Maulendo Anga Owona Zinyama mu Africa—Analipo kaamba ka Ine—Kodi Adzakhalapo kaamba ka Ana Anga?
“JAMBO!” Titadzidzimutsidwa, tinachotsa tulo m’maso mwathu ndi kuitananso kuti, “Jambo!” Kuli kuitana kwathu kwa kudzutsa, liwu la chiSwahili kaamba ka “Kodi chatsopano nchiyani?” Pambuyo pa miyezi ingapo ya kukonzekera ndi kuyenda kwa mamailosi zikwi zoŵerengeka, tinali m’msasa wa m’malo osungira nyama za m’nkhalango mu Kenya—pa ulendo wowona zinyama mu Africa!a
Ulendowo unayamba kwenikweni tsiku limodzi pasadakhale. Pa kufika kwathu wotitsogolera wathu anatitenga ife pa ulendo wochezera zinyama. “Mphoyo!” mmodzi wa ife anafuula tero pamene tinawona cha kumbali m’magalimoto athu a paulendo. Mikono itatambasulidwa mofulumira kaamba ka kugwira makamera, mabukhu otsogoza paulendo, ndi ziwiya zowonera zinthu zomwe ziri patali.
Wotitsogolera, mwamuna wachichepere wokangalika wolankhula Chingelezi, anaseka kaamba ka kuzizwitsidwa kwathu. “Mphoyo ya Grant, m’chenicheni. Nyama zazing’ono zabwino kwambiri, kodi izo siziri tero?”
Zazing’ono, zokometseredwa monga zosalimba, komabe m’chenicheni zokhalitsa ndi zokonzekeretsedwa kaamba ka liŵiro, zolengedwa zazing’ono zokongolazi ndi mphoyo yaing’ono kwambiri ya ku Thomson zinkawoneka kulikonse kumene tinapita. Pa ulendo woyambirira wa maseŵerawu tinawonanso ndi kujambula ndi kamera ntchefu yaikulu, oryx, ndi gerenuk, ndipo tinawonanso m’ng’oma waukulu wosawonekawoneka ndi mphoyo ya m’mapiri.
Tikumazungulira, tinazizwitsidwa pa unyinji wa mphalapala. Ziri chiimirire izo zinadumpha m’mwamba mapazi asanu ndi limodzi kapena asanu ndi anayi, monga ngati kuti zinaponyedwa m’mwamba ndi chiwiya choponyera chobisika.b “Monga mmene mungalingalire, kudumpha kumeneku kumasokoneza adani ake osadziŵa kumene idzagwera,” anatero wotsogoza wathu. Kenaka mphalapalazo zinathaŵa, zikumakwaniritsa mapazi 30 pa kudumpha kumodzi.
Tinawona mbidzi, zikumawoneka zokongola kwenikweni mu mizere yake yakuda ndi yoyera, ndipo tinakumbutsidwa za cholembedwa cha m’Baibulo cha bukhu la Yobu chimene chimasonyeza kuti mbidzi sizingawetedwe. (Yobu 39:5) Ndinafunsa wotsogoza ponena za icho. “Anthu a ku America anapanga kanema pano nthaŵi zina kumbuyo,” iye anatero. “Iwo anafunafuna mbidzi yoweta kaamba ka woseŵera wamkazi kuti akakwerepo koma sanakhoze kupeza ngakhale ndi imodzi yomwe chifukwa chakuti panalibe iriyonse. Iwo anangolemba mizere pa kavalo.”
Pamene tinabwerera ku msasa pa tsiku loyambirira limenelo, tinawona nthiwatiwa. Pamene iyo inatiwona inathaŵa, miyendo yake ya mphamvu ikumaikankha iyo kukwera pamwamba pa phiri. Nthiwatiwa ingakhoze kuthamanga pa liwiro la mamailosi 40 pa ora limodzi, mapazi 25 pa mtanzi umodzi. Liwiro lake linandipangitsa ine kuganizira ponena za lemba lina la Baibulo la Yobu: “Iseka kavalo ndi wa pamsana pake.” (Yobu 39:18) Iyo inakhoza kuseka pa magalimoto athunso, ndinalingalira tero, pamene tinkapita m’mbali.
