Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingapeŵe Bwanji Zoopsa pa Intaneti?
TADZIYEREKEZERANI kuti mwaloŵa m’nyumba yoŵerengeramo mabuku yaikulu kwambiri padziko lonse. Muli mabuku, nyuzipepala, makatiloji, zithunzi, ndiponso matepi a mtundu uliwonse. Zinthu zonsezi n’zokhudza nkhani iliyonse, ndiye zangoti mbwee kukuzungulirani. Nkhani zonse zatsopano ndiponso mabuku ambiri a m’zaka mazana a m’mbuyomu akupezeka m’menemo.
Inde, Intaneti ingakutheketseni kupeza nkhani zoterezi mosavuta. Ali khale pa kompyuta yake, munthu angathe kutumiza ndiponso kulandilira zinthu zosiyanasiyana zochokera pamakompyuta ndiponso kwa anthu ena owagwiritsa ntchito kuzungulira padziko lonse.a Imatheketsa oigwiritsa ntchito kugulitsa zinthu, kugula, kukambirana ndi mabanki, kucheza, kumvetsera nyimbo zimene zangotuluka kumene; ndipotu zonsezi n’kumazichita ali phee m’nyumba mwawo.
Choncho, n’zosadabwitsa, kuti akatswiri ena akunena kuti pakutha kwa chaka chino anthu opitirira mamaliyoni 320 adzakhala akugwiritsa ntchito intaneti. Motero kugwiritsa ntchito intaneti kwayamba kufala m’madera ambiri a padziko. Pakuti masukulu ngakhalenso nyumba zoŵerengeramo mabuku zikulimbikitsa kwambiri kuti aziigwiritsa ntchito, achinyamata mamiliyoni ambiri akutha kuigwiritsa ntchito. Ku United States, achinyamata pafupifupi 65 mwa achinyamata 100 alionse a zaka zapakati pa 12 ndi 19 aigwiritsako kale ntchito kapena alembetsa kuti azigwiritsa nawo ntchito zinthu zina zopezekapo.
Mwakugwiritsa ntchito bwino intaneti, mungapeze chidziŵitso chothandiza cha zanyengo, za maulendo, ndiponso nkhani zina. Mungaigwiritse ntchito pogula mabuku, zitsulo za galimoto, ndi zinthu zina. Anthu ambiri amaigwiritsira ntchito ya kusukulu.
Ngakhale kuti intaneti ingakhale yothandiza, ingakhalenso ngati nyumba yoŵerengeramo mabuku yopanda anthu oiyang’anira kapena anthu ena okuonani. Munthu angathe kuunguzamo podziŵa kuti palibe amene akumuona. Koma ichi ndicho chimodzi mwa zoopsa za pa intaneti. N’chifukwa chiyani chili choopsa? Chifukwa chakuti Malo Achidziŵitso ambiri amakhala ndi nkhani zonyansa ndiponso zowononga uzimu. Motero, intaneti ingathe kuika Akristu achinyamata pachiyeso. Ndiponsotu, mwachibadwa anthu amafuna kudziŵa zinthu zachilendo, ndipo Satana Mdyerekezi wakhala akuwapezerera chifukwa cha khalidwe limeneli. Ndithudi Satana anatengerapo mwayi podziŵa kuti Hava anali ndi chikhumbo chofuna kudziŵa zinthu zachilendo ndipo ‘anam’nyenga iye ndi kuchenjera kwake.’—2 Akorinto 11:3.
Mofananamo, Mkristu wachinyamata angathe kunyengedwa mosavuta ndi nkhani zonyansa ngati sali wotsimikiza kuteteza uzimu wake. Nkhani ya m’magazini otchedwa Better Homes and Gardens inalongosola kuti: “Intaneti ndi malo osangalatsa kwambiri amene akatswiri aluntha amatsatsapo malonda a nkhani zawo; koma nawonso achidyamakanda, akathyali, osamva za ena, ndiponso anthu ena oipa amaika nkhani zawo m’malo Achidziŵitso.”
Wachinyamata wina wotchedwa Javierb ananena kuti: “Malo Achidziŵitso ena ndi osokoneza maganizo. Angangotulukira mwadzidzidzi.” Iye anawonjeza kuti: “Potero amakhala akuyesa kukunyengerera. Amafuna akukole, kuti akudyere ndalama.” Mkristu wachinyamata wotchedwa John akuvomereza kuti: “Ukangoyamba kuona zinthu zosayenera, zimavuta kusiya, zimazoloŵereka kwambiri.” Achinyamata ena achikristu akhala akutsegula kaŵirikaŵiri Malo Achidziŵitso a zonyansa, ndipo potero aloŵa m’mavuto aakulu. Mpaka ena awononga unansi wawo ndi Yehova. Kodi zimenezi zingapeŵedwe bwanji?
