Lingaliro la Baibulo
Nkulamuliriranji Mkwiyo Wanu?
CHIYAMBI chake chinasonyezeratu kuti zinthu sizidzakhala bwino mtsogolo. “Tsopano poti ine ndine mutu m’nyumba muno, suyenera kumandichititsa manyazi chifukwa cha kubwera kwako mochedwa,” anatero John kukalipira mkazi wake watsopano Ginger.a Kwa mphindi zoposa 45 anali kulalata uku akumukakamiza kuti asachoke pasofa. Kulankhula konyozana linali khalidwe m’banja mwawomo. Zachisoni, mkwiyo wa John unakulirakulira. Anali kumenyetsa zitseko, kumenya thebulo la m’khichini, ndi kuyendetsa galimoto mosasamala uku akumenya chiwongolero cha galimotoyo, choncho akumaika moyo wa ena pangozi.
Mwatsoka, mosakayika konse mukudziŵa bwino kuti zoterezi zimachitika kaŵirikaŵiri. Kodi kukwiya kwa munthu ameneyu kunali bwino kapena kunali konyanyira? Kodi mkwiyo uliwonse ndi woipa? Kodi ndi liti pamene mkwiyo umakhala wosalamulirika? Ndi liti pamene umafika poipitsitsa?
Mkwiyo wolamulirika ungakhale wabwino. Mwachitsanzo, mkwiyo wa Mulungu unayakira midzi yamakhalidwe oipa ya Sodomu ndi Gomora. (Genesis 19:24) Chifukwa ninji? Chifukwa anthu a m’midzi imeneyo analoŵerera m’makhalidwe achisembwere chachiwawa ndiponso chonyansa, zimene zinali zodziŵika bwino m’dera lonselo. Mwachitsanzo, pamene amithenga aungelo anazonda munthu wolungamayo Loti, gulu la anyamata pamodzi ndi nkhalamba zomwe anayesayesa kuti agwire alendo a Loti ndi kugona nawo. Yehova Mulungu anakwiya molungama chifukwa cha chiwerewere chawo chachikulucho.—Genesis 18:20; 19:4, 5, 9.
Monga Atate ake, Yesu Kristu munthu wagwiro nthaŵi zina amapsa mtima. Kachisi wa ku Yerusalemu amayenera kukhala malikulu olambirira a anthu osankhidwa a Mulungu. Anayenera kukhala ‘nyumba yopemphereramo’ imene munthu aliyense akanaperekeramo nsembe ndi zopereka zake kwa Mulungu ndiponso kumene akanalandirirako malangizo ake ndi kukhululukidwa machimo awo. Pakachisipo, akanatha kuyanjana mophiphiritsa ndi Yehova. M’malo mwake, atsogoleri achipembedzo m’tsiku la Yesu anasandutsa kachisi “nyumba ya malonda” ndiponso “phanga la achifwamba.” (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:14-17) Iwo amapindula pogulitsa ziŵeto zoti achitire nsembe. Kunena zoona, amadyera nkhosa zawo masuku pamutu. Choncho, Mwana wa Mulungu anachita molungama pamene anathamangitsa anthu akuba ameneŵa kuŵatulutsa m’nyumba ya Atate wake. Nzomveka bwino kuti Yesu anapsa mtima!
Pamene Anthu Opanda Ungwiro Apsa Mtima
Nthaŵi zina nawonso anthu opanda ungwiro angapse mtima moyenera. Lingalirani zomwe zinachitika ndi Mose. Mtundu wa Israyeli unali utangopulumutsidwa kumene mozizwitsa ku Aigupto. Yehova anali atasonyeza mphamvu zake kuposa milungu yonyenga ya ku Aigupto mwa kukantha Aigupto ndi miliri khumi. Ndiye anagaŵanitsa madzi a m’Nyanja Yofiira kutsegula njira kuti Ayuda adutse. Pambuyo pake, anawatsogolera kupita ku phiri la Sinai, kumene anawalinganiza kukhala mtundu. Akumatumikira monga nkhoswe, Mose anapita m’phiri kukalandira malamulo a Mulungu. Kuphatikiza pa malamulo ena onse, Yehova anampatsa Moses Malamulo Khumi, olembedwa ndi “chala cha Mulungu” pa miyala imene Mulungu mwini anasema m’phiri. Komabe, pamene Mose anatsika, nchiyani chimene anapeza? Anthu anali atayamba kulambira fano la mwana wa ng’ombe wagolidi! Anaiŵala mwamsanga chotani! Panali patangopita masabata chabe. Moyenerera, “Mose anapsa mtima.” Anaswa miyalayo ndipo anatenga mwana wa ng’ombeyo namuwononga.—Eksodo 31:18; 32:16, 19, 20.
