Lingaliro Labaibulo
Kodi Kusamvera Lamulo la Boma Kumalungamitsidwa?
“PAMENE muwona anthu anu akugwiriridwa chigololo ndi kuphedwa,” anatero m’mishonale wa Chikatolika wa zaka 30 za kubadwa, “pamene muwona mizinda yonse ikugwetsedwa ndi asilikali, ndipo achichepere akuchotsedwa m’nyumba zawo, ndipo pamene muzindikira kuti 2 peresenti ya chiŵerengero cha dziko ikulamulira kale makota atatu a chuma, inu simungazike mutu wanu m’Baibulo ndi kunyalanyaza zenizeni zimenezi.”—Kanyenye ngwathu.
Ngati inu munali mu mkhalidwe umenewu wa m’mishonale, kodi nchiyani chimene mukanachita? Kugwirizana mu kuwonetsera kwa mtendere kapena kuleka kugwira ntchito? Bwanji ngati izi sizinabweretse kusintha kofunikako? Kodi chiwawa kenaka chingalungamitsidwe? Kusinthika kapena kulanda boma mwaupandu? Kodi nchiyani chimene “atsogoleri auzimu” a lerolino amayamikira? Onani maripoti otsatirawa:
◻ Mtsogoleri wa chipembedzo mu Nicaragua ananena kuti iye amatumikira Mulungu mwa kutumikira anthu ndi magulu a chisinthiko.
◻ Mu Philippines minisitala anachotsedwa m’dziko kaamba ka kupangitsa kusakhazikika kwa ndale za dziko ndi kusonyeza Yesu monga wowukira lamulo.
◻ Ansembe ndi a virigo agwirizana ndi omenyera ufulu m’kuyesayesa kwa kugwetsa boma mu Central America.
Kachitidwe kawo kanapereka uthenga wowirikiza ndi womvekera: Kusamvera lamulo la boma kumalungamitsidwa kapena ngakhale kuwonedwa monga ntchito ya Chikristu. Koma kodi ichi chiri chowona, ngakhale pamene zisonkhezero ndi zolinga ziri zotsimikizirika ndi za umunthu? Kodi ndi kati kamene kali kawonedwe ka Baibulo?
‘Kukaniza Choikika ndi Mulungu’?
Mulungu ali ndi lamulo lolongosoledwa bwino kwambiri kulinga ku maboma aumunthu kapena maulamuliro. Baibulo limalongosola kuti: “Palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.” Inde, Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zoyenerera za kuloŵerera kapena kuchotsapo ulamuliro uliwonse womwe ulipo pa nthaŵi iriyonse yopatsidwa. Ngati iwo akugwira ntchito, chiri chifukwa chakuti iye akuwalola iwo.—Aroma 13:1.
Pambuyo pa kukhazikitsa nsonga imeneyi, lembalo likuwonjezera kuti: “Kotero kuti iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.” (Aroma 13:2) M’kawonedwe ka mawu amenewa, kodi Mkristu mwachikumbumtima anganene kuti iye ‘amatumikira Mulungu mwa kutumikira gulu la chisinthiko’? Kodi wina akukaniza ‘choikika ndi Mulungu’ mwakudzilowetsa, kapena ngakhale kulengeza, machitachita omwe mwachindunji amatsutsa ulamuliro wa boma lomwe liripo?
Tiyeni tiyang’ane ku mbiri yakale ya Baibulo kaamba ka yankho. Pamapeto pa zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., Yehova analola ufumu wa Babulo kulamulira Aisrayeli, akumapangitsa Zedekiya wa ku Yerusalemu kukhala mfumu ya mu ukapolo. Pambuyo pa zaka zisanu ndi zitatu za kugonjera, ngakhale kuli tero, Zedekiya anamva kukhala wopanikizidwa kutsutsana ndi kachitidwe koteroko. Iye anaitana Aigupto kaamba ka thandizo. Iye sanakhozenso kulola mphamvu zachilendo—zachikunja pa nthaŵiyo—kulamulira anthu a Mulungu. Malingaliro ake anawoneka kukhala oyera. Komabe, ndimotani mmene Mulungu anachiwonera? Kodi Zedekiya adafunikira kukhala “womenyera ufulu” wovomerezedwa mwaumulungu? Ayi! Popeza kuti m’kuukira motsutsana ndi Babulo, iye ankakhozanso kuukira Mulungu. M’chigwirizano ndi kuukira kumeneku, Yehova analamulira kuti Zedekiya afe monga kapolo mu Babulo.—2 Mafumu 24:17-20; Ezekieli 17:15, 16.