Koma munali mmawa mmenemo pamene tinadzuka ku kufuula kwakuti “Jambo!” pamene tinadzimva kuti ulendo wathu wowona zinyama unachitikadi. Tikumatuluka titakwera pa akavalo modutsa mtunda wa udzu wokhawokha wokometseredwa ndi mitengo ya acacia, tinakhumbira Phiri la Kenya pa mtunda. Mwadzidzidzi wotsogoza wathu anatiimitsa mwakachetechete ndi kuloza. Kumeneko, chapamwamba pa mitengo, kunali gulu la zinyama—nswala zikumadya masamba a acacia!
Nyama zazitali kwambiri m’dziko, nswala zinawoneka kwa ife kukhala zodekha, zosadera nkhaŵa, chilengedwe chosakhoza ngakhale kudzichinjiriza. Koma sitero; “khosi lawo lalitalilo liri lopindulitsa osati kokha kuzilola izo kudya pamwamba pa mitengo komanso kuzipatsa izo malo abwino oyang’anira ku amene zingakhoze kutsegula maso awo akulu, okhoza kuwona patali pa ana awo, zinzawo, kapena ngozi yomayandikira. Izo zinawoneka kwa ife kukhala zikuyenda pang’onopang’ono molemekezeka, komabe nswala ingakhoze kuthamanga mamailosi 35 pa ora limodzi ndi kumenya chibakera kwa mkango chomwe chingakhoze kuthyola nthiti zake. Iyo ingakhozenso kugwiritsira ntchito mutu wake monga nsando yaikulu. Nswala yokhala mosungira zinyama pa nthaŵi imodzi inapereka kukantha koteroko pa nsefu ya mapaundi 1,000 ndipo inapangitsa iyo kupita ndi phewa lothyoka!c
Tinapita titakwera pa akavalo kufika pakati penipeni pa izo. Tikanapita ndi miyendo, izo zikanamwazikana, komabe pa akavalo tinkawonedwa kokha ngati gulu lina la nyama zomadya. Mphoyo zina ndi nsefu zinali pafupi, limodzinso ndi mbidzi zosiyana kwenikweni ndi zina zomwe tinawona tsiku limodzi lapita—zazitali kwambiri, mizere yochepereko, ndipo zokongola, ndi makutu akulu ozungulira.
“Mbidzi za Grévy,” wotitsogolera wathu anatiwuza tero. “Mtundu uwu ukucheperachepera mofulumira m’chiŵerengero, kwakukulukulu chifukwa cha kukongola kwa zikopa zawo. Okometsera amalipira zochulukira kaamba ka izo.” Nchomvetsa chisoni chotani nanga kuti munthu akuwononga zambiri za zolengedwazi ndi malo ake achilengedwe! Koma panali mbiri yomvetsa chisoni kwambiri yomwe inkadza.
Tiri m’galimoto tinachezera kokhala chipembere, malo otsekeredwa a maekala 5,000 ozunguliridwa ndi mpanda woikidwa magetsi wotalika mapazi 10 ndipo wochinjirizidwa ndi nduna zokhala ndi mfuti.d Iwo uli mudzi wa zipembere 13 zakuda ndi imodzi yoyera. Tikumayenda pang’onopang’ono mochenjera kuyandikira ku imodzi ya zolengedwa zowopsyazi, zomwe tinakwerapo mwadzidzidzi zinawoneka kukhala zitawopsyedwa ndi kukhala zopanda mphamvu.
“Chipembere sichiwona bwino,” wotitsogolera anatero. “Ngati akakowa omwe amakhala pa msana pake alira ndi kuwuluka kaamba ka kuwopsyedwa, chipembere sichingakhoze kuwona chomwe chinawasokoneza ndipo chimatukula mphuno mwamsanga ku chirichonse chimene icho chiri, kuti ichinunkhize. Icho chimakhala ndi moyo m’dziko la fungo. Tsopano chipembere chikusakidwa ku mlingo wakutheratu.”
Pa kulowa kwa dzuŵa, tinabwerera ku msasa wathu mwakachetechete. Madzulo amenewo, pamene tinakhala mozungulira moto wa mumsasa tikumalankhula mwazochitika za chipembere, tinazizwitsidwa kumva kubangulira kum’mero, kozama. Iko kunayankhidwa ndi ena.