Nthaŵi ina pambuyo pake, Mose anapsa mtima pamene anthu anadandaula chifukwa cha kuchepa kwa madzi. Atapsa mtima, anaiŵala kaye khalidwe lake lodziŵika bwino lofatsa, kapena kudekha. Izi zinampangitsa kuchita cholakwa chachikulu. M’malo molemekeza Yehova monga Mpatsi wa Israyeli, Mose analankhula kwa anthuwo mwaukali ndipo anadzikweza iye mwini ndi mbale wake Aroni. Motero, Mulungu anachiona choyenera kupatsa Mose chilango. Iye sadzaloledwa kuloŵa m’dziko lolonjezedwa. Pambuyo pa zomwe zinachitika pa Meribazi, sikunenedwanso kuti Mose anapsa mtima. Mwachionekere, anatengapo phunziro.—Numeri 20:1-12; Deuteronomo 34:4; Salmo 106:32, 33.
Motero, pali kusiyana Mulungu ndi munthu. Yehova akhoza ‘kuchedwetsa mkwiyo wake’ ndipo amalongosoledwa bwino kukhala “wolekereza” chifukwa chikondi, osati mkwiyo, ndilo khalidwe lake lalikulu. Mkwiyo wake ndi wolungama nthaŵi zonse, wabwino nthaŵi zonse, wolamulirika nthaŵi zonse. (Eksodo 34:6; Yesaya 48:9; 1 Yohane 4:8) Munthu wangwiro Yesu Kristu nthaŵi zonse amatha kuwongolera mkwiyo wake; analongosoledwa kukhala “wofatsa.” (Mateyu 11:29) Komabe, anthu opanda ungwiro, ngakhale achikhulupiriro monga Mose, zimaŵavuta kuti alamulire mkwiyo wawo.
Ndiponso, anthu nthaŵi zambiri amalephera kuti aganizire bwino zomwe mkwiyo wawo wosalamulirika ungawabweretsere. Mukhoza kupeza mavuto chifukwa cha mkwiyo wanu wosalamulirika. Mwachitsanzo, kodi nchiyani chomwe mwachionekere chingachitike ngati mwamuna akwiyira mkazi kufika poti nkumenya khoma ndi nkhonya mpaka kuboola? Katundu amawonongeka. Akhoza kuvulala dzanja lake. Koma kuposa apo, kodi ukali wakewo udzakhudza motani chikondi ndi ulemu umene mkazi wake ali nawo kwa iye. Khoma likhoza kukonzedwa masiku oŵerengeka chabe ndipo dzanja lake lingakhale bwino pa masabata oŵerengeka; koma kodi kudzamutengera nthaŵi yaikulu chotani kuti mkazi wake ayambenso kumkhulupirira ndi kumpatsa ulemu?
Kunena zoona, Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za anthu omwe analephera kulamulira mkwiyo wawo ndipo anapeza nazo mavuto. Tiyeni tione zingapo chabe. Kaini anathamangitsidwa atapha mbale wake Abele. Simeoni ndi Levi anatembereredwa ndi atate wawo chifukwa chopha amuna a ku Sekemu. Yehova anakantha Uziya ndi khate pamene Uziyayo anapsera mtima ansembe omwe anafuna kumuwongolera. Pamene Yona “anapsa mtima,” Yehova anamdzudzula. Onseŵa anayenera kuyankha mlandu chifukwa cha mkwiyo wawo.—Genesis 4:5, 8-16; 34:25-30; 49:5-7; 2 Mbiri 26:19; Yona 4:1-11.