Nkhani ya Zedekiya siiri chochitika cha kamodzikamodzi. Mbiri yakale yasonyeza kaŵirikaŵiri kuti kusamvera lamulo la boma, ngakhale ngati kutakhala ndi cholinga chabwino, sikungabweretse yankho losatha ku mavuto a munthu. Chenicheni chiri chakuti zobuka ndi magulu a chisinthiko kaŵirikaŵiri amakhoza kuipitsanso mkhalidwe. M’nkhani zambiri pambuyo pa kupambana kowonedweratu kwa magulu a chisinthiko, “omenyera” iwo eniwo potsirizira pake amadzadzimva a mlandu kaamba ka nkhalwe ndi kudidikiza. M’kupita kwa nthaŵi, mbadwo watsopano wa anthu odidikizidwa umafunafuna kuukira. Zungulirezungulire woteroyo wa kuipa wakhala ukukumanizidwa m’maiko ambiri. Mwachitsanzo, dziko limodzi mu South America posachedwapa linakumana ndi kulanda boma kwake kwa 189 m’zaka 154!
Kulephera kwa Munthu—Nchifukwa Ninji?
Nchifukwa ninji kuli kwakuti amuna otsimikizirika sangakhoze kumasula mtundu wa anthu ku kupanikizidwa ndi nkhalwe? Kokha chifukwa chakuti amasowa zinthu ziŵiri—nzeru ndi mphamvu. Nchosadabwitsa kuti Baibulo limatichenjeza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Masalmo 146:3.
Kuchitira chitsanzo, pangani chithunzi cha inu eni muli m’chipatala mukuyembekezera kutumbulidwa. Mukulira kaamba ka kuwawidwa ndi kusamva bwino. Mwadzidzidzi, woyeretsa malo yemwe akungopita akumvani, agwira mpeni, ndipo akufunsani za chithandizo chake kuti akupatseni mpumulo wofunika. Kodi mungamulole iye kukutumbulani? Ndithudi ayi! Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti chikondi chake ndi chifundo zokhazo sizingamuyeneretse iye kaamba ka ntchito yovuta yoteroyo. Kachitidwe kake kadzangoipitsirako kuvutika kwanu, ngakhale kukuikani inu m’ngozi yokhoza kufa nayo. Kachitidwe koteroko kangakhale ka nsontho ndipo kopanda thayo kwakukulukulu ndipo konyalanyaza nsonga yakuti nthaŵi yaikidwa pambali kaamba ka dokotala wotumbula anthu woyeneretsedwa kuti achite ntchitoyo. Iko m’kupita kwa nthaŵi, kungakhale kwabwino kwambiri kaamba ka iye kungokutsimikizirani kokha kuti chithandizo chikubwera.
Mofananamo, Akristu owona lerolino samadziloŵetsa m’kusamvera lamulo la boma. Iwo amayembekezera tsiku ndi ora pamene kuloŵereramo koyeneretsedwa kwa Mulungu kudzabwera. Kokha iye ali ndi nzeru ndi mphamvu za kubweretsera yankho losatha ku mtundu wa anthu. Kupyolera mu ntchito yawo yolalikira, Mboni za Yehova zimatsimikizira awo omwe akuvutika ndi kupanda chilungamo kuti mpumulo woterowo uli pafupi kudza.—Yesaya 9:6, 7; 11:3-5.
Padakali pano, tingakhoze kutsatira njira za lamulo ndi za mtendere zomwe ziripo za kukhazikitsira ndi kuchinjiriza kuyenera kwathu ndi kupeza mpumulo kwa otsendereza. Ngati izi zalephera, ngakhale kuli tero, chikakhala kulakwa kusinthira ku kusamvera lamulo la boma. Mwatsatanetsatane, mtumwi Paulo analangiza kuti: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pa mkwiyo; pakuti kwalembedwa: ‘Kubwezera kuli kwanga, ndidzabwezera, ati Ambuye.’” Akristu enieni ndi achimvero amatenga kudandaulira kwanzeru kumeneku ku mtima.—Aroma 12:18, 19.
[Mawu a Chithunzi patsamba 21]
Reuters/Bettmann Newsphotos