“Mikango,” anatero wotitsogolera wathu, akumasonkhezera moto mosadera nkhaŵa. “Iyo, eee, ikumveka monga iri pafupi kwambiri, kodi iyo siiri?” Ndinafunsa tero mwamantha. “Ayi ndithu. Mamailosi angapo kutali. Kubangula kwa mikango kungapite mamailosi asanu kapena kuposerapo.” Titatsimikiziridwa, tinapita kukagona, tikumayembekezera kuwona ena a avumbwe a akulu amenewa a mu paki yosungira nyama ya ku Masai Mara, kotsatira komwe tinakaima. Sitinakakhoza kugwiritsidwa mwala.
Avumbwe a Akulu a ku Mara
Pamene tinayenda modutsa malo opanda mitengo a udzu a gawo la kumadzulo limeneli la Chidikha chachikulu cha Serengeti, tinasangalatsidwa ku kufuula kwa woyendetsa galimoto kuti “Simba!” Tinadzutsidwa mochenjera kuwona osati kokha mkango umodzi koma unyinji wonse—40 yonse pamodzi. Chiŵerengero ndithu cha mikango yaikazi inali gone mu magulumagulu. Yochulukira inabwera kuchokera ku thengo. Yoŵerengeka inadzaza mozungulira chithaphwi kuti imwe. Yachichepere inaseŵera ndi kupikisana uku ndi uko ina ndi inzake.
Tinakhumba kutuluka ndi kukaseŵera ndi iyo koma tinadziletsa ife eni pamene tinawona minofu yamphamvu pansi pa thupi la mkango waukazi ndipo tinawona zazimuna zazikulu ziŵiri zokhala ndi manyenje osangalatsa atatambasulidwa mu mkhalidwe wonga wa fano—avumbwe akulu agolidi akuphethira maso awo achikasu mobwerezabwereza mu cheza chotsirizira cha dzuŵa. Nthaŵi yoseŵera ndi ana a mikango idakali kutsogolo.—Yesaya 11:6-9.
“Mikango imapuma chifupifupi maora 20 pa 24,” anatero wotitsogolera. “Ngakhale ochulukirapo kwa yaimuna. Yaikazi imachita kulera konse kwa ana mwaubwino ndi 90 peresenti ya kusaka nyama, komabe yaimuna imakhala yoyamba kudya nthaŵi zonse.” Akazi mu gulu lathu anawoneka kukhala akuwona nsongazi kukhala zapadera moseketsa! Koma pangakhale kulera ana kochepera ndi kudyetsa kwa mtendere popanda yaimuna yochinjiriza mu gululo. Ngati yaphedwa ndi mfuti monga nyama ndi osaka nyama kapena monga mphoto za kupambana za osaka, gululo kaŵirikaŵiri limamwazikana, ndipo ana amasiidwa.
Pamene kuli kwakuti mkango ukugwiririra kuyenera kwake tsopano molimbana ndi kuwopsyeza kwa kusakhalako, cheetah sakukhala bwino. M’mawa wotsatira tinakumana ndi ziŵiri za zolengedwa zosangalatsa ndi zokongola zimenezi. Anali amayi akuphunzitsa mwana mmene angasakire. Ziŵirizo zinathamanga kulinga ku khamu la mphoyo za Thomson, koma pamene mayi wake anathamanga pang’onopang’ono kukawenderera mochenjerera, mwana wake wansonthoyo anangopitirizabe kuthamangitsa nyama za Tommizo. Iye anawonjezera liwiro ku kuthamanga kwake kowopsya kwa mamailosi 70 pa ora limodzi, akumangowoneka kokha mwa deruderu. Kokha pachabe! Acheetah angakhoze kuthamanga mwaliwiro koposa kokha kwa kanthaŵi kochepa, ndipo chotero nyama za Tommizo zinathaŵa, zikumamwazikana.
Iye anayesera ndipo analepheranso. Potsirizira pake atagwiritsidwa mwala ndi kutopetsedwa, iye analola amayi wake kumsonyeza iye mmene zimachitidwira. Mayi anawenderera mphoyo kufikira itafika pafupi kwambiri ndipo kenaka anadumpha mophulapo kanthu. Mayiyo anagawana nyamayo ndi mwana wake.
“Tawonani!” wotsogolera anafuula tero, akumaloza. Fisi anangobwera mwadzidzidzi komwe anachokera osadziŵika. Iye anathamangira a cheetah, kuwawopsya iwo kuti achoke pa mphoyo yomwe anangopha kumene, ndipo anatenga nathawa nayo.
