Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingasiye Motani Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri?
“Ndinanyalanyaza zonse zimene makolo anga ananena,” Ann akuulula motero.a “Ndinali wopanduka ndipo ndinayamba kuwanyengeza. Ndinkawauza kuti ndinali kupita kukagula zinthu, koma kwenikweni ndinali kupita kukaonana ndi mnyamata.”
ANN anali kukhala ndi moyo wapaŵiri, ndipo posapita nthaŵi anali kunyalanyaza osati makolo ake okha komanso chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Mwaona nanga, Ann anali kugonana mtseri ndi bwenzi lake lachinyamata. Iye akukumbukira kuti: “Ndinayesa kunyalanyaza Yehova kotheratu.” Komabe, posapita nthaŵi anayang’anizana mwachindunji ndi chowonadi chosautsa chakuti ‘chimene anthu achifesa, chimenenso adzachituta.’ (Agalatiya 6:7) Ann anatenga pathupi. “Ndimakonda mwana wanga ndi mtima wanga wonse,” iye akutero, “koma palibe aliyense amene ayenera kugwera m’zimenezi. Osati wosakwatiwa. Osati yekha.”
Kodi inu mwanjira ina mwagwidwa mumsampha wa kukhala ndi moyo wapaŵiri—mukumabisa amene muli kwa makolo anu ndi Akristu anzanu? Mwinamwake mumangotaya nthaŵi yochuluka muli ndi mabwenzi ena akusukulu amene mudziŵa kuti makolo anu sangawavomereze. Kapena mwinamwake mwachita choipa chachikulu, chonga kusuta fodya, kuledzera, kapena kugonana musanaloŵe muukwati. Mulimonse mmene zingakhalire, monga momwe zinachitikira kwa Ann, patapita nthaŵi padzakhala zotsatirapo zake zowopsa.b
Ngakhale zili choncho, achichepere ena samalola konse chowonadi chimenechi kuwachotsa panjira yawo yachipanduko. Ali ngati munthu amene amadziyang’ana m’kalirole “naiŵala pompaja nali wotani.” (Yakobo 1:23, 24) Tikhulupirira kuti inu muli wosiyana. Mwinamwake mwayamba kale kudzipenda mosamalitsa—ndipo simukukonda zimene mukuona. Mukufuna kusintha. Mwaona kufunika kwa kusintha. Funso nlakuti, kodi mumasintha motani?
Kulapa—Sitepe Loyamba
Choyamba, muyenera kupanga chosankha chotsimikizirika cha kusintha. Machitidwe 3:19 imafulumiza kuti: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya [Yehova, NW].” Komabe, kulapa sikumangosonkhezeredwa chabe ndi maganizo. Kulapa kumatanthauza “kuchita chisoni, kuipidwa, kapena kulaswa mtima, ndi zimene munthu wachita.” Wolemba Baibulo Yakobo analangiza kuti: “Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa [Yehova, NW].” (Yakobo 4:9, 10) Kodi mungamve chisoni motani pa chinthu chimene mwakhala mukusangalala nacho kufikira tsopano? Ganizirani za kuipa kwake. Ganizirani za mmene chapwetekera Mulungu. Ganizirani za mavuto amene njira yanu ya moyo yamtseri yakudzetserani ndi mabodza amene mwanena kuti mubise njirayo. Kumbukirani kuti Mulungu amanyansidwa ndi ochita chinyengo! (Salmo 5:6) Kusinkhasinkha mfundo zimenezi kungakuthandizeni kukana khalidwe loipa mwamaganizo ndi mtima womwe.