Akristu Ayenera kuyankha Mlandu
Mofananamo, Akristu lerolino ayenera kuyankha mlandu pazochita zawo kwa Mulungu, ndiponso pamlingo wina, kwa okhulupirira anzawo. Izi zimaoneka bwino m’Baibulo ndi mmene limagwiritsirira ntchito liwu lachigiriki lotanthauza mkwiyo. Liwu limodzi mwa mawu aŵiri ogwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri ndilo or·geʹ. Kaŵirikaŵiri limatembenuzidwa kukhala “mkwiyo” ndipo limasonya kuzindikira mwina ngakhale kuganizirapo kwambiri, kaŵirikaŵiri ncholinga chobwezera. Choncho, Paulo analimbikitsa Akristu a ku Roma: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; [or·geʹ] pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.” M’malo mosungira abale awo chakukhosi, iwo analimbikitsidwa kuti ‘ndi chabwino agonjetse choipa.’—Aroma 12:19, 21.
Liwu lina logwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri ndilo thy·mosʹ. Tsinde la liwulo “limatanthauza kuyenda kosalamulirika kwa mphepo, madzi, kaya nthaka, zinyama kapena anthu.” Choncho, liwuli limalongosoledwa mosiyanasiyana monga “kufufuma koopsa chifukwa cha chidani,” “kupsa mtima,” kapena “kuvunduka mtima,” kosokoneza mtendere wa maganizo, ndi kuyambitsa ndewu m’nyumba ndi kunja komwe.” Monga momwe phiri la volcano limaphulikira modzidzimutsa ndi kuponya phulusa lotentha, miyala, ndi matope otentha amoto, zimene zingavulaze, kupundula, ndi kupha, momwemonso mwamuna kapena mkazi amene sangalamulire mkwiyo wake. Mpangidwe wochulukitsa wa liwu la thy·mosʹ ndiwo umene wagwiritsiridwa ntchito pa Agalatiya 5:20, pamene Paulo akutchula “zopsa mtima” pamodzi ndi “ntchito [zina] zathupi” (vesi 19), monga dama, kukhumba zonyansa, ndi kuledzera. Ndithudi, khalidwe la John—lolongosoledwa poyamba paja—likusonyeza bwino “zopsa mtima.”
Motero, kodi mpingo wachikristu uyenera kuona motani anthu omwe amasonyeza khalidwe lotero akumachitira wina kapena katundu wa mwini mwachiwawa mobwerezabwereza? Mkwiyo wosalamulirika ngwoipa ndipo umayambitsa ndewu. Yesu anali ndi chifukwa chabwino chonenera kuti: “Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu.” (Mateyu 5:21, 22) Amuna akuchenjezedwa kuti: “Kondani akazi anu, ndipo musaŵaŵire mtima iwo.” Yemwe amapsa “mtima msanga” sayenera kukhala woyang’anira mumpingo. Motero, anthu omwe salamulira mkwiyo wawo sayenera kuonedwa monga zitsanzo mumpingo. (Akolose 3:19; Tito 1:7; 1 Timoteo 2:8) Ndipo pambuyo popenda mzimu wake wa munthuyo, khalidwe lake, ndiponso m’mene wavulazira ena, munthu wokwiya mosadziletsayo angachotsedwe mumpingo—zotsatirapo zoŵaŵa ndithu.
Kodi John, wotchulidwa poyamba uja, anayamba wayesapo kulamulira mkwiyo wake? Kodi amatha kupeŵa ngozi? Zachisoni kunena kuti kukuwa kunakula kufika pomakankha ndi kumduduluza mkazi wake. Pofuna kuloza kuti mnzakeyo ndiye walakwa amamudonyola ndi chala mpaka chalacho kuŵaŵa ndi kutupa. Mochenjera John amagwira Ginger m’malo oti akamvulaza musaonekere kwa anthu motero akumabisa khalidwe lake. Komabe, kenaka anayamba kumamponda, kummenya ndi zibakera, kumkoka tsitsi, ndi zoposerapo. Tsopano Ginger analekana naye John.
Izi sizikanachitika. Ena amene zimenezi zawachitikira atha kubweza mkwiyo wawo. Choncho, nkofunika kwambiri kuti titsanzire chitsanzo changwiro cha Yesu Kristu. Sanalakwepo nkamodzi komwe mwa kupsa mtima mosalamulirika. Mkwiyo wake unali wolungama nthaŵi zonse; sanafikepo pochita kulusa. Mwanzeru, Paulo analangiza tonsefe kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire,” (Aefeso 4:26) Mwa kuzindikira kuti tili ndi malire monga anthu ndi kuti tidzatuta chomwe tifesa, tili ndi zifukwa zabwino zoti tichepetsere mkwiyo wathu.
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 11]
Sauli Afuna Kupha Davide/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.