“Aah, waulesi uja!” Wotitsogolera wathu anakalipa tero. Iye anayesera kupitikitsa fisiyo kuti amulande nyama yomwe cheetah anapha, koma mbalayo inali itathawa. Afisi saali ozoloŵerana kwenikweni ndi anthu. Komabe fisi sanawopsyezepo mtundu uliwonse wa nyama ndi kale lonse kumlingo wa kutheratu. Ngati kokha anthu angakhoze kunena chofananacho!
Mabanja Osangalatsa
Pambali pa abvumbwe akulu, tinawona mabanja osiyanasiyana a zamoyo mu malo osungirako a Mara. Banja la nthiwatiwa linkayenda kumbali kwathu, makolo awo otalika mapazi asanu ndi aŵiri akumatsogolera gulu la zachichepere la mawonekedwe oipa pakati pawo. Mabanja a m’njiri anatulukira, nawonso, akawonekedwe koipa ndipo oseketsa. Mokhumbika zachangu ndipo zochenjera, zinayenda uku ndi uko limodzi ndi mitu yawo yopangidwa monga fosholo, yokhala ndi nyanga itatukulidwa m’mwamba. Michira yawo yowonda imaloza m’mwamba, monga milongoti ya galimoto.
Woyendetsa galimoto wathu wa ku Masai analoza chala chake cholozera m’mwamba ndi kuseka, “Iyo ndiyo njira ya Bambo m’Njiri ya kunena kuti, ‘Ndine wopambana onse.’”
Mabanja a apusi, nawonso, anali magwero achisangalalo chosalekeka. Pusi wa pamaso pakuda wochenjera anadumpha ndi kusinthasintha m’mitengo pamene makanda awo ankaphunzira kukwera mwa kuseŵera kosakhoza kulamulirika pansipo. Apusi a ku Colobus, akumachita maseŵera olimbitsa thupi m’mwamba mu khungu lawo lakuda pang’ono ndi loyera, anawoneka ngati ansembe openga. Banja la mkhwere linali konsekonse nalonso, makanda awo kaŵirikaŵiri akumakwera amayi awo monga nkhandwe zazing’ono. Ankhwere ali aukali ndipo amafuna kudziŵa kwakukulukulu. Mu Tanzania, mkazi wanga ndi ine tinakhoza ngakhale kupitikitsa mmodzi kuchoka ku chipinda chathu cha mu hotelo!
Yaikulu Koposa ya mu Africa
Mu imodzi ya nkhalango za mu Mara, tinawona njovu, kapangidwe kawo ka kuyera pang’ono kakumaderukaderuka bwino pakati pa mitengo. Linali gulu la nyama zisanu ndi zitatu, ndi kamwana kakang’ono ka miyezi itatu ya kubadwa ka mayiyo. Gululo linakhoza kuchinjiriza kamwana kakang’onoka kotero kuti sitinakhoze kukawona pamene kankayenda mopanda mantha pakati pa miyendo yawo yonga mizati, kakumafufuza mayi wake ndi kuyamwa kaŵirikaŵiri. Gululo, ndinadziŵa kuti, lidzayenda ku kamwanako ndi kuimirira pamodzi kuti akatetezere. M’chenicheni, padatsala pang’ono kuti mayiyo apitikitse woyendetsa galimoto wathu—iye mwamsanga anadumphira mkati mwa galimoto!
Njovu za zimuna zimakhala zosungulumwa kaŵirikaŵiri. Mu Ngorongoro Crater mu Tanzania, tinawona yaimuna yachikulire imodzi yokhala ndi minyanga yaitali yoyera. Iyo ingaigwiritsire ntchito kukumba mayenje kaamba ka mchere ndi zinthu za mu nthaka kapena ngakhale kukumba mayenje a madzi amene nyama zina zidzagawanamo m’nyengo youma. Chiri chodabwitsa chotani nanga kuti ziwiya zokongola zimenezi, zopangidwa mwachiwonekere kuti zithandize njovu kupulumuka, zasonkhezera umbombo wa munthu kotero kuti akhoze kupangitsa kuzimiririka kwake!