Komabe, kungomva chisoni ndi zimene mukuchita sikuli kokwanira. Mnyamata wina wotchedwa Robert, amene anali ndi chizoloŵezi chamtseri cha kumwa anamgoneka, akuvomereza kuti: “Ndinali wachisoni. Ndinadziŵa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Chikhalirechobe, ndinapitiriza kukhala ndi moyo wapaŵiri.” Chotero kuchitapo kanthu molimba mtima nkofunika! Pa 2 Mbiri 7:14, Mulungu anati ngati ochimwa ‘akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope [yake], nakatembenuka kuleka njira zawo zoipa, pamenepo [iye mwiniyo] akamvera m’mwamba, ndi kukhululukira choipa chawo.’
‘Kufuna nkhope ya Mulungu’ kumatanthuza kumfika m’pemphero, kuulula cholakwa chanu, ndi kupempha chikhululukiro. Kuchita zimenezi kungakhale kovuta, koma mosakayikira mudzapeza mpumulo waukulu chifukwa cha kuchita motero. Wamasalmo anati: “Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; . . . Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.”—Salmo 32:3-5.
Kuuza Makolo Anu
Munthu wina afunikira kudziŵa za mavuto anu. Koma kodi ndani? Wachichepere wina wotchedwa Brian akuvomereza kuti: “Chimodzi cha zolakwa zanga zazikulu chinali kupereka mavuto anga kwa otchedwa mabwenzi mmalo mopita kwa amayi anga Achikristu. Koma ndinali wamantha kulankhula nawo chifukwa cha kuganiza kwanga za mmene akachitira, chotero ndinatembenukira kwa mabwenzi anga, amene anandichititsa kutalikirana kwambiri ndi chowonadi.” Musachite cholakwa chimodzimodzicho. Patsani mtima wanu makolo anu owopa Mulungu. (Yerekezerani ndi Miyambo 23:26.) Ali ndi kuyenera kwa kudziŵa zimene mwakhala mukuchita. Mutu 2 wa buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza uli ndi malingaliro ambiri a mmene mungafikire makolo anu pankhaniyi.c
Mwachibadwa, iwo sadzakhala okondwa ponena za kuwanyengeza kwanu. Koma makolo nthaŵi zonse ali ndi chikondi chachikulu pa ana awo. Wolemba Clayton Barbeau akunena kuti: “Iwo sadzakukanani chifukwa chakuti mwachita cholakwa kapena mwaloŵa m’vuto lina lake. Achichepere atenga pathupi, ayambukiridwa ndi nthenda yopatsirana mwa kugonana, akhala ndi vuto lauchidakwa kapena la anamgoneka kapena kuloŵa m’mavuto ena naganizira kuti makolo awo adzachita kakasi ndi kuipidwa, kukwiya, ndi kusokonezeka maganizo. Koma pamene auza makolo awo, amangoona kuti akuwakupatira kapena kuwagwira papheŵa, nati, ‘Ulidi m’vuto, ndipo tidzangofunikira kuona zimene tingachite kukuchotsamo.’” Inde, pamene kuchita kakasi kwawo ndi mkwiyo wawo uchepa, makolo ochuluka amayesa kuwachirikiza. Zimenezi zimakhala choncho motani nanga pamene makolo ali owopa Mulungu! Nkhaŵa yawo yaikulu iyenera kukhala, osati kukunyazitsani kapena kukuvulazani, koma kuwongolera zinthu. (Yerekezerani ndi Yesaya 1:18.) Pankhani imeneyi iwo angalinganizenso kuti mukakambitsirane ndi akulu a mpingo.—Yakobo 5:14, 15.
Zoona, pangakhale chilango choyenerera chochokera kwa makolo anu chimene mungafunikire kupirira ndipo mwinamwake ziletso zolimbirapo. Koma zimenezi zingakuthandizeni kwenikweni kupeŵa kuyambiranso njira zanu zakale. Ndiponso, kukambitsirana zinthu ndi makolo anu ndi kuona chisamaliro chawo chachikondi mosakayikira kungasinthe mmene mumawaonera. Kufikira tsopano lino, mwina mwakhala mukuipidwa ndi malamulo awo ndi ziletso. Mtsikana wina wotchedwa Paulette akuvomereza kuti: “Nkovuta kulandira uphungu ndi zitsogozo zimene timapatsidwa ndi makolo athu. Koma ndafikira pakuzindikira kuti zimenezi zilipo kaamba ka phindu lathu ndi chimwemwe chathu chokhalitsa.”
