangidwa mu butter wa katungulume—kungotchula zochepa za kusintha kokoma kwakukulu komwe kumapangidwa kulonjeza ziwalo zathu zolawirako. Ndipo tisaiwale masiwiti otsekemera onsewo, zinthu za mu bekala, ndi ice creams zokometseredwa ndi katungulume wathunthu kapena wopunthidwa!
Kukulira m’munda wa mitengo ya katungulume kunatsimikizira kukhala kosangalatsa kwakukulukulu ndi kokumbukika kwa ine. Inu mungalingalire kuti ndikanadziwa zonse zimene ziriko kuti ndidziwe ponena za zipatso zonga ntedza. Osati kwenikweni. Chiyamikiro changa cha katungulume chinawonjezereka kwakukulukulu pambuyo pa kuyamba kwanga kuphunzira Baibulo. “Baibulo?” inu mukufunsa. Inde, kupyolera mu kuphunzira kwanga, ndapeza kuti mtengo wa katungulume unali ndi mbali yapadera m’kuchita kwa Mulungu ndi anthu ake.
Katungulume m’Baibulo?
Kodi munadziwa kuti liwu la Chihebri la mtengo wa katungulume mchenicheni limatanthauza “wodzutsa,” kapena “kudzutsa wina”? Ichi chiri choyenera titakumbukira kuti m’mbali za Palestine mitengo ya katungulume iri pakati pa mitengo yoyambirira yonse yobala zipatso yomwe imakhala ndi maluŵa, koyambirira kwa January kapena koyambirira kwa February. Chimathandizanso kulongosola chimene Mulungu anatanthauza pamene anasonya ku “nthyole ya katungulume.” (Yeremiya 1:11, 12) Mu mawu ena, Yehova Mulungu “akukhala wogalamuka [NW]” Ponena za malonjezo ake kotero kuti awakwaniritse.
Chitsanzo china cha kugwiritsiridwa ntchito kwa mtengo wa katungulume mu Baibulo chiri cholembedwa chodzutsa mtima cha kutokosa kwa Israyeli ulamuliro wa Aroni monga wansembe wamkulu wodzozedwa ndi Mulungu. Kuti athetse nkhani, Mulungu analamulira kalonga m’modzi ndi m’modzi wa mafuko 12 a Israyeli kubweretsa ndodo yake ya ulamuliro patsogolo ndi kuika pamaso pa likasa lopatulika la umboni. Ndodo ya Aroni, yopangidwa kuchokera ku nthambi ya katungulume, inaikidwa pamodzi ndi zina 12. Tsiku lotsatira linabweretsa zotulukapo—chisonyezero cha kuvomereza kwa Yehova pa Aroni. Ndodo yake inaphukira usiku; iyo “inawonetsa timaani, nichita maluŵa, nipatsa akatungulume.” M’malo mwa mchitidwe wa chibadwa wa kuphuka, kuchita maluŵa, ndiyeno zipatso, mbali zonse zitatu zinachitikira pamodzi. Chozizwitsa ndithudi!—Numeri 17:1-11.
Katungulume analinso chotsekemera chapadera kwa Aisrayeli. Kulongosola mwachitsanzo, pamene kholo lakale Yakobo anafuna kupeza chiyanjo ndi mfumu ya ku Igupto, iye anatumiza mphatso kuphatikizapo ndi unyinji wa akatungulume monga chimodzi cha “zipatso zabwino kwambiri za m’dziko.” (Genesis 43:11, NW) Kuwonjezerapo, maluŵa okoma a katungulume anagwiritsiridwa ntchito monga chifaniziro cha zikho pa nthambi za choyikapo nyali chopatulika cha kachisi.—Eksodo 25:33, 34.
Popanda kukaikira, zisonyezero za Baibulo zimenezi kulinga ku katungulume zandipangitsa iye kuyamikira mokulira kwenikweni chinthu chimodzi chowonjezereka cha zolengedwa zambiri zodabwitsa zimene Mulungu wapanga kaamba ka chisangalalo chosatha cha munthu.