“Kupenya Zachabe”
Nthaŵi zina adiresi ya Malo Achidziŵitso payokha imasonyezeratu kuti malowo ali ndi nkhani zosayenera.c Miyambo 22:3 amachenjeza kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; Koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”
Komabe, nthaŵi zambiri vuto limakhala lakuti anthu angathe kungotulukira pa malo osayenera, mwangozi. Patsamba lamalonje pangakhale zithunzi zotenga mtima zokonzedwa mosamala kwambiri pokunyengererani kuti mufune kudziŵa zili pamalowo, ndi kuti muzibwererapo nthaŵi ndi nthaŵi!d
Kevin akulongosola zimene zinachitikira m’nzake wina: “Analibe chochita ndipo anachita chidwi pofuna kudziŵa zina ndi zina. Posapita nthaŵi kuona zinthuzi zamaliseche kunasanduka chizoloŵezi chake.” Mwamwayi, Mkristu wachinyamata ameneyu anakaonana ndi mkulu ndipo anam’thandiza.
Kodi mwatsimikiza kale kuti ngati mutatulukira pamalo otere mudzachita zakutizakuti? Zimene Mkristu ayenera kuchita n’zodziŵikiratu: Ayenera kuchoka pamalopo nthaŵi yomweyo, kapena ngakhale kungozimitsiratu intanetiyo! Khalani ngati wamasalmo amene anati: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe” (Salmo 119:37; yerekezani ndi Yobu 31:1.) Kumbukirani kuti ngakhale patakhala kuti palibe munthu aliyense amene akutiona, sikuti sitionedwa. Baibulo limatikumbutsa kuti zinthu zonse “zikhala za pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.”—Ahebri 4:13.
Kulankhulana ndi makolo anu kapena ndi Akristu ena achikulire kungalimbikitse chitsimikizo chanu chakuti simudzatsekulanso malo okhala ndi zonyansa. Ndiponsotu, kodi mutatitimira mumchenga, mungalimbane nawo nokha mpaka utakulekezani m’khosi ndiye kenaka n’kumaitana okuthandizani?
Kodi Tinganenepo Chiyani pa za Mayanjano a pa Intaneti?
Njira ya macheza a pa intaneti imatheketsa oigwiritsa ntchito padziko lonse kulankhulana panthaŵi imodzi. Anthu abizinesi amaigwiritsa ntchito pamisonkhano yawo ya pa intaneti ndiponso pothandiza makasitomala. Zipinda zina zochezeramo zimatheketsa ozigwiritsa ntchito kugaŵana chidziŵitso chokhudza nkhani za maluso, monga kukonza galimoto kapena kukonza mapologalamu apakompyuta. Njira zina za macheza zimatheketsa abwenzi ndiponso achibale kuti athe kukambirana mwamtseri m’malo mowononga ndalama zambiri poimba telefoni yopita kutali. Ngakhale kuti pangakhale zifukwa zabwino zoigwiritsira ntchito njira imeneyi, koma kodi ili ndi zoopsa zilizonse?
Pali zifukwa zenizeni zofunika kukhalira osamala pogwiritsa ntchito zipinda zochezeramo aliyense, chifukwa zingathedi kubweretsa mavuto. Wolemba wotchedwa Leah Rozen inati: “Achinyamata odziŵa kugwiritsa ntchito zida za magetsi akuwononga nthaŵi yambiri pocheza ndi anthu osawadziŵa a m’dziko lawo lonse, ndipo ngakhale a padziko lonse lapansi. Tsoka lake n’lakuti, ena mwa anthu osawadziŵa amene achinyamata angamalankhule nawo pa intaneti amakhala anthu opulukira ofuna kupeza ana kuti apangane nawo malo oti akachitireko nawo chigololo.” Nkhani ya m’magazini yotchedwa Popular Mechanics inachenjeza kuti “muyenera kukhala wosamala kwambiri mukamagwiritsa ntchito zipinda zochezeramo aliyense. Kuuza dzina ndiponso adiresi yanu munthu amene simukumudziŵa kungakhale kuitana mavuto aakulu! Mudziikirenji m’mavuto otereŵa?
