Zozizwitsa za Kubadwanso kwa Moyo Zifotokozedwa
CHIMODZI cha zifukwa zokanira chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo nchakuti unyinji wa anthu pa dziko lapansi sumakumbukira konse kuti unayamba wakhalako. Ndiponso, samaganizira nkomwe kuti angakhale atakhala ndi miyoyo yapapitapo.
Nzoona kuti nthaŵi zina timakhala ndi lingaliro lodabwitsa la kuzindikira munthu amene timakumana naye nthaŵi yoyamba. Nyumba inayake, tauni, kapena malo okongola zingaonekere kukhala zodziŵika kwa ife, ngakhale kuti tikudziŵa kuti ndiko kuyamba kupezeka kumeneko. Komabe, zimenezi zingafotokozedwe popanda kutembenukira ku chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo.
Mwachitsanzo, malo ena m’madera otalikirana kwambiri angakhale ofanana mwanjira ina yake, kotero kuti pamene tiona malo atsopanowo, tingalingalire kuti tinayamba tafikako, ngakhale kuti sitinatero. Nyumba zambiri, maofesi, masitolo, matauni, ndi malo okongola kumbali zina za dziko zimakhala zofanana ndi zinthu zofanana nazo kumalo ena. Kuoneka kwawo kukhala zofanana ndi zimene tinaonapo kale sikuli umboni wakuti tinafika kumalo amenewo m’moyo wapapitapo. Amangofanana ndi malo amene tidziŵa.
Ndi mmenenso zilili ndi anthu. Ena n’ngofananadi m’kaonekedwe, ngakhale kuoneka ngati mapasa. Munthu angakhale ndi mikhalidwe imene imatikumbutsa za munthu wina wamoyo kapena ngakhale amene anafa. Koma anthuwo tinawadziŵira m’moyo uno, osati m’kukhalapo kwapapitapo. Kufanana m’kaonekedwe ndi m’maumunthu sikumatanthauza kuti anthu ameneŵa tinawadziŵira m’moyo wapapitapo. Mosakayikira tonsefe panthaŵi ina tinayesa munthu wina kukhala uja amene timamdziŵa. Koma anthu aŵiriwo akhala ndi moyo pa nthaŵi imodzimodziyo imene inuyo mwakhalapo ndi moyo ndipo osati m’moyo wapapitapo. Si chifukwa cha kubadwanso kwa moyo ayi.
Chisonkhezero cha Kugoneka Tulo
Ngakhale zoonedwa pamene wina agonekedwa tulo zingafotokozedwe popanda kutembenukira ku chiphunzitso cha kubadwanso kwa moyo. Chikumbukiro chathu chobisika ndicho nkhokwe ya chidziŵitso yaikulu kwambiri koposa imene tingayerekezere. Chidziŵitso chimaloŵa m’nkhokwe imeneyi kupyolera m’mabuku, magazini, TV, wailesi, ndi kupyolera m’zochitika zina ndi zooneka.
Chochuluka cha chidziŵitso chimenechi chimasungidwa m’malo ena obisika a chikumbukiro chathu chobisika chifukwa chakuti sitimachigwiritsira ntchito mwachindunji kapena panthaŵi yomweyo. Chikumbukiro chathu chobisika chili monga ngati mabuku a m’laibulale amene sakufunika kwambiri panthaŵiyo ndipo chotero aikidwa pa shelufu yapadera.
Komabe, atagonekedwa tulo, chikumbukiro cha munthuyo chimasinthidwa kotero kuti zoiŵalidwa zimakumbukika. Anthu ena amaona zimenezi kukhala za m’moyo wapapitapo, koma zimangokhala chabe zochitika za m’moyo wapanthaŵi ino zimene tinali titaiŵala kwa kanthaŵi.
Komabe, pali zochitika zingapo zimene zingakhale zovuta kwambiri kuzifotokoza mwanjira yachibadwa. Chitsanzo ndicho pamene munthu ayamba kulankhula “chinenero” china atagonekedwa tulo. Nthaŵi zina chinenerocho chimamveka, koma kaŵirikaŵiri sichimatero. Awo amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo anganene kuti chimenechi ndi chinenero chimene munthuyo ankalankhula m’moyo wapapitapo.