Yachiŵiri yokha ku njovu mu mlingo iri mvuu yaikulu. (Ena amanena kuti chipembere choyera chiri nyama yapamtunda yoyamwitsa yachiŵiri mu ukulu.) Tinakaima pafupi ndi mtsinje waung’ono kuti tiwone gulu lawo lonse likumasangalala, kukhudzanakhudzana ndi kuyasama tsiku lonselo.
“Mvuu,” wotitsogolera wathu anatiuza tero, “iyo imakhala m’madzi tsiku lathunthu kupewa kutentha kwa dzuŵa, kenaka imatuluka kunja kudzadya usiku. Mafuta pa khungu lake amaichinjiriza ilo ku dzuŵa lotentha kwambiri ndi madzi. Modabwitsa,” iye anapitiriza tero, “mvuu zimapha anthu ambiri kuposa nyama ina iriyonse ya mu Africa. Izo siziri zakudya nyama, koma zimasambira kapena kusendera pafupi kwambiri—ndipo kuluma kumodzi kumangotha zonse!”
Tikumayang’ana pa izo, tinakhoza kuwona chifukwa chimene bukhu la Yobu limanena kuti ngakhale ngati madzi mu mtsinje akula akumathira pa kamwa pa nyama yaikuluyi sinjenjemera. Mutu wake wokha ungalemere kufika ku tani limodzi!—Yobu 40:23.
Zidikha za Serengeti
Tinapita cha kum’mwera ku Tanzania, tikumaimirira pa Ngorongoro Crater wodabwitsa, malo akuya a mamailosi 12 mu ukulu odzala ndi nyama za m’nkhalango. Pa malo ake amadzi akuya, mitsinje ya alkaline inawoneka chapatali ngati kuti iri ndi mtambo wofiirira pang’ono pamwamba pake. Iwo unadzazidwa ndi amfulagombe oŵerengeka, a unyinji wochepa ndi ofiirirako. Iwo ankatulutsa chiwunda ndi phokoso pamene ankayenda monyada mu unyinji, miyendo yawo ikumawoneka monga nkhalango yadzaza ndi udzu wofiira kwambiri ukumakhota ndi kuwongokera.
Zidikha za Serengeti za kumpoto cha kumadzulo kwa crater ziri nyanja zosalala za udzu wokhawokha zokhala ndi zisumbu za apo ndi apo zotchedwa kopjes. Magulu akulu, a miyala yachilengedwe, zisumbu za kopjes zokhala ndi nyama zazing’ono zaubweya zokhala m’miyala ndi abuluzi okongola. M’nkhalango yapafupi tinawona a dik-dik, nyama za mapaundi khumi, zotalika phazi limodzi zomwe kudzichinjiriza kwawo kokha kuli kudziŵa kubisala.
Tinapita mu gulu la wildebeest lomwe linadzala kufikira ku malekezero ku mbali zonse. Izo zinkasonkhana pamodzi kaamba ka ulendo wawo, zikumaimba ndi kuyenda uku ndi uko mosangalatsa. Ndinamwetulira pa chiŵerengero chawo chachikulucho ndi phokoso, ndipo ndinalingalira, ‘pano potsirizira pali nyama imene sinachotsedwepo ndi mtundu wa anthu!’
Wotitsogolera wathu anasangalatsidwa. “Padzakhala mamiliyoni aŵiri a izo chaka chino, sindikukaikira. Tsopano lino izo zikupita kulinga ku malo komwe kukugwa mvula chapafupi—izo zingakhoze kuzindikira kumodzi mamailosi 30 kutali!”
Mochedwa madzulo amodzi mu chidikhacho, tinkawona mbalame, tikumakondweretsedwa kuti tinawona chifupifupi 200 zosiyanasiyana, zonsezo zokongola.
“Sichingakhale chowona!” mlongo wanga anazizwitsidwa, akumaloza. Ndinatembenuka kuti ndiyang’ane, ndikumayembekezera kuti ndidzawona mbalame, ndipo m’malomwake ndinawona nyalugwe, atatambalala mwaufulu mu nthambi za mtengo wa acacia osati mayadi 20 kutali.e Iye anangotinyalanyaza mopepuka ndi kuyasamula, akumawoneka kukhala wopanda mantha kotheratu. Mikango nayonso ingakhoze kukwera mitengo, koma iri yolemera kuwirikiza kaŵiri kuposa kuja kwa nyalugwe, iyo imangozichita kokha mwakamodzikamodzi, kuthawa kutentha ndi ntchentche. Mikango yomwe tinawona m’mitengo inawoneka kukhala ya uve ndi ya mantha m’mwamba mmenemo chakuti tonsefe tinaseka. Koma nyalugwe amadya, kugona, ndipo kwenikweni kukhala m’mitengo.
