Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingachite Chiyani Ndikalephera?
“Ndangolandira kumene zotsatira zanga za mayeso ndipo ndalephera maphunziro anayi omwe ndinalepheranso nthawi yapita. Ndinayesetsa, koma ndalepheranso kachiwiri.”—Anatero Lauren, wa zaka 15.
“Kuthana ndi kulephera n’kovuta kwambiri. N’zosavuta kuti munthu ayambe kuganiza molakwika.”—Anatero Jessica, wa zaka 19.
KULEPHERA. Mwina simukonda n’komwe kuganizira liwu limenelo. Koma nthawi ndi nthawi, tonsefe timalephera. Kaya n’kulephera kusukulu, kapena kuchita zinthu zochititsa manyazi pagulu, kukhumudwitsa munthu amene timamukonda, kapena kusonyeza khalidwe loipa, kulephera kungatipweteke kwambiri mumtima.
N’zoona kuti anthu onse amalakwitsa nthawi zina. Baibulo limati: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Komabe, ena a ife timavutika kuti tikhalenso bwinobwino pambuyo polephera. Mnyamata wina dzina lake Jason anafotokoza zimenezi motere: “Ineyo ndi amene ndimadzidzudzula kwambiri kuposa wina aliyense. Ndikalakwitsa chinachake, anthu akhoza kuseka, koma nthawi zambiri amaiwala pakapita nthawi. Ineyo sindiiwala, ndipo ndimangoganizirabe zimene ndinalakwitsazo.”
Kuganizira zolakwa zanu sikuti n’chinthu choipa, makamaka ngati kuchita zimenezo kungakuthandizeni kusintha. Komabe, kudziimba mlandu kwa nthawi yaitali ndiponso mosalekeza kungakupwetekeni. Lemba la Miyambo 12:25 limati: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu.”
Taganizirani za munthu winawake wotchulidwa m’Baibulo dzina lake Epafrodito. Anatumizidwa ku Roma kuti akatumikire Paulo pa zosowa zake. Koma Epafrodito anadwala ndipo sanathe kugwira ntchito yakeyo. M’malo mwake, Paulo ndi amene anamusamalira iyeyo! Paulo anakonza zoti Epafrodito abwerere kwawo, ndipo anauza mpingo wakwawo kuti mwamuna wokhulupirika ameneyu analinso kuvutika maganizo. Anavutika maganizo chifukwa chiyani? “Chifukwa mudamva kuti anadwala,” anafotokoza choncho Paulo. (Afilipi 2:25, 26) Epafrodito atamva kuti anthu adziwa zoti anadwala ndipo sanakwanitse ntchito imene anapatsidwa, mwina anamva ngati kuti anali munthu wolephera. N’zosadabwitsa kuti anavutika maganizo!
Kodi pali njira iliyonse yopewera kupwetekedwa mtima chifukwa cholephera?
Muzidziwa Zomwe Simungathe Kuchita
Njira imodzi yochepetsera kulephera ndiyo kudziikira zolinga zoti mukhoza kukwanitsa. Baibulo limati: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2; 16:18) Ndipo munthu wodzichepetsa amadziwa zinthu zomwe sangathe kuchita. N’zoona kuti nthawi zina ndi bwino kudziikira zolinga zovuta kuti mukulitse luso lanu ndi kuphunzira kuchita zinthu zina zatsopano. Koma musanyanyire. Mwina inuyo sindinu katswiri wa masamu kapena simungathe kulamulira thupi lanu bwinobwino ngati mmene angachitire katswiri wa zamasewera, ngakhale mutayesetsa chotani. Mnyamata wina dzina lake Michael anavomereza kuti: “Ndikudziwa kuti sindichita bwino kwambiri pa masewera. Choncho ndimasewerabe, koma sindiyesera dala kuchita zinthu zomwe ndikudziwa kuti sindingazithe.” Iye anafotokoza kuti: “Munthu ayenera kudziikira zolinga zomwe angathe kukwanitsa.”
Taonani mmene amaonera zinthu mtsikana wina wa zaka 14 dzina lake Yvonne, yemwe ali ndi msana wopunduka ndiponso amadwala matenda a ubongo oziziritsa ziwalo. Iye anati: “Sindingathe kuyenda, kuvina, kapena kuthamanga ngati mmene amachitira anthu ena. Sizindikhalira bwino kuona kuti sindingathe kuchita zinthu zimene ena amachita. Anthu ambiri samvetsa mmene ndimamvera. Koma ndimatha kupirira bwinobwino.” Kodi malangizo ake ndi otani kwa ena? “Osasiya ayi. Muzingoyeserabe. Mukalephera kapena mukapanda kuchita bwino, musamasiyire pomwepo. Muzingoyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe.”