Komabe, nkodziŵika bwino lomwe kuti kulankhula m’zotchedwa malilime kumachitikanso pamene anthu ali mumkhalidwe wamatsenga kapena wotengeka maganizo ndi zachipembedzo. Awo amene zimenezo zimawachitikira ali otsimikiza kuti zimenezo sizili chifukwa cha moyo wapapitapo koma kuti akusonkhezeredwa ndi mphamvu yosaoneka m’moyo uno.
Malingaliro amasiyanasiyana ponena za chimene mphamvuyo ili. M’chilengezo chochitidwa mogwirizana cha Fountain Trust ndi Church of England Evangelical Council, munanenedwa za kulankhula malilime kuti: “Tikudziŵanso kuti chozizwitsa chofananacho chingachitike mosonkhezeredwa ndi matsenga/ziŵanda.” Chotero kunena kuti zozizwitsa zotero zili umboni wakuti tinakhalako ndi moyo wapapitapo kungakhale kungofulumira kudzinyengeza.
Zoonedwa Pamene Munthu Atsala Pang’ono Kufa
Pamenepa, bwanji ponena za zoonedwa pamene munthu atsala pang’ono kufa zimene anthu amanena kuti anaziona? Zimenezi zaonedwa ndi ena kukhala umboni wakuti munthu ali ndi moyo umene umapitiriza kukhalako pambuyo pa imfa ya thupi. Koma zoonedwa zimenezo zimafotokozedwa bwino lomwe mwanjira zambiri zachibadwa.
M’kope la March 1991 la magazini asayansi Achifalansa otchedwa Science & Vie, mbali zosiyanasiyana za zoonedwa pamene munthu atsala pang’ono kufa zimatchedwa “mkhalidwe wa kubwebweta wa aliyense” umene wakhala wodziŵika kwa nthaŵi yaitali. Zoonedwa zofanana ndi zimenezo sizimangochitika chabe kwa awo amene amakhala mumkhalidwe wotsala pang’ono kufa. Zingachitikenso chifukwa cha “kutopa, manthunthumira, kugwidwa ndi khunyu, ndi kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka.”
Woyambitsa opaleshoni ya minyewa yaubongo, Wilder Penfield, amene anachita opaleshoni pa odwala khunyu omwe anachititsidwa dzanzi pa malo amodzi, anapeza zokondweretsa. Anapeza kuti mwa kukhudza mbali zosiyanasiyana za ubongo ndi nsambo yamagetsi, anachititsa wodwalayo kumva ngati kuti ali kunja kwa thupi lake, akumayenda m’ngalande, ndi kukumana ndi achibale akufa.
Umboni wosangalatsa pa nkhaniyi n’ngwakuti ana amene aonapo zinthu pamene iwo atsala pang’ono kufa amakumana, osati ndi achibale awo akufa, koma anzawo akusukulu kapena aphunzitsi—awo amene akali amoyo. Zimenezi zimasonyeza kuti zoonedwa zotero zimagwirizana ndi chitaganya chakutichakuti. Zimene zimaonedwazo nzogwirizana ndi moyo wapanthaŵi ino, osati ndi kanthu kena pambuyo pa imfa.
Dr. Richard Blacher akulemba m’magazini akuti The Journal of the American Medical Association kuti: “Kutsirizika, kapena kuvutika ndi mkhalidwe wowopsa wakuthupi, kuli njira yofera; imfa ndi mkhalidwe.” Mwachitsanzo, Blacher akulankhula za munthu amene kwa nthaŵi yoyamba akuuluka pandege kuchokera ku United States kupita ku Ulaya. “Kuuluka pandegeko si[ndiko kukhala ku] Ulaya,” akulemba motero. Mlendo amene akupita ku Ulaya, koma amene ndege yake itembenuka nibwerera patangopita mphindi kuyambira pamene yanyamukira, sangauze anthu zambiri ponena za ku Ulaya monga momwe aliyense amene anali atakomoka sangauzire aliyense ponena za imfa.
