Chikhulupiriro Chawo Chisuntha Mapiri
NDI mutu wankhani umenewo nyuzipepala ya ku Buenos Aires ya tsiku ndi tsiku ya Crónica, ya December 7, 1990, inachitira lipoti msonkhano wa Mboni za Yehova umene unachitidwira m’mabwalo amaseŵera a mpira wachitanyu a River Plate ndi Vélez Sarsfield. Ndithudi, chinali chikhulupiriro cholimba chomwe chinasonkhezera pafupifupi nthumwi zachilendo 6,000 zochokera ku maiko oposa 20 kupita ku Argentina kukagwirizana ndi zikwi makumi ambiri za abale awo a ku Argentina kaamba ka Msonkhano wawo wakuti “Chinenero Choyera.” Chiwonkhetso chimenechi chinaphatikizapo mipingo ingapo yakumaloko ya Mboni za Chikorea. Nthumwi zachilendozo zinachokera ku Briteni, Canada, Chile, Japan, Spanya, United States (kuphatikizapo Alaska), ndi maiko ena ambiri. Kodi nchiyani chinaŵasonkhezera? Chikhumbo chawo chakuchirikiza msonkhano wachiŵiri wamitundu yonse wochitidwira ku Argentina.
Kuperekedwa kwa Beteli Yatsopano
Koma zochitika zazikulu zachikhulupriro zinachitika nthaŵi ya msonkhanowo isanafike. Mu October ofesi yanthambi yatsopano ya ku Argentina ya Asociación de los Testigos de Jehová inaperekedwa ndi mlendo Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Nyumba yokhalamo yosanja yatsopanoyo inamangidwa ndi antchito odzifunira amitundu yonse 259 ndi 690 a ku Argentina. Beteli, kapena “Nyumba ya Mulungu,” yokhala m’dera lochingidwa ndi mitengo la Buenos Aires, iri ndi zipinda zokhalamo zokwanira 129 ndi chipinda chodyeramo anthu okwanira 300. Pokhala ndi Mboni zoposa 84,000 mu Argentina ndi kuthekera kwa chiwonjezeko chachikulu, palibe kukaikira kuti nyumba yanthambi yatsopanoyi idzazala posachedwapa.
“Mboni za Yehova ndi Chinenero Choyera”
Mutu wa msonkhano wamitundu yonse wakuti “Chinenero Choyera” unachititsa chidwi ambiri, kuphatikizapo oimira bungwe loulutsa nkhani. Nyuzipepala ya Crónica inasonyeza mutu wankhani uli pamwambapa ndipo inagwira mawu tanthauzo la “chinenero choyera” monga momwe linalongosoledwera ndi wolankhula kuti: “Ndicho kumvetsetsa kolondola kwa chowonadi chonena za Mulungu ndi chifuno chake kaamba ka dziko lapansi ndi anthu, chopezedwa m’Baibulo . . . Pamene wina aphunzira kulankhula chinenero choyera, pamenepo njira yake ya kulingalira, kulankhula kwake, ndi mayendedwe ake zimazikidwa pa kuzindikira Mulungu monga Mulungu wowona yekha.”
Buenos Aires, likulu la boma ndi mzinda womakulakula wokhala ndi anthu oposa mamiliyoni khumi, unadziŵitsidwa bwino lomwe za msonkhano komweko. Mkati mwa nyengo ya masiku asanu ndi limodzi, masitesheni a wailesi ya 40-second ndi TV ovomerezedwa mwalamulo, anaulutsa chochitikachi kwaulere. Programu ya pa Loŵeruka yokhala ndi ubatizo wa Mboni zatsopano inakopa amtola nkhani. Maiŵe 3 owonekera ku gulu anakhazikitsidwa kothera kulikonse kwa mabwalo amaseŵera onse aŵiriwo, koma ngakhale maiŵe 12 anali osakwanira kumaliza ubatizowo nthaŵi idakalipo kaamba ka programu ya masana. Chotero maiŵe a ku Bwalo Lamaseŵera la River Plate anasinthidwa kuti asawonekere. Ku River Plate, anthu 1,363 anabatizidwa ndipo ku Vélez Sarsfield, anthu 748 anabatizidwa, onse pamodzi 2,111! Mutu wankhani mu Crónica unati: “Chisonyezero China Chodabwitsa cha Chikhulupiriro mu River ndi Vélez—Mboni Zibatizidwa.” Chiŵerengero cha opezekapo pamisonkhano iŵiriyo chinali choposa 67,000.
Kukongola Kwamitundu Yonse
Pamene wina ankayenda pakati pa gulu lokongolali, kusiyana kwakuthupi kwa fuko ndi makhalidwe kunali kowonekera. Panali mlongo wa ku Argentina amene anali kumwa yerba maté wake, tii wopsontha kupyolera m’bombilla, kapena mpaipi wachitsulo, kuchokera m’chikho chapadera chamtengo. Pakati pa ochokera ku Spanya okwanira 800 panali alongo ovala malaya okongola a ku dzikolo. Gulu la ochokera ku Japan okwanira 900 linaphatikizapo akazi ena ovala makimono amwambo. Nthumwi yochokera ku Mexico inavala suti yakuda ndi chipewa chotambalala cha ku Mexico. Komabe, mosasamala kanthu za kusiyana kwakunja kumeneku, kugwirizana kwawo kwauzimu kunali kowonekera bwino kwa onse. Pakutha kwa msonkhanowo, ambiri anali kusinthana zinthu zokumbukirana—mabaji a msonkhano, mapeni, mapostcard—chirichonse chimene chikatumikira monga chokumbutsa cha chochitika chokongolachi.
Mzimu wamsonkhanowo unasefukira ku mabwalo andege. Ichi chinali chowonekera makamaka ku Miami, Florida, U.S.A, kumene magulu ambiri anakumana pamene ankasintha ndege. Pobwerera kuchokera ku Buenos Aires, gulu lalikulu lochokera ku United States linakumana ndi gulu lochokera ku Japan, lomwe linkapita ku Mexico. Posachedwa, apaulendo a ku Amereka onse anali kuloŵetsedwa m’kukambitsirana ndi anzawo a ku Japan osangalala. Unyinji wotsala m’malowo unadabwa ndi kuchita chidwi ndi zimene zinali kuchitika. Zinali Mboni zomwe zinali kusonyeza mzimu wa “chinenero choyera”!
Programu yamsonkhano ndi kuyanjana kwamitundu yonse kunali kwapadera kwambiri kotero kuti pamene msonkhanowo unatha pa Sande, palibe aliyense anafuna kuchoka pa mabwalo amaseŵerawo. Mitundu yosiyanasiyanayo chapamodzi inayamba kuimba nyimbo za Ufumu m’zinenero zawo zosiyanasiyana popanda ziŵiya zoimbira namapukusirana tinsalu tominira. Izi zinapitiriza kwapafupifupi ola limodzi osonkhanawo asanapite kwawo pomalizira pake. Mtola nkhani wojambula zithunzithunzi wosatengeka maganizo mokhweka wa ku Argentina ananena kuti: “Zimenezi sizinachitikepo m’Argentina . . . chisangalalo choterocho ndi chikondano choterocho!”
[Zithunzi patsamba 15]
Oposa 67,000 anapezekapo pa Misonkhano ya Mboni za Yehova yakuti “Chinenero Choyera” ku Buenos Aires, December 6-9, 1990
[Zithunzi patsamba 16]
Nyumba yosanja yanthambi yatsopano ya ku Argentina njokonzekera kutumikira Mboni zoposa 84,000