“Iye ali wowopsya, kodi sitero?” Wotitsogolera wathu analongosola tero kudzimva kwake. Nchachisoni kunena kuti, iye anapitirizabe, “odzacheza ambiri amabwerera kunyumba popanda kuwona nyalugwe masiku ano. Iwo amaphedwa kwakukulu ndi akupha nyama popanda lamulo kaamba ka chikopa chawo chokongola.” Makamera athu onse anatulutsa phokoso la kujambula ndi kung’anima pamene dzuŵa linalowa m’chidikha. Sindidziŵa ngati nyalugwe amene uja adakali ndi moyo lerolino, kokha miyezi yoŵerengeka pambuyo pake.
Kodi Zidzakhalako kaamba ka Ana Athu
Pamene ndege yathu inanyamuka kupita kumudzi, ndinayang’ana pansi pa Serengeti ndikumva chisoni. Chinali chachisoni, kaamba ka chinthu chimodzi, kuchoka pa malo okongola amenewa. Ndinachida kotheratu. Koma nkhani zosiyanasiyana za maulendo owona zinyamawo, nazonso, zinali zomvetsa chisoni.
Mwachitsanzo, liŵiro la cheetah, minyanga ya njovu, khosi la nswala, ndi mikhalidwe ya cholengedwa chirichonse chimene tinawona, zonsezo zimalozera ku Mpangi yemwe amasanganiza kukongola ndi kufunika, kupanga ndi kugwira, m’ntchito yake yonse. Apangi aumunthu amalemekezedwa pamene ntchito yawo yakhoza ngakhale kufikira pa mtundu wa kulinganizika kumeneko. Komabe Mpangi wa ntchito zazikulu zimenezi zosakhoza kuyerekezeredwa samazindikiridwa nkomwe monga mpangi. M’malomwake, ulemu umapatsidwa ku magwero a khungu omwe achititsa ngozi mabiliyoni angapo, otchedwa chisinthiko. Nchachisoni.
Choipabe, ntchito zenizenizo zikuwonongedwa mokhazikika, mosasamala. Mosasamala kanthu za zoyesayesa zolimba za awo omwe amagwira ntchito mwakalavulagaga kuzisungirira izo, mafunso ovuta amaumirirabe ponena za nyama za m’nkhalango za ku Africa. Kodi zolengedwa zimenezi zingakhoze kupulumuka kuphedwa kopanda lamulo ndi kudidikiza kwa kuzimiririka kokhazikika kwa malo okhalako? Kodi zidzakhalako kaamba ka ana athu, adzukulu athu?
Mafunso ovuta, ndithudi. Ndipo komabe, kwa anthu olingalira bwino, mafunso oterewa sangakhoze kuthandiza koma kutsogolera ku funso lina lofunika kwambiri: Kodi Mpangi wanzeru wa dziko lapansi ndi zolengedwa zake zonse adzangoimirira ndi kupenyerera likuwonongedwa lonselo? Ayi; iye amalonjeza “kuwononga owononga dziko.” Mwaubwinobe, iye amalonjeza nthaŵi mwamsanga pambuyo pake pamene mtundu wa anthu udzakhala pa mtendere ndi nyama.—Chivumbulutso 11:18; Yesaya 11:1-9.
Inde, Mlengi amapereka mayankho osangalatsa, odalirika ku mafunso athu ovuta kwambiri. Kulingalira ponena za malonjezo ake kumathetsa kumva chisoni kwanga pa kusakazidwa kwa nyama za m’nkhalango ya mu Africa. Osati kokha kuti zikali kumeneko tsopano; izo zidzakhala kumeneko m’nthaŵi za mtsogolo.—Yothandiziridwa.
[Mawu a M’munsi]
a 1 mi = 1.6 km.
b 1 ft = 0.3 m.
c 1 lb = 0.5 kg.
d 1 a. = 0.4 ha.
e 1 yd = 0.9 m.