Kaŵirikaŵiri, nditapenyetsetsa mosamalitsa modutsa chigwa pa kawonekedwe kokongola ka munda wa katungulume mu nthaŵi ya kumasula maluŵa, ndimalingalira pa mawu awa olembedwa mazana ambirimbiri apitawo: “Lemekezani Yehova kuchokera ku dziko lapansi, . . . mapiri ndi zitunda zonse; mitengo ya zipatso ndi yamikungudza yonse.” (Masalmo 148:7-9)—Yothandiziridwa.
[Bokosi patsamba 26]
Katungulume—Mitolo Yaing’ono ya Mphamvu Zowunjikana Pamodzi
Katungulume amasonkhanitsa zakudya zambiri mu m’tolo waung’ono, wokhoza kunyamulidwa ku manja. Zimakhala ndi zakudya zofunika zopezedwa m’magwero a magulu anayi onse a zakudya—zomanga thupi, zipatso ndi ndiwo za masamba, zotulutsidwa za mkaka, ndi chimanga. Tiyeni tiyang’anitsitse mosamalitsa pa kapangidwe kawo ka zakudya.a
◻ ZINTHU ZOPATSA THANZI: Katungulume ali cholowanecholowane wa magwero ogwira ntchito a zinthu zopatsa thanzi. Zinthu zopatsa thanzi ziri magwero okulira amphamvu zanu za m’thupi. Aunsi imodzi ya akatungulume, chifupifupi nthanga 20-25, zimadzapanga ma-calories 170.b
◻ ZOTENTHETSA NDI KUPATSA MPHAMVU: Pakati pa zomera zogwiritsiridwa ntchito monga zakudya, katungulume ziri zimodzi za magwero olemeretsa a zotenthetsa ndi kupatsa mphamvu. Ndipo katungulume samakhala ndi cholesterol. Zotenthetsa ndi kupatsa mphamvu ziri magwero ofunika amphamvu; ziri mchitidwe wathupi lanu wopambana kwambiri wa mafuta osonkhanitsidwa. Chifupifupi theka la kulemerera kwa katungulume kuli mafuta a ndiwo za masamba—zomwe ziri zotenthetsa ndi kupatsa mphamvu zosanganizidwa ndi madzi ndipo zoposadi.
◻ ZOLIMBITSA MISEMPHA: Aunsi imodzi ya katungulume imapatsa thupi lanu chifupifupi 10 peresenti ya zolimbitsa mitsempha zofunika za tsiku ndi tsiku. Chimene chiri zolimbitsa mitsempha zambiri kuposa ndi zimene zimapezeka mu zidutswa ziŵiri za mkate wa tirigu wokhawokha.
◻ ZOLIMBITSA ZOPEZEKA MZAKUMWA: Katungulume amapatsa unyinji wokulira wa zolimbitsa zopezeka mzakumwa zofunika zonga phosphorus, mkuwa, ndi magnesium. Zolimbitsa zopezeka mzakumwa zimafunidwa ndi thupi lanu kaamba ka kukula ndi kusamalira kwabwino. Aunsi imodzi ya katungulume iri ndi unyinji umodzimodzi wa calcium wonga maaunsesi 2.3 a mkaka ndipo uli ndi unyinji umodzimodzi wa iron wonga maaunsesi 1.3 anthuli ya nyama ya ng’ombe kapena nthuli ya nyama ya nkhumba yopanda mafuta.
◻ ZOMANGA THUPI: Katungulume ali magwero abwino a zomanga thupi za ndiwo za masamba. Zomanga thupi ziri zabwino kaamba ka kukula kwa thupi lanu ndi kusamalira. Aunsi imodzi ya katungulume imapatsa 10 peresenti ya RDA ya ku U.S. (Recommended Daily Allowance) ya zomanga thupi.
◻ ZOTETEZERA MATENDA: Katungulume ali magwero abwino a zothandizira thupi kukula (vitamini B2) ndi vitamini E. Zotetezera matenda ziri zofunika kaamba ka umoyo wanu wabwino. Aunsi imodzi ya katungulume imakhala ndi unyinji wa vitamini E (35 peresenti ya U.S. RDA) yopezedwa mu maaunsesi 7 amagwero a tirigu kapena kuchokera ku maaunsesi 18 kufika ku 20 a chiwindi.
[Mawu a M’munsi]
a Chidziŵitsochi chazikidwa mu kabroshuwa ka Almonds—A Health Nut, kofalitsidwa ndi Almond Board of California.
b 1 oz = 28 g.