Koma musadzivutitse maganizo podziyerekezera ndi anthu ena. Mnyamata wina wa zaka 15 dzina lake Andrew, anati: “Ndimayesetsa kupewa kudziyerekezera ndi anthu ena chifukwa tonsefe tili ndi luso ndi mphamvu zosiyanasiyana.” Mawu a Andrew akufanana ndi mawu a m’Baibulo opezeka pa Agalatiya 6:4, oti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”
Ngati Ena Akufuna Kuti Muchite Zoposa Zomwe Mungathe
Koma nthawi zina anthu ena, monga makolo, aphunzitsi, ndi ena, ndi amene amafuna kuti muchite zinthu zoposa zomwe mungathe. Ndipo mwina mukuona kuti ngakhale mutayesetsa bwanji, simungawasangalatse. Kuwonjezera apo, anthu amenewo mwina angamakuuzeni mmene akhumudwira nanu m’mawu opsetsa mtima kapena olefula kwambiri. (Yobu 19:2) Mosakayikira mukudziwa kuti makolo anu ndi anthu enawo sikuti akufuna dala kukupweteketsani mtima. Monga momwe Jessica ananenera, “nthawi zambiri sadziwa n’komwe mmene akukupwetekerani. Nthawi zina kumangokhala kusamvetsetsana basi.”
Komabe, kodi zingatheke kuti mwina akuona zimene inuyo simukuona? Mwachitsanzo, mwina n’kutheka kuti mukungodziderera ndipo mungathe kuchita zinthu zoposa zimene mukuganiza. M’malo mongowanyalanyaza akamakulimbikitsani, mungachite bwino ‘kumvera mwambo.’ (Miyambo 8:33) Michael anafotokoza kuti: “Zimenezi n’zothandiza inuyo. Iwo amafuna kuti muzichita zinthu bwino kuposa mmene mukuchitira panopa. Muziona zimenezo ngati mpata woti muthe kuchita zinthu zina zatsopano.”
Koma bwanji ngati mukuona kuti zimene makolo anu ndi anthu ena akufuna kuti muchite n’zoti simungazikwanitse, ndiponso kuti mulimonse mmene zingakhalire mulephera basi? Ngati ndi choncho zingakhale bwino kulankhula nawo, mwaulemu koma moona mtima, n’kuwauza mmene mukumvera. Mukatero mukhoza kukonzera limodzi zolinga zimene mungathedi kuzikwanitsa.
“Kulephera” pa Moyo Wanu Wauzimu
Achinyamata amene ali a Mboni za Yehova ali ndi ntchito yovuta yotumikira Mulungu. (2 Timoteo 4:5) Ngati ndinu Mkristu wachinyamata, nthawi zina mungamaone kuti mukulephera. Mwina mumaona kuti simuyankha bwino kwenikweni pa misonkhano. Kapena mwina mumavutika kufotokozera ena uthenga wa m’Baibulo. Mwachitsanzo, Jessica anaphunzira Baibulo ndi mtsikana winawake wa msinkhu wake. Kwa kanthawi, wophunzira wakeyo ankachita bwino kwambiri. Koma mwadzidzidzi mtsikanayo ananena kuti sakufunanso kutumikira Mulungu. Jessica anati: “Ndinaona ngati ndalephera kumuphunzitsa.”
Kodi Jessica anathana bwanji ndi maganizo amenewo? Choyamba, anazindikira kuti wophunzira wakeyo anakana Mulungu osati iyeyo. Chinanso chimene chinamuthandiza chinali kusinkhasinkha za chitsanzo cha m’Baibulo cha Petro, munthu woopa Mulungu amene anali ndi zolephera zingapo. Iye anafotokoza kuti: “Baibulo limasonyeza kuti Petro anathana ndi zolephera zakezo, ndipo Yehova anamugwiritsa ntchito m’njira zambiri kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu.” (Luka 22:31-34, 60-62) Komabe, ngati luso lanu monga mphunzitsi likufunika kulikulitsa, bwanji osayesetsa kusintha kuti muziphunzitsa bwino? (1 Timoteo 4:13) Pemphani thandizo kwa anthu okhwima maganizo mu mpingo amene angakuphunzitseni kuchita zimenezi.