Kusintha Mayanjano Anu
Kaŵirikaŵiri wachichepere samakhala ndi moyo wapaŵiri payekha. Mwinamwake amsinkhu wanu angakhale anakusonkhezerani kupanduka! Kuti mupeŵe kuyambiranso moyo wamtseri, mudzafunikira kusintha mayanjano anu. Wamasalmo anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika.” (Salmo 26:4) Kuthetsa maubwenzi anthaŵi yaitali nkovuta. Mofanana ndi wamasalmo mungafunikire kupemphera kuti: “Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.” (Salmo 43:1) Chitani mogwirizana ndi pemphero limeneli mwa kuuza oyanjana nawo anu anthaŵi yaitali kuti mwasintha ndipo muli wotsimikiza kuchita chimene chili chabwino. Mmalo mwa kukhala wophunzira wamtseri wa Yesu, uzani ena za chikhulupiriro chanu. (Yerekezerani ndi Yohane 19:38.) Kaŵirikaŵiri, oyanjana nawo oipa adzapeza anzawo ena mwamsanga.
Ndiyeno, mufunikira kupeza mabwenzi abwino mmalo mwa mayanjano oipa. Kodi achichepere owopa Mulungu akusoŵeka? Pamenepo ganizirani za mneneri Yeremiya, amene anati: “Sindinakhala m’msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu.” (Yeremiya 15:17) Kungakhale bwino kwa inu kukhala panokha kuposa kupitirizabe kuyanjana ndi achichepere amene adzakufooketsani mwauzimu. Komabe, nthaŵi zambiri, mabwenzi enieni angapezedwe ngati muyesayesa zolimba. Mwachitsanzo, Tammy anayamba kuyanjana ndi msuwani wake amene anali mlaliki wanthaŵi yonse. “Tinakondana kwambiri,” Tammy akukumbukira motero. “Pamasiku amene sindinali kusukulu, ndinkapita naye m’ntchito yolalikira. Kutereku kunandithandiza kupanga masinthidwe m’moyo wanga.”
Koma “chitetezo chabwino koposa,” akutero wachichepere wina wa ku Germany, “ndicho chikumbumtima chabwino, chimene chimakhalapo chifukwa cha unansi wabwino ndi Yehova Mulungu.” Mtsikana wina wachichepere amene anayamba kukhala ndi moyo wapaŵiri akuvomereza kuti: “Sindinakulitse konse unansi wabwino ndi Atate wanga, Yehova.” Kupyolera mwapemphero ndi phunziro laumwini, anayamba kusintha zinthu. “Tsopano ndili ndi unansi ndi Yehova umene palibe aliyense amene angaulande,” iye akutero monyadira. Nanunso mungakhale ndi ubwenzi wabwino wotero ndi Mulungu. Iye adzakutsogozani ndi kukuchirikizani, ngakhale pamene muvutika kusintha njira zanu zakale. Salmo 37:24 limanena za mtumiki wokhulupirika wa Mulungu kuti: “Angakhale akagwa, satayikiratu: pakuti Yehova agwira dzanja lake.” Inde, mothandizidwa ndi Yehova, mungasiye kukhala ndi moyo wapaŵiri.
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
b Onani nkhani za “Achichepere Akufunsa . . . ” m’kope lathu la January 8, 1994.
c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
“Ndinayesa kunyalanyaza Yehova kotheratu”
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Muyenera kupanga chosankha chotsimikizirika cha kusintha
[Chithunzi patsamba 13]
Fotokozerani mabwenzi anu anthaŵi yaitali kuti mwasintha ndipo simudzagwirizananso nawo pakuchita zoipa