Awo amene anatsala pang’ono kufa, m’mawu ena, sanali konse akufa. Kanthu kena kanawachitikira pamene anali akali ndi moyo. Ndipo munthu amakhalabe wamoyo ngakhale m’timphindi tingapo asanamwalire. Iwo anatsala pang’ono kufa koma anali asanafebe.
Ngakhale awo amene mtima wawo unaleka kugunda kwakanthaŵi natsitsimuka sangathe kukumbukiradi kalikonse kuyambira panthaŵi ya kukomokako pamene akananenedwa kukhala “akufa.” Ngati amatero, angangokumbukira zimene zinachitika m’nthaŵi imene kuleka kugunda kwa kanthaŵiko kunatsala pang’ono kuchitika, osati kutachitika.
Pafupifupi nthaŵi zonse zofalitsidwa za zoonedwa munthu atatsala pang’ono kufa zimasonyezedwa kukhala zabwino, ngakhale kuti nkwachidziŵikire kuti pamakhalanso zoonedwa zoipa. Catherine Lemaire, dokotala wa nthenda zamaganizo akufotokoza zimenezo motere: “Awo amene sanakhalepo ndi zimene anaona [pamene anatsala pang’ono kufa] zoyenerana ndi mtundu wosankhidwa ndi IANDS [International Association for Near-Death Studies] samafuna konse kusimba nkhani yawo.”
Sitimakumbukira
Choonadi nchakuti sitinakhalepo ndi moyo wina kusiyapo umene tili nawo tsopano, ngakhale moyo wapapitapo kapena moyo wapambuyo pa imfa. Nchifukwa chake, sitimakumbukira zinthu zilizonse kusiyapo moyo umene takhala nawo basi.
Awo amene amakhulupirira kubadwanso kwa moyo amanena kuti tanthauzo lenileni la kubadwanso ndilo kupeza mwaŵi wina wa kuwongolera mkhalidwe wathu. Ngati tinakhaladi ndi miyoyo papitapo, koma nkuiiŵala, kuiŵala koteroko kungakhale kulemala kowopsa. Timapindula ndi zolakwa zathu mwa kuzikumbukira.
Ndiponso, awo amene amachirikiza yotchedwa njira yochiritsira ya kubadwanso kwa moyo amaganiza kuti mungachite bwino lomwe ndi mavuto amakono ngati, mwa kugonekedwa tulo, mungakumbukire miyoyo yanu yapapitapo. Chiphunzitsocho chimanena kuti timabadwanso kuti tiwongolere kanthu kena, komabe taiŵala zimene kanthu kenako kali.
Kuiŵala m’moyo wamakono kumalingaliridwa kukhala kulemala. Ziyenera kukhaladi choncho m’nkhaniyi. Kutsutsa mwa kunena kuti kuiŵala koteroko sikuli kanthu, popeza kuti ndi anthu abwino okha amene amabadwa monga anthu, sikuli chigomeko chanzeru m’nthaŵi ino pamene kuipa kwafalikira padziko lonse koposa ndi kalelonse. Ngati ndi anthu abwino okha amene amabadwanso monga anthu, kodi anthu onse oipa anachokera kuti? Kodi sipayenera kukhala anthu oipa omacheperachepera? Choonadi nchakuti: Palibe aliyense, wabwino kapena woipa, amene amabadwanso kuyamba moyo wina monga munthu kapena chinthu china chilichonse.
Komabe, munganene kuti, ‘Kodi kubadwanso kwa moyo sikuli chiphunzitso cha m’Baibulo?’ Tiyeni tipende funso limeneli m’nkhani yotsatira.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Chikumbukiro chathu chobisika chili ngati laibulale ya chidziŵitso chimene chaikidwa padera koma chimene chingadzakumbukiridwe mtsogolo
[Mawu Otsindika patsamba 22]
“Imfa ndi mkhalidwe,” si njira yofera ayi.—Dr. Richard Blacher mu The Journal of the American Medical Association