Koma mwina chinthu chimene chimakuvutani kwambiri ndi ulaliki wa khomo ndi khomo. Jason anavomereza kuti: “Nthawi iliyonse imene mwininyumba wakana kulankhula nane ndimaona ngati ndalephera.” Kodi iye amatani kuti athane ndi maganizo amenewa? “Ndimafunika kukumbukira kuti sindinalephere ayi.” Inde, amakhala atachita ntchito imene Mulungu anamulamula kuchita, ntchito yolalikira. Ndipo ngakhale kuti zimapweteka munthu akakana kulankhula nanu, si anthu onse amene amakana uthenga wa m’Baibulo. Jason anati: “Ndikapeza munthu womvetsera, ndimadziwa kuti khama langa silinapite pachabe.”
Zolakwa Zazikulu
Bwanji ngati mwachita cholakwa chachikulu, kapena mwachita tchimo lalikulu kumene? Mtsikana wina dzina lake Ana, amene ali ndi zaka 19, anachita cholakwa choterocho.a Iye anavomereza kuti: “Ndinakhumudwitsa mpingo, anthu a m’banja mwanga, ndipo makamaka Yehova Mulungu.” Kuti zinthu ziyambenso kukuyenderani bwino, muyenera kulapa n’kupeza thandizo kwa amuna achikulire mwauzimu mumpingo. (Yakobo 5:14-16) Ana akukumbukira mawu olimbikitsa amene mkulu wina anamuuza: “Iye anati ngakhale kuti Mfumu Davide anachita zinthu zambiri zolakwa, Yehova anamukhululukirabe, ndipo zinthu zinayambanso kumuyendera bwino. Mawu amenewo anandithandiza.” (2 Samueli 12:9, 13; Salmo 32:5) Muyeneranso kuchita zonse zomwe mungathe kuti mudzilimbitse mwauzimu. Ana anati: “Ndinawerenga buku la Masalmo kambirimbiri, ndipo ndili ndi buku limene ndimalembamo malemba olimbikitsa.” Pakapita nthawi munthu akhoza kukhalanso bwinobwino ngakhale kuti anachita cholakwa chachikulu. Lemba la Miyambo 24:16 limati: “Wolungama amagwa kasanu ndi kaŵiri, nanyamukanso.”
Kukhalanso Bwinobwino Pambuyo Polephera
N’zoona kuti ngakhale zolakwa zazing’ono zingakupweteketseni mtima. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhalanso bwinobwino pambuyo pochita zolakwa zoterozo? Choyamba, muziona moyenera zolakwa zanuzo. Michael anati: “M’malo mongodziona ngati munthu wolephera basi, muyenera kupeza chinthu chenicheni chimene munalephera kuchita, ndi chifukwa chake munalephera. Mukatero ndiye kuti nthawi ina mungadzachite bwino.”
Chinanso, musamade nkhawa kwambiri mukalakwitsa. Pali “mphindi yakuseka,” ndipo nthawi zina zimenezi zingatanthauze kudziseka nokha! (Mlaliki 3:4) Ngati mwakhumudwa chifukwa cholephera, chitani chinachake chimene mumachichita bwino, monga zinthu zimene mumakonda kuchita mukakhala ndi mpata, kapena masewera enaake. ‘Kuchita ntchito zabwino zochuluka,’ monga kukambirana chikhulupiriro chanu ndi ena, kungakuthandizeni kusangalala ndi zochita zanu.—1 Timoteo 6:18.
Pomaliza, kumbukirani kuti “Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo . . . Sadzasunga mkwiyo wake kosatha.” (Salmo 103:8, 9) Jessica anati: “Ndikuona kuti ndikamayandikirana kwambiri ndi Yehova Mulungu, m’pamenenso ndimakhulupirira kwambiri kuti adzandithandiza pa chilichonse chimene chingandichitikire.” Inde, n’zolimbikitsa kudziwa kuti ngakhale kuti nthawi zina mumalephera, Atate wanu wakumwamba amakuonani kuti ndinu munthu wofunika.
[Mawu a M’munsi]
a Dzina lake lasinthidwa.
[Chithunzi patsamba 30]
Ngati mukuona kuti zinthu zimene ena akufuna kuti muchite simungazikwanitse, auzeni mwaulemu mmene mukumvera
[Chithunzi patsamba 31]
Kuchita zinthu zimene mumazichita bwino kungakuthandizeni kuthetsa maganizo oti ndinu munthu wolephera