Komabe, choopsa china chovuta kuchiona ndicho kutanganidwa ndi mayanjano osayenera a anthu osawadziŵa amene salemekeza mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo.e Ofufuza akunena kuti nkhani zambiri za achinyamata m’zipinda zochezeramo zoterezi zimakhala zokhudza kugonana. Choncho, malangizo a m’Baibulo opezeka pa 1 Akorinto 15:33 ndi omveka: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Mayanjano oipa odzera pa kompyuta ali oopsa. Kodi wachinyamata woopa Mulungu ayenera kudziika dala pangozi zoterezi.?
Zodzitetezera
Pakuti intaneti ili ndi zoopsa zina, iyenera kugwiritsidwa ntchito mosamala. Mwachitsanzo, mabanja ena, amaika kompyuta pamene amadutsadutsapo, monga pabalaza. Ndiponso angaike lamulo lakuti ayenera kugwiritsa ntchito intaneti kokha ngati pakhomopo pali anthu ena. Ngati makolo anu akhazikitsa malamulo otere, amvereni. (Miyambo 1:8) Malangizo omveka bwino ali umboni woti amakukondani.
Ngati ntchito ya kusukulu ikufunika kuti mugwiritse ntchito intaneti, bwanji mutamayang’ana nthaŵi pamene muli pa intanetipo? Yesani kuganiziratu nthaŵi imene mukufuna kukhalapo, ndipo gwiritsani ntchito wotchi yolira kuti ikukumbutseni nthaŵiyo ikakwana. Tom ananena kuti: “Konzekereranitu, dziŵani bwinobwino zimene mukufuna kuona, ndipo chitani zomwezo, ngakhale zinthu zina zisangalatse motani.”
Tiyeneranso kusamala pogwiritsa ntchito njira yolemberana makalata yotchedwa E-mail. Achinyamata achikristu amakhala osamala kuti asazoloŵere kuŵerenga nkhani zambirimbiri za pa E-mail, makamaka ngati zambiri zili zosafunikira ndiponso zosatsimikizika. Kugwiritsa ntchito E-mail monyanyira kungaononge nthaŵi yamtengo wapatali yofunika pa maphunziro a kusukulu ndiponso zinthu zauzimu.
Mfumu Solomo anati: “Saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.” (Mlaliki 12:12) Mawu amenewo angagwirenso ntchito pa nkhani ya intaneti. Osatanganidwa kwambiri ndi kufunafuna kudziŵa zinthu ndiponso kuŵerengera zinazake mwakuti mpaka n’kuiwala kuphunzira Baibulo panokha ndiponso kuloŵa nawo muutumiki wachikristu. (Mateyu 24:14; Yohane 17:3; Aefeso 5:15, 16) Kumbukiraninso kuti ngakhale kuti pali nthaŵi imene kulankhulana kwa pakompyuta kungakhale koyenera, palibe chinthu china choloŵa m’malo mwa kukumana kwa pamaso m’pamaso ndi Akristu anzathu. Choncho ngati mukufunikiradi kugwiritsa ntchito intaneti, sankhani motsimikiza kuti mudzaigwiritsa ntchito mwanzeru. Peŵani Malo Achidziŵitso oopsa, ndipo musawononge nthaŵi yambiri muli pa intaneti. ‘Chinjirizani mtima wanu’ ndipo musakhale kapolo wa intaneti.—Miyambo 4:23.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani zakuti “The Internet—Is It for You?” (Kodi Inuyo Muyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti?) zimene zili mu magazini ya Galamukani! ya m’Chingerezi ya July 22, 1997.
b Mayina ena asinthidwa.
c Adiresi ya Malo Achidziŵitso ndi mpambo wa malemba umene umagwiritsidwa ntchito kuti munthu apeze Malo Achidziŵitsowo. Nthaŵi zina maadiresi amakhala ndi mawu osonyeza cholinga cha malowo.
d Tsamba lamalonje tingaliyerekezere ndi zenera lakumaso kwa sitolo. Limalongosola zimene zili pamalopo, amene anakonza malowo, ndi zina zotero.
e Zoopsa zoterezi zingakhalepo m’zipinda zochezeramo aliyense zokhazikitsidwa ndi Akristu okhala ndi zolinga zenizeni pofuna kukambirana nkhani zauzimu. Atambwali ndiponso ampatuko nthaŵi zina akhala akuloŵa nawo m’zokambirana zimenezi ndipo ayesa kukopa ena kuti avomereze maganizo awo osakhala a m’malemba.
[Mawu Otsindika patsamba 20]
“Malo Achidziŵitso ena ndi osokoneza maganizo. Angangotulukira mwadzidzidzi”
[Chithunzi patsamba 21]
Mabanja ena amaika kompyuta ya banja